Yohane 9:1-41

9  Tsopano pamene anali kuyenda anaona munthu amene anabadwa wakhungu.  Ophunzira ake anamufunsa kuti: “Rabi,+ anachimwa ndani+ kuti munthu uyu abadwe wakhungu chonchi? Ndi iyeyu kapena makolo ake?”+  Yesu anayankha kuti: “Munthuyu kapena makolo ake, onsewa palibe amene anachimwa. Izi zinachitika kuti ntchito za Mulungu zionekere kudzera mwa iye.+  Tiyenera kugwira ntchito za iye amene anandituma ine kudakali masana.+ Usiku+ ukubwera pamene munthu sangathe kugwira ntchito.  Pamene ine ndili m’dziko, ndine kuwala kwa dzikoli.”+  Atanena zimenezi, analavulira malovu pansi ndi kukanda thope ndi malovuwo. Atatero anapaka thopelo m’maso mwa munthuyo.+  Kenako anamuuza kuti: “Pita ukasambe+ m’dziwe la Siloamu”+ (dzina limene kumasulira kwake ndi ‘Otumidwa’). Choncho anapita kukasamba,+ ndipo anabwerako akuona.+  Tsopano anthu okhala naye pafupi ndi anthu ena amene m’mbuyomo anali kumuona akupemphapempha anayamba kunena kuti: “Si uyu kodi amene anali kukhala pansi n’kumapemphapempha uja?”+  Ena anati: “Ndi yemweyu.” Enanso anati: “Iyayi, wangofanana naye.” Mwiniwakeyo anati: “Ndine amene.” 10  Pamenepo anayamba kumufunsa kuti: “Nanga maso akowa atseguka bwanji?”+ 11  Iye anayankha kuti: “Munthu wina dzina lake Yesu anakanda thope ndi kupaka m’maso mwangamu, ndiyeno anandiuza kuti, ‘Pita ku Siloamu+ ukasambe.’ Ndinapitadi kukasamba ndipo ndayamba kuona.” 12  Pamenepo anthuwo anamufunsa kuti: “Ali kuti munthu ameneyo?” Iye anati: “Sindikudziwa.” 13  Iwo anatenga munthu amene anali wakhunguyo ndi kupita naye kwa Afarisi. 14  Tsiku limene Yesu anakanda matope ndi kutsegula maso a munthuyo,+ linali la Sabata.+ 15  Pamenepo Afarisi nawonso anayamba kufunsa munthu uja mmene anayambira kuona.+ Iye anawafotokozera kuti: “Iye anapaka thope m’maso mwanga, ndiyeno ndinapita kukasamba, basi kenako ndayamba kuona.” 16  Ena mwa Afarisiwo anayamba kunena kuti: “Munthu ameneyu si wochokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata.”+ Ena anayamba kunena kuti: “Koma munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro+ zoterezi?” Choncho panakhala kugawanika+ pakati pawo. 17  Ndiyeno Afarisiwo anafunsanso munthu amene anali wakhungu uja kuti: “Nanga iwe ukuti bwanji za munthu ameneyu, popeza kuti wakutsegula maso?” Munthuyo anati: “Ndi mneneri.”+ 18  Komabe atsogoleri achipembedzo achiyudawo sanakhulupirire zakuti munthuyu analidi wakhungu ndipo wayamba kuona, mpaka anaitanitsa makolo ake. 19  Makolowo anawafunsa kuti: “Kodi uyu ndi mwana wanu amene mukuti anabadwa wakhungu? Nanga zatheka bwanji kuti tsopano aziona?” 20  Pamenepo makolo akewo anayankha kuti: “Tikudziwa kuti uyu ndi mwana wathu ndi kuti anabadwa wakhungu. 21  Koma za mmene wayambira kuona tsopano, ndi amene wamutsegula maso, zimenezo sitikudziwapo kanthu ayi. Mufunseni mwiniwakeyu. Ndi wamkulu, afotokoze yekha.” 22  Makolo akewo ananena zimenezi chifukwa anali kuopa+ atsogoleri achipembedzo achiyuda. Pakuti iwo anali atagwirizana kale kuti, ngati wina angavomereze kuti Yesu alidi Khristu, adzamuchotsa musunagoge.+ 23  N’chifukwa chake makolo akewo ananena kuti: “Ndi wamkulu. Mufunseni mwiniwakeyu.” 24  Choncho iwo anaitananso munthu anali wakhungu uja kachiwiri ndi kumuuza kuti: “Lemekeza Mulungu,+ ife tikudziwa kuti munthu ameneyu ndi wochimwa.” 25  Iye anayankha kuti: “Zakuti iye ndi wochimwa, ine sindikudziwa. Chimodzi chokha chimene ine ndikudziwa n’chakuti, poyamba ndinali wakhungu, koma tsopano ndikuona.” 26  Pamenepo iwo anati: “Anakuchita chiyani? Watsegula bwanji maso ako?” 27  Iye anawayankha kuti: “Ndakuuzani kale, koma inu simunamvetsere. Nanga n’chifukwa chiyani mukufuna kumvanso? Kapena inunso mukufuna kukhala ophunzira ake?” 28  Atanena zimenezi, iwo anamulalatira kuti: “Iweyo ndiye wophunzira wa munthu amene uja, ifetu ndife ophunzira a Mose. 29  Tikudziwa kuti Mulungu analankhula ndi Mose,+ koma za munthu uyu, sitikudziwa kuti iye akuchokera kuti.”+ 30  Poyankha munthuyo anati: “Izi n’zodabwitsa ndithu,+ simukudziwa kumene wachokera, chikhalirecho wanditsegula maso. 31  Tikudziwa kuti Mulungu samvetsera ochimwa,+ koma ngati munthu ali woopa Mulungu ndipo amachita chifuniro chake, ameneyo amamumvetsera.+ 32  Sizinamveke n’kale lonse kuti wina watsegula maso a munthu amene anabadwa wakhungu. 33  Munthu uyu akanapanda kuchokera kwa Mulungu,+ sakanatha kuchita kanthu.” 34  Poyankha iwo anati: “Wobadwira mu uchimo wokhawokha iwe,+ ukufuna kuphunzitsa ife kodi?” Pamenepo anamuchotsa musunagoge!+ 35  Yesu anamva kuti munthu uja amuchotsa musunagoge. Ndipo atakumana naye anamufunsa kuti: “Kodi ukukhulupirira mwa Mwana+ wa munthu?” 36  Munthuyo anayankha kuti: “Kodi mwana wa munthuyo ndani ndimudziwe bambo, kuti ndikhulupirire mwa iye?” 37  Yesu anamuuza kuti: “Wamuona kale, ndi amene akulankhula nawe panopa.”+ 38  Pamenepo iye ananena kuti: “Ndakhulupirira mwa iye Ambuye.” Ndipo anamugwadira.+ 39  Ndiyeno Yesu ananena kuti: “Ndinabwera m’dziko lino kudzapereka chiweruzo ichi:+ Osaona ayambe kuona,+ ndipo oona akhale akhungu.”+ 40  Afarisi amene anali naye anamva zimenezi, ndipo anafunsa Yesu kuti: “Kodi ifenso tingakhale akhungu?”+ 41  Yesu anati: “Mukanakhala akhungu, simukanakhala ndi tchimo. Koma popeza mukunena kuti, ‘Tikuona.’+ Tchimo+ lanu likhalabe chikhalire.”

Mawu a M'munsi