Yona 1:1-17

1  Yehova anayamba kulankhula ndi Yona+ mwana wa Amitai, kuti:  “Nyamuka upite kumzinda waukulu wa Nineve.+ Kumeneko ukadzudzule anthu a mumzindawo ndi kuwauza kuti ine ndaona zoipa zimene akuchita.”+  Pamenepo Yona ananyamuka n’kulowera ku Tarisi,+ kuthawa Yehova.+ Kenako anafika ku Yopa+ ndipo kumeneko anapeza chombo chopita ku Tarisi. Iye analipira malipiro a ulendowo n’kukwera chombocho kuti apite ku Tarisi limodzi ndi anthu amene anali m’chombomo, kuthawa Yehova.  Ndiyeno Yehova anabweretsa chimphepo champhamvu panyanjapo,+ ndipo panachita mkuntho wamphamvu.+ Chotero chombocho chinatsala pang’ono kusweka.  Zitatero oyendetsa chombo anayamba kuchita mantha ndipo aliyense anayamba kufuulira mulungu wake+ kuti amuthandize. Iwo anayamba kuponya m’nyanja katundu amene anali m’chombomo kuti chipepukidwe.+ Apa n’kuti Yona atatsikira mkatikati mwa chombocho, pakuti chinali ndi zipinda zapansi. Kumeneko Yona anagona tulo tofa nato.+  Kenako woyendetsa chombocho anafika pamene Yona anagonapo n’kumufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukungogona? Dzuka ufuulire mulungu wako!+ Mwina Mulungu woona atikomera mtima ndipo sitifa.”+  Ndiyeno anayamba kuuzana kuti: “Tiyeni tichite maere+ kuti tidziwe amene wachititsa kuti tsoka limeneli litigwere.”+ Iwo anachitadi maere ndipo maerewo anagwera Yona.+  Choncho anamufunsa kuti: “Tiuze, ndani wachititsa kuti tsoka limeneli litigwere?+ Umagwira ntchito yanji ndipo ukuchokera kuti? Kwanu n’kuti ndipo ndiwe wa mtundu uti?”  Iye anayankha kuti: “Ndine Mheberi,+ ndipo ndimaopa+ Yehova Mulungu wakumwamba,+ amene anapanga nyanja ndi mtunda.”+ 10  Pamenepo anthuwo anachita mantha kwambiri, ndipo anamufunsa kuti: “Wachitiranji zimenezi?”+ Anthuwo anamufunsa choncho chifukwa anadziwa kuti Yona akuthawa Yehova, pakuti iye anali atawauza zimenezo. 11  Kenako anamufunsa kuti: “Ndiye tichite nawe chiyani+ kuti nyanjayi ikhale bata?” Apa n’kuti mkuntho wamphamvu uja ukukulirakulira. 12  Iye anawayankha kuti: “Mundinyamule n’kundiponya m’nyanjamu ndipo nyanjayi ikhala bata. Chifukwa ndikudziwa kuti mkunthowu ukuchitika chifukwa cha ine.”+ 13  Koma anthuwo anayesetsa kuti adutse mafunde amphamvuwo ndi kukakocheza kumtunda. Koma sanakwanitse chifukwa mkunthowo unali kuwonjezeka kwambiri.+ 14  Pamenepo anthuwo anafuulira Yehova ndi kunena kuti:+ “Chonde inu Yehova, musalole kuti tiwonongeke chifukwa cha munthu uyu! Musaike pa ife mlandu wa magazi a munthu wosalakwa,+ chifukwa zonsezi zachitika pokwaniritsa chifuniro chanu, inu Yehova!”+ 15  Kenako ananyamula Yona ndi kum’ponya m’nyanja. Atatero nyanjayo inakhala bata.+ 16  Zimenezi zitachitika anthuwo anayamba kuopa Yehova kwambiri.+ Choncho anapereka nsembe kwa Yehova+ ndi kuchita malonjezo.+ 17  Tsopano Yehova anatumiza chinsomba chachikulu kuti chikameze Yona,+ moti Yona anakhala m’mimba mwa nsomba masiku atatu, usana ndi usiku.+

Mawu a M'munsi