Yona 2:1-10

2  Tsopano Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake, ali m’mimba mwa chinsombacho,+  kuti:“Pamene ndinali m’masautso ndinaitana Yehova,+ ndipo anandiyankha.+Ndinafuula kupempha thandizo ndili m’Manda* akuya.+Ndipo inu munamva mawu anga.+   Pamene munandiponya m’malo ozama, pansi penipeni pa nyanja yakuya,+Madzi amphamvu anandimiza.Mafunde anu amphamvu anadutsa pamwamba panga.+   Ndipo ine ndinati, ‘Mwandipitikitsa pamaso panu!+Kodi kachisi wanu woyera ndidzamuonanso?’+   Ndinatsala pang’ono kufa+ chifukwa madzi anandimiza.Zomera zam’nyanja zinakulunga mutu wanga.   Ndinatsikira m’tsinde mwenimweni mwa mapiri.Zotsekera za dziko lapansi zinanditsekereza kuti ndikhale komweko mpaka kalekale.*Koma inu Yehova Mulungu wanga, munanditulutsa m’dzenje ndili wamoyo.+   Pamene ndinalefuka kwambiri,+ ndinakumbukira Yehova.+Ndipo pemphero langa linafika kwa inu, m’kachisi wanu woyera.+   Anthu okhulupirira mafano, amaleka kusonyeza kukoma mtima kwawo kosatha.+   Koma ine, ndidzakutamandani ndi kupereka nsembe kwa inu.+Zimene ndalonjeza ndidzazikwaniritsa.+ Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”+ 10  Kenako Yehova analamula chinsombacho, ndipo chinalavula Yona kumtunda.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 5.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.