Yoswa 1:1-18

1  Mose mtumiki wa Yehova atamwalira, Yehova analankhula ndi Yoswa+ mwana wa Nuni, mtumiki+ wa Mose, kuti:  “Mose mtumiki wanga wamwalira.+ Tsopano konzeka limodzi ndi anthu onsewa, kuti muwoloke Yorodanoyu ndi kulowa m’dziko limene ndikulipereka kwa ana a Isiraeli.+  Malo alionse amene phazi lanu lidzapondapo ndidzawapereka ndithu kwa inu, monga mmene ndinalonjezera kwa Mose.+  Dziko lanu lidzayambira kuchipululu ndi ku Lebanoni uyu mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate, dziko lonse la Ahiti+ mpaka kukafika ku Nyanja Yaikulu, kolowera dzuwa.+  Palibe amene adzatha kulimbana nawe masiku onse a moyo wako.+ Ndidzakhala nawe+ monga mmene ndinakhalira ndi Mose, sindidzakutaya kapena kukusiya ngakhale pang’ono.+  Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ pakuti ndiwe amene utsogolere anthuwa kuti akalandire dziko+ limene ndinalumbirira makolo awo kuti ndidzawapatsa.+  “Iwe khala wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Uonetsetse kuti ukutsatira malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakulamula.+ Malamulowo usawasiye ndi kupatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere,+ kuti uchite mwanzeru kulikonse kumene udzapitako.+  Buku la malamulo ili lisachoke pakamwa pako,+ uziliwerenga ndi kusinkhasinkha usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatira zonse zolembedwamo.+ Pakuti ukatero, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzachita zinthu mwanzeru.+  Monga ndakulamula kale,+ ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa,+ pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.”+ 10  Tsopano Yoswa analamula akapitawo a anthuwo kuti: 11  “Pitani mumsasa wonsewu, mukauze anthu kuti, ‘Konzekani ndi kutenga zonse zofunikira, chifukwa pakapita masiku atatu kuchokera lero, mudzawoloka Yorodano uyu, ndi kulowa m’dzikolo kuti mukalilande, dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale lanu.’”+ 12  Kenako, Yoswa analankhula ku fuko la Rubeni, ku fuko la Gadi, ndi ku hafu ya fuko la Manase, kuti: 13  “Mukumbukire mawu amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani,+ akuti, ‘Yehova Mulungu wanu akukupatsani mpumulo, ndipo wakupatsani dziko ili. 14  Akazi anu ndi ana anu aang’ono atsale limodzi ndi ziweto zanu m’dziko lino limene Mose anakupatsani, tsidya lino la Yorodano.+ Koma amunanu, mudzawoloka patsogolo pa abale anu, mutafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+ Inuyo, amuna nonse amphamvu ndi olimba mtima,+ muwoloke kuti mukawathandize abale anu. 15  Ndipo Yehova akadzapereka mpumulo kwa abale anu, monga waperekera kwa inu, nawonso abale anu akakalanda dziko limene Yehova Mulungu akuwapatsa,+ m’pamene inuyo mudzabwerere. Mudzabwerera kudziko la cholowa chanu limene Mose mtumiki wa Yehova wakugawirani,+ tsidya lino la Yorodano, kum’mawa kuno.’”+ 16  Amunawo anayankha Yoswa kuti: “Zonse zimene mwatilamula tichita, ndipo kulikonse kumene mungatitumize tipita.+ 17  Monga tinamvera Mose m’chilichonse, tidzakhalanso omvera kwa inu. Yehova Mulungu wanu akhale nanu+ mmene anakhalira ndi Mose.+ 18  Munthu aliyense wopandukira malamulo anu,+ ndi wosamvera mawu anu pa chilichonse chimene mungamulamule, ameneyo aphedwe.+ Inuyo mukhale wolimba mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu.”+

Mawu a M'munsi