Yona 4:1-11

4  Koma zimenezi sizinamusangalatse m’pang’ono pomwe Yona + ndipo anakwiya nazo koopsa.  Choncho iye anapemphera kwa Yehova kuti: “Inu Yehova, kodi zimene ndimaopa ndili kwathu zija si zimenezi? N’chifukwa chaketu ine ndinathawa kupita ku Tarisi.+ Ndinadziwa kuti inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wachifundo,+ wosakwiya msanga, wodzaza ndi kukoma mtima kosatha+ komanso mumatha kusintha maganizo pa tsoka limene mumafuna kubweretsa.+  Tsopano inu Yehova, chotsani moyo wanga,+ pakuti kuli bwino kuti ndife kusiyana n’kukhala ndi moyo.”+  Poyankha, Yehova anati: “Kodi pali chifukwa chilichonse choti ukwiyire?”+  Kenako, Yona anatuluka mumzindawo ndi kukakhala pansi kumbali ya kum’mawa kwa mzindawo. Kumeneko anamanga chisimba* kuti akhale pamthunzi+ kufikira ataona zimene zichitikire mzindawo.+  Ndiyeno Yehova Mulungu anameretsa chomera cha mtundu wa mphonda kuti chiyange pamene Yona anakhala ndi kum’chitira mthunzi. Anachita zimenezi kuti amupulumutse ku masautso ake.+ Yona anasangalala kwambiri chifukwa cha chomeracho.  Kenako Mulungu woona anatumiza mbozi+ m’bandakucha wa tsiku lotsatira, kuti ikawononge chomera cha mtundu wa mphonda chija, moti chomeracho chinafota.+  Dzuwa litatuluka, Mulungu anatumiza mphepo yotentha yochokera kum’mawa.+ Dzuwalo linamutentha Yona pamutu moti anangotsala pang’ono kukomoka.+ Choncho Yona anapempha mobwerezabwereza kuti angofa. Iye anali kunena kuti: “Kuli bwino ndife kusiyana n’kuti ndikhale ndi moyo.”+  Pamenepo Mulungu anafunsa Yona kuti: “Kodi pali chifukwa chilichonse chokwiyira ndi chomera cha mtundu wa mphondachi?”+ Yona anayankha kuti: “Ndikuyeneradi kukwiya moti ndikufuna kufa chifukwa cha mkwiyowo.” 10  Koma Yehova anati: “Iwe ukumvera chisoni chomera cha mtundu wa mphondachi, chimene sunachivutikire kapena kuchikulitsa, chimene changomera usiku umodzi wokha n’kufa usiku umodzi. 11  Kodi ine sindikuyenera kumvera chisoni mzinda waukulu wa Nineve,+ mmene muli anthu oposa 120,000, omwe sadziwa kusiyanitsa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere? Kodi sindiyenera kumveranso chisoni ziweto zambiri zimene zili mmenemo?”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”