Yohane 7:53–8:59

* Mipukutu ya Codex Sinaiticus, Codex Vaticanus ndi Sinaitic Syriac, inachotsa vesi 53 mpaka chaputala 8, vesi 11. (M’mabuku ambiri Achigiriki mawu a mavesi amenewa amasiyanasiyana.) Ndimezi zili ndi mawu akuti: 53  Zitatero aliyense ananyamuka n’kupita kwawo. 8  Kenako Yesu anapita kuphiri la Maolivi.  M’mawa kwambiri, anafikanso kukachisi ndipo anthu onse anayamba kubwera kwa iye. Choncho iye anakhala pansi ndi kuyamba kuwaphunzitsa.  Tsopano alembi ndi Afarisi anabweretsa mkazi amene anagwidwa akuchita chigololo. Ndipo atamuimika pakati pawo,  anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa akuchita chigololo.  M’Chilamulo, Mose analamula kuti akazi oterewa tiziwaponya miyala. Nanga inu mukutipo bwanji?”  Iwo kwenikweni anali kunena zimenezi pofuna kungomuyesa, kuti amupeze chifukwa chomuimbira mlandu. Koma Yesu anawerama ndi kuyamba kulemba pansi ndi chala chake.  Atalimbikira kumufunsa, iye anaweramuka ndi kuwauza kuti: “Munthu amene ali wopanda tchimo pakati panu, ayambe iyeyo kumuponya mwala mkaziyu.”  Kenako anaweramanso ndi kupitiriza kulemba pansi.  Koma iwo atamva zimenezi, anayamba kuchoka mmodzimmodzi. Oyamba kuchoka anali akulu, mpaka Yesu anamusiya yekha ndi mkazi amene anali pakati pawo uja. 10  Tsopano Yesu ataweramuka, anafunsa mkaziyo kuti: “Mayi iwe, anthu aja ali kuti? Kodi palibe amene waona kuti ndiwe woyenera kulangidwa?” 11  Mkaziyo anati: “Palibe bambo.” Ndiyeno Yesu anati: “Inenso sindikuona kuti ndiwe woyenera kulangidwa. Pita, kuyambira lero usakachitenso tchimo.” 12  Pamenepo Yesu analankhula nawonso kuti: “Ine ndine kuwala+ kwa dziko. Wonditsatira ine sadzayenda mumdima,+ koma adzakhala nako kuwala kwa moyo.” 13  Chotero Afarisi anauza Yesu kuti: “Iwe umadzichitira wekha umboni koma umboni wakowo si woona ayi.” 14  Poyankha Yesu anati: “Ngakhale kuti ndimadzichitira ndekha umboni,+ umboni wanga ndi woona, chifukwa ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita.+ Koma inu simukudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. 15  Inu mumaweruza mwa kungoona maonekedwe a munthu.+ Inetu sindiweruza munthu aliyense.+ 16  Koma ndikati ndiweruze, chiweruzo changa chimakhala cholungama, chifukwa sindiweruza ndekha, pakuti Atate amene anandituma ali ndi ine.+ 17  Ndiponso m’Chilamulo chanu chomwechi analembamo kuti, ‘Umboni wa anthu awiri ndi woona.’+ 18  Ineyo pandekha ndimadzichitira umboni, ndipo Atate amene anandituma amandichitiranso umboni.”+ 19  Pamenepo iwo anati: “Atate wako ali kuti?” Yesu anayankha kuti: “Inu simukundidziwa ine kapena Atate wanga.+ Mukanandidziwa ine, mukanadziwanso Atate wanga.”+ 20  Ananena mawu amenewa ali m’malo a zopereka+ pamene anali kuphunzitsa m’kachisi. Koma palibe amene anamugwira,+ chifukwa nthawi yake+ inali isanafikebe. 21  Choncho iye anawauzanso kuti: “Ine ndikuchoka ndipo mudzandifunafuna,+ koma mudzafabe m’tchimo lanu.+ Kumene ine ndikupita inu simungathe kukafikako.” 22  Pamenepo Ayudawo anayamba kunena kuti: “Kodi akufuna kudzipha? Nanga n’chifukwa chiyani akunena kuti, ‘Kumene ine ndikupita inu simungathe kukafikako?’”+ 23  Iye anawauza kuti: “Inu ndinu ochokera pansi pano, ine ndine wochokera kumwamba.+ Inu ndinu ochokera m’dziko lino,+ ine si wochokera m’dziko lino.+ 24  N’chifukwa chake ndakuuzani kuti, Inu mudzafa m’machimo anu.+ Pakuti ngati simukhulupirira kuti ine ndine amene munali kumuyembekezera uja, mudzafa m’machimo anu.”+ 25  Choncho iwo anayamba kunena kuti: “Kodi iwe ndiwe ndani?” Yesu anati: “N’chifukwa chiyani ndikudzivuta kulankhula nanu? 26  Ndili ndi zambiri zoti ndinene zokhudza inu ndi kuperekerapo chiweruzo. Ndipotu amene anandituma ine amanena zoona. Zimene ndinamva kwa iye, zomwezo ndikuzilankhula m’dzikoli.”+ 27  Iwo sanazindikire kuti anali kunena za Atatewo. 28  Pamenepo Yesu anati: “Mukadzamukweza+ Mwana wa munthu,+ pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine amene munali kumuyembekezera uja,+ ndi kutinso sindichita kanthu mongoganiza ndekha.+ Koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.+ 29  Ndipo amene ananditumayo ali ndi ine. Iye sandisiya ndekha, chifukwa ndimachita zinthu zomukondweretsa nthawi zonse.”+ 30  Pamene anali kulankhula zimenezi, ambiri anakhulupirira mwa iye.+ 31  Chotero Yesu anapitiriza kuuza Ayuda amene anamukhulupirirawo kuti: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse,+ ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. 32  Mudzadziwa choonadi,+ ndipo choonadi chidzakumasulani.”+ 33  Iwo anamuyankha kuti: “Ifetu ndife ana a Abulahamu+ ndipo sitinakhalepo akapolo a munthu.+ Tsopano iwe ukunena bwanji kuti, ‘Mudzamasulidwa’?” 34  Yesu anawayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimo.+ 35  Komanso, kapolo sakhala m’banjamo kwamuyaya, mwana ndiye amakhalamo kwamuyaya.+ 36  Choncho ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.+ 37  Ndikudziwa kuti ndinu ana a Abulahamu, koma mukufuna kundipha,+ chifukwa mawu anga sakukhazikika mwa inu.+ 38  Zimene ndinaziona kwa Atate wanga+ ndi zimene ndimalankhula.+ Chotero inunso mumachita zimene mwamva kwa atate wanu.” 39  Poyankha iwo anati: “Atate wathu ndi Abulahamu.”+ Yesu anawauza kuti: “Ngati ndinu ana a Abulahamu,+ chitani ntchito za Abulahamu. 40  Koma tsopano mukufuna kundipha ine, munthu amene ndakuuzani choonadi chimene ndinachimva kwa Mulungu.+ Abulahamu sanachite zimenezi.+ 41  Inu mumachita ntchito za atate wanu.” Iwo anati: “Ife sitinabadwe m’chigololo,* tili ndi Atate mmodzi,+ ndiye Mulungu.” 42  Pamenepo Yesu anati: “Mulungu akanakhala Atate wanu, mukanandikonda,+ pakuti ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo ndili pano.+ Sindinabwere mwakufuna kwanga ayi, koma Iyeyo anandituma.+ 43  N’chifukwa chiyani mukulephera kuzindikira zimene ine ndikunena? N’chifukwa chakuti simukufuna kumvetsera mawu anga.+ 44  Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi,+ ndipo mukufuna kuchita zokhumba za atate wanu.+ Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake,+ ndipo sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi. Pamene akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.+ 45  Koma popeza ine ndimanena zoona, simundikhulupirira.+ 46  Ndani wa inu amene angandipeze ndi mlandu wa tchimo? Ndipo ngati ndimanena zoona, n’chifukwa chiyani simundikhulupirira?+ 47  Wochokera kwa Mulungu amamvetsera mawu a Mulungu.+ Ndiye chifukwa chake inu simumvetsera, chifukwa sindinu ochokera kwa Mulungu.”+ 48  Poyankha Ayudawo anati: “Kodi tikamanena kuti, Ndiwe Msamariya+ ndipo uli ndi chiwanda,+ tikulakwitsa ngati?” 49  Yesu anayankha kuti: “Ndilibe chiwanda ine, ndimalemekeza Atate wanga,+ koma inu mukundinyoza. 50  Komatu ine sindikudzifunira ndekha ulemerero.+ Alipo Wina amene akuufuna ndipo iye ndi woweruza.+ 51  Ndithudi ndikukuuzani, ngati munthu akusunga mawu anga, sadzaona imfa.”+ 52  Ayudawo anati: “Tsopano tadziwa ndithu kuti uli ndi chiwanda.+ Abulahamu anamwalira,+ ndiponso aneneri.+ Koma iwe ukunena kuti, ‘Ngati munthu asunga mawu anga sadzalawa+ imfa.’ 53  Kodi iweyo ndiwe wamkulu+ kuposa atate wathu Abulahamu amene anamwalira? Aneneri nawonso anamwalira.+ Ndiye iweyo ukudziyesa ndani?” 54  Yesu anayankha kuti: “Ngati ndikudzilemekeza ndekha, ndiye kuti ulemerero wanga ndi wopanda pake. Atate wanga ndi amene amandilemekeza,+ amene inu mukuti ndi Mulungu wanu, 55  chikhalirecho simukumudziwa.+ Koma ine ndikumudziwa.+ Ngati ndinganene kuti sindikumudziwa ndingakhale wabodza, kufanana ndi inuyo. Koma ndikumudziwa ndithu ndipo ndikusunga mawu ake.+ 56  Atate wanu Abulahamu anali wosangalala poyembekezera kuona tsiku langa,+ ndipo analiona moti anakondwera.”+ 57  Pamenepo Ayudawo anati: “Zaka 50 zakubadwa sunakwanitse n’komwe, ndiye ukuti unamuona Abulahamu?” 58  Yesu anati: “Ndithudi ndikukuuzani, Abulahamu asanakhaleko, ine n’kuti ndilipo kale.”+ 59  Pamenepo anatola miyala kuti amugende nayo,+ koma Yesu anabisala ndi kutuluka m’kachisimo.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 7.