Yoswa 10:1-43

10  Tsopano Adoni-zedeki, mfumu ya Yerusalemu anamva zakuti Yoswa walanda mzinda wa Ai+ ndi kuuwononga.+ Iye anamva kuti Yoswa wawononga mzindawo ndi kupha mfumu yake+ monga anachitira ndi mzinda wa Yeriko+ ndi mfumu yake.+ Anamvanso kuti anthu okhala ku Gibeoni apangana za mtendere ndi Aisiraeli+ ndipo akukhala pakati pawo. Atangomva zimenezi,  Adoni-zedeki anachita mantha kwambiri+ chifukwa Gibeoni unali mzinda waukulu ngati mzinda wolamulidwa ndi mfumu. Komanso mzindawo unali waukulu kuposa mzinda wa Ai,+ ndiponso amuna onse a kumeneko anali amphamvu.  Pamenepo Adoni-zedeki mfumu ya Yerusalemu+ anatumiza uthenga kwa Hohamu mfumu ya ku Heburoni,+ kwa Piramu mfumu ya ku Yarimuti,+ kwa Yafiya mfumu ya ku Lakisi+ ndi kwa Debiri mfumu ya ku Egiloni.+ Anatumiza uthenga wakuti:  “Bwerani kuno mudzandithandize. Tiyeni tikakanthe Agibeoni, chifukwa apangana za mtendere ndi Yoswa ndi ana a Isiraeli.”+  Choncho mafumu asanu a Aamoriwo+ anakumana pamodzi n’kunyamuka. Mafumuwo anali: Mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Heburoni, mfumu ya ku Yarimuti, mfumu ya ku Lakisi, ndi mfumu ya ku Egiloni. Mafumu amenewa, pamodzi ndi magulu awo ankhondo anakamanga msasa pafupi ndi mzinda wa Gibeoni, n’cholinga chouthira nkhondo.  Amuna a ku Gibeoni ataona zimenezi, anatumiza uthenga kwa Yoswa kumsasa ku Giligala,+ kuti: “Musatitaye ife akapolo anu!+ Bwerani kuno msanga, mudzatithandize ndi kutipulumutsa. Mafumu onse a Aamori okhala kudera lamapiri atisonkhanira kuti atithire nkhondo.”  Chotero Yoswa limodzi ndi amuna onse ankhondo, ndiponso amuna onse amphamvu ndi olimba mtima,+ ananyamuka kuchokera ku Giligala.+  Ndiyeno Yehova anauza Yoswa kuti: “Usawaope,+ chifukwa ndawapereka m’manja mwako.+ Palibe aliyense amene adzatha kulimbana nawe.”+  Yoswa anayenda usiku wonse kuchokera ku Giligala, ndipo anatulukira adaniwo modzidzimutsa. 10  Pamenepo Yehova anasokoneza adaniwo pamaso pa Aisiraeli.+ Ndiyeno Aisiraeli anayamba kupha adaniwo kwadzaoneni ku Gibeoni,+ ndi kuwathamangitsa kulowera kuchitunda cha Beti-horoni. Ndipo anapitiriza kuwapha mpaka kukafika ku Azeka+ ndi ku Makeda.+ 11  Atafika pamalo otsetsereka otchedwa Beti-horoni pothawa Aisiraeli, Yehova anawagwetsera miyala ikuluikulu ya matalala+ kuchokera kumwamba yomwe inawagwera ndi kuwapha mpaka kukafika ku Azeka. Amene anaphedwa ndi matalalawo anali ambiri kuposa amene ana a Isiraeli anapha ndi lupanga. 12  Pa tsiku limene Yehova anapereka Aamori kwa ana a Isiraeli, Yoswa analankhula ndi Yehova pamaso pa Aisiraeli kuti:“Dzuwa iwe,+ ima pamwamba pa Gibeoni,+Ndipo iwe mwezi, ima pamwamba pa chigwa cha Aijaloni.”+ 13  Choncho dzuwa linaimadi, ndiponso mwezi unaima mpaka mtunduwo utalanga adani ake.+ Kodi sizinalembedwe m’buku la Yasari?+ Dzuwa linaima kumwamba pakatikati, silinafulumire kulowa pafupifupi kwa tsiku lonse lathunthu.+ 14  Palibe tsiku lina lofanana ndi limenelo, kaya pambuyo pake kapena patsogolo pake, loti Yehova anamvera mawu a munthu mwa njira imeneyi,+ popeza Yehova mwiniyo anali kumenyera nkhondo Isiraeli.+ 15  Zitatero, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anabwerera kumsasa ku Giligala.+ 16  Koma mafumu asanu aja anathawa+ n’kukabisala kuphanga la ku Makeda.+ 17  Ndiyeno Yoswa analandira uthenga wakuti: “Mafumu asanu aja apezeka atabisala kuphanga la ku Makeda.”+ 18  Yoswa atamva anati: “Gubuduzirani miyala ikuluikulu pakamwa pa phangalo ndipo musankhe amuna oti azilonderapo. 19  Koma amuna enanu, musangoima chilili. Thamangitsani adani anu ndipo muzipha amene muziwapeza.+ Musawalole kuti akalowe m’mizinda yawo, pakuti Yehova Mulungu wanu wawapereka m’manja mwanu.”+ 20  Yoswa ndi ana a Isiraeli atangomaliza kupulula adani awo onse,+ ndipo opulumuka atathawa n’kukalowa m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri,+ 21  Aisiraeli onse anayamba kubwerera mwamtendere kwa Yoswa kumsasa, ku Makeda. Ndipo palibe munthu amene ananena zamtopola kwa ana a Isiraeli.+ 22  Ndiyeno Yoswa anati: “Tsegulani phangali munditulutsire mafumu asanu amene ali mmenemowo.” 23  Iwo anatseguladi phangalo n’kumutulutsira mafumu asanuwo: Mfumu ya ku Yerusalemu,+ mfumu ya ku Heburoni,+ mfumu ya ku Yarimuti,+ mfumu ya ku Lakisi ndi mfumu ya ku Egiloni.+ 24  Atangowatulutsa mafumuwo anapita nawo kwa Yoswa. Iye anaitana amuna onse a Isiraeli amene anapita naye kunkhondoko, n’kuuza atsogoleri awo kuti: “Bwerani kuno muponde kumbuyo kwa makosi a mafumuwa.”+ Iwo anabwera n’kupondadi kumbuyo kwa makosi awo.+ 25  Ndiyeno Yoswa anawauza kuti: “Musaope kapena kuchita mantha.+ Khalani olimba mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu, chifukwa umu ndi mmene Yehova azichitira ndi adani anu onse amene mukumenyana nawo.”+ 26  Kenako Yoswa anawakantha ndi kuwapha. Atatero anawapachika pamitengo isanu, pomwe anakhalapo mpaka madzulo.+ 27  Dzuwa likulowa, Yoswa analamula kuti atsitse mafumuwo pamitengoyo+ n’kuwaponyera m’phanga limene anabisalamo lija, ndipo anthuwo anachitadi zimenezi. Kenako anaika miyala ikuluikulu pakhomo la phangalo, yomwe ilipobe mpaka lero. 28  Yoswa analanda mzinda wa Makeda+ tsiku limenelo ndipo anapha anthu a mumzindawo ndi lupanga. Mfumu ya mzindawo ndi anthu ake onse anawapha,+ ndipo Yoswa anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Mfumu ya ku Makeda+ anaichita zofanana ndi zomwe anachita mfumu ya ku Yeriko. 29  Zitatero, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anachoka ku Makeda n’kupita ku Libina+ komwe anakachitako nkhondo. 30  Yehova anaperekanso mzindawo ndi mfumu yake m’manja mwa Isiraeli. Choncho Aisiraeli anapha anthu onse a mumzindawo ndi lupanga, ndipo anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Mfumu ya ku Libina anaichita zofanana ndi zomwe anachita mfumu ya ku Yeriko.+ 31  Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse omwe anali naye anachoka ku Libina n’kupita ku Lakisi.+ Kumeneko anamanga msasa pafupi ndi mzindawo n’kuuthira nkhondo. 32  Yehova anapereka Lakisi m’manja mwa Isiraeli, moti analanda mzindawo pa tsiku lachiwiri. Anapha ndi lupanga munthu aliyense amene anali mumzindawo,+ mofanana ndi zonse zimene anachita ku Libina. 33  Apa m’pamene Horamu mfumu ya ku Gezeri+ anapita kukathandiza mzinda wa Lakisi. Koma Yoswa anapha Horamu ndi anthu ake onse, moti sipanatsale wopulumuka.+ 34  Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anachoka ku Lakisi n’kupita ku Egiloni.+ Kumeneko anakamanga msasa pafupi ndi mzindawo n’kuuthira nkhondo. 35  Analanda mzindawo pa tsikulo n’kuyamba kupha ndi lupanga aliyense amene anali mumzindawo. Anachitira mzindawo zonse zimene anachitira mzinda wa Lakisi.+ 36  Atachoka ku Egiloni, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anapita kumzinda wa Heburoni+ n’kuyamba kuuthira nkhondo. 37  Analanda mzindawo ndipo anapha ndi lupanga anthu amene anali mmenemo ndi m’midzi yake yonse, komanso anapha mfumu yawo. Yoswa anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Anachitira mzindawo zonse zimene anachitira mzinda wa Egiloni. Chotero Yoswa anawononga mzindawo ndi aliyense amene anali mmenemo.+ 38  Pomaliza, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye, anatembenuka n’kupita kumzinda wa Debiri,+ n’kuyamba kuuthira nkhondo. 39  Analanda mzindawo ndi midzi yake yonse n’kugwiranso mfumu yake. Ndiyeno anapha ndi lupanga munthu aliyense amene anali mmenemo,+ ndipo Yoswa anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka.+ Anachitira mzinda wa Debiri ndi mfumu yake zonse zimene anachitira mzinda wa Heburoni, komanso zimene anachitira mzinda wa Libina ndi mfumu yake.+ 40  Choncho Yoswa anapha anthu a m’dera lonse la mapiri,+ anthu a ku Negebu,+ a ku Sefela,+ ndi a m’madera otsetsereka+ pamodzi ndi mafumu awo onse. Iye anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka,+ ndipo anapha chamoyo chilichonse*+ monga mmene Yehova Mulungu wa Isiraeli analamulira.+ 41  Yoswa anawapha kuchokera ku Kadesi-barinea+ mpaka ku Gaza+ ndi dera lonse la Goseni+ mpaka ku Gibeoni.+ 42  Yoswa anagwira mafumu onsewa n’kulanda malo awo pa nthawi imodzi,+ chifukwa Yehova Mulungu wa Isiraeli ndiye anali kuwamenyera nkhondo.+ 43  Atatero, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anabwerera kumsasa ku Giligala.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mpweya uliwonse.”