Yohane 7:1-53

7  Zimenezi zitatha, Yesu anapitiriza kuyendayenda mu Galileya. Iye sanafune kumayendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anali kufunitsitsa kumupha.+  Komabe chikondwerero cha Ayuda, chikondwerero cha misasa+ chinali pafupi.  Chotero abale ake+ anamupempha kuti: “Mupite ku Yudeya kuti ophunzira anunso akaone zimene mukuchita.  Pakuti palibe amene amachita kanthu mseri koma n’kumafuna kudziwika ndi anthu. Ngati inu mumachita zimenezi, mudzionetsere poyera kudzikoli.”  Abale akewo+ sanali kumukhulupirira.+  Chotero Yesu anati: “Nthawi yanga yoyenera sinakwanebe,+ koma kwa inu, iliyonse ndi nthawi yanu yoyenera.  Dziko lilibe chifukwa chodana ndi inu, koma limadana ndi ine, chifukwa ndimachitira umboni kuti dzikoli ntchito zake ndi zoipa.+  Inuyo nyamukani mupite ku chikondwereroko. Ine sindipitako panopa, chifukwa nthawi yanga yoyenera+ sinafike.”+  Atawauza zimenezi, iye anatsalira mu Galileya. 10  Koma abale akewo atanyamuka kupita ku chikondwereroko, iyenso ananyamuka payekha. Sanapite moonekera koma mwamseri.+ 11  Chotero Ayuda anayamba kumufunafuna+ ku chikondwereroko. Iwo anali kunena kuti: “Kodi munthu ujayu ali kuti?” 12  Ndipo panali manong’onong’o ambiri onena za iye m’khamu lonse la anthulo.+ Ena anali kunena kuti: “Amene uja ndi munthu wabwino.” Ndipo ena anali kunena kuti: “Ayi si munthu wabwino amene uja, iye akusocheretsa anthu ambiri.” 13  Koma panalibe amene anali kulankhula poyera za iye chifukwa choopa Ayuda.+ 14  Tsopano chikondwererocho chitafika pakatikati, Yesu analowa m’kachisi ndipo anayamba kuphunzitsa.+ 15  Pamenepo Ayudawo anayamba kudabwa ndi kufunsa kuti: “Kodi munthu ameneyu zolembazi anazidziwa bwanji,+ popeza sanapite kusukulu?”+ 16  Yesu anawayankha kuti: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma.+ 17  Ngati munthu akufuna kuchita chifuniro cha amene ananditumayo, adzadziwa za chiphunzitsochi ngati chili chochokera kwa Mulungu,+ kapena ngati ndimalankhula za m’maganizo mwanga. 18  Wolankhula za m’maganizo mwake amadzifunira yekha ulemerero.+ Koma wofunira ulemerero iye amene anamutuma, ameneyu ali woona, ndipo mwa iye mulibe kusalungama. 19  Mose anakupatsani Chilamulo,+ si choncho kodi? Komatu palibe ngakhale mmodzi wa inu amene amamvera Chilamulocho. Nanga n’chifukwa chiyani inu mukufuna kundipha?”+ 20  Khamu la anthulo linayankha kuti: “Uli ndi chiwanda iwe.+ Akufuna kukupha ndani?” 21  Poyankha Yesu anati: “Ndangochita chinthu chimodzi chabe,+ ndipo nonsenu mukudabwa. 22  Pa chifukwa chimenechi Mose anakupatsani mdulidwe.+ Sikuti mdulidwewo ndi wochokera kwa Mose ayi, koma ndi wochokera kwa makolo akale,+ ndipo mumachita mdulidwe tsiku la sabata. 23  Ngati munthu amadulidwa tsiku la sabata posafuna kuphwanya chilamulo cha Mose, kodi mukundipsera mtima ine chifukwa ndinachiritsa munthu tsiku la sabata?+ 24  Lekani kuweruza poona maonekedwe akunja, koma muziweruza ndi chiweruzo cholungama.”+ 25  Pamenepo anthu ena okhala mu Yerusalemu anayamba kunena kuti: “Si ameneyu kodi akufuna kumupha uja?+ 26  Koma taonani! Si uyu akulankhula poyera apa,+ ndipo palibe akunenapo kanthu kwa iye. Olamulirawo sakutsimikiza ngati iyeyo alidi Khristu eti?+ 27  Koma ife tikudziwa kumene munthu ameneyu akuchokera.+ Komano Khristuyo akadzabwera, palibe amene adzadziwe kumene wachokera.”+ 28  Chotero pamene anali kuphunzitsa m’kachisimo Yesu anafuula kuti: “Inu mukundidziwa ine komanso mukudziwa kumene ndikuchokera.+ Ndipo ine sindinabwere mwa kufuna kwanga,+ alipo ndithu amene anandituma,+ koma inu simukumudziwa.+ 29  Ine ndikumudziwa,+ chifukwa ndine nthumwi. Iyeyu anandituma ine.”+ 30  Pamenepo anayamba kufufuza njira yomugwirira,+ koma palibe amene anamugwira chifukwa nthawi yake+ inali isanafike. 31  Komabe ochuluka m’khamu la anthulo anakhulupirira mwa iye+ ndipo anayamba kunena kuti: “Akadzafika Khristu, kodi adzachita zizindikiro zochuluka+ kuposa zimene munthu uyu wachita?” 32  Afarisi anamva khamu la anthulo likunong’onezana motero za iye, ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma alonda kuti akamugwire.+ 33  Pamenepo Yesu anati: “Ndikhala nanube kanthawi pang’ono ndisanapite kwa iye amene anandituma.+ 34  Mudzandifunafuna,+ koma simudzandipeza, ndipo kumene ndidzapiteko inu simudzatha kukafikako.”+ 35  Chotero Ayudawo anayamba kufunsana kuti: “Ameneyu akufuna kupita kuti, kumene ife sitingathe kukam’peza? Kapena akufuna kupita kwa Ayuda omwazikana+ mwa Agiriki ndi kukaphunzitsa Agirikiwo? 36  Kodi akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mudzandifunafuna, koma simudzandipeza, ndipo kumene ine ndidzapite inu simudzatha kukafikako’?” 37  Tsopano pa tsiku lomaliza, tsiku lalikulu la chikondwererocho,+ Yesu anaimirira ndi kufuula kuti: “Ngati wina akumva ludzu,+ abwere kwa ine adzamwe madzi. 38  Wokhulupirira mwa ine,+ ‘Mkati mwake mwenimwenimo mudzatuluka mitsinje ya madzi amoyo,’ monga mmene Malemba amanenera.”+ 39  Pamenepa anali kunena za mzimu umene onse okhulupirira mwa iye anali pafupi kulandira. Pakuti pa nthawiyi n’kuti asanaulandire,+ chifukwa Yesu anali asanalandire ulemerero wake.+ 40  Choncho ena m’khamulo, amene anamva mawu amenewa, anayamba kunena kuti: “Ameneyu ndi Mneneri ndithu.”+ 41  Ena anali kunena kuti: “Khristu uja ndi ameneyu.”+ Koma ena anati: “Iyayi, kodi Khristu+ angachokere mu Galileya?+ 42  Kodi Malemba sanena kuti Khristu adzatuluka mwa ana a Davide,+ komanso mu Betelehemu+ mudzi umene Davide anali kukhala?”+ 43  Choncho khamu la anthulo linagawanika pa nkhani ya iye.+ 44  Ena a iwo anali kufunitsitsa kumugwira, koma palibe ngakhale mmodzi amene anamukhudza. 45  Tsopano alonda aja anabwerera kwa ansembe aakulu ndi Afarisi. Ndiyeno iwowa anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani simunabwere naye?” 46  Alondawo anayankha kuti: “Palibe munthu amene analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.”+ 47  Pamenepo Afarisiwo anati: “Kodi inunso mwasocheretsedwa? 48  Palibe ndi mmodzi yemwe mwa olamulira kapena Afarisi amene wakhulupirira mwa iye, alipo ngati?+ 49  Koma khamu lonseli la anthu osadziwa Chilamulo ndi lotembereredwa.”+ 50  Nikodemo, amene m’mbuyomo anabwera kwa iye, komanso anali mmodzi wa iwo, anawauza kuti: 51  “Chilamulo chathu sichiweruza munthu asanafotokoze maganizo ake choyamba+ ndi kudziwa zochita zake, chimatero ngati?” 52  Poyankha iwo anati: “Kodi iwenso ndiwe wochokera ku Galileya eti? Fufuza ndipo sudzapeza pamene pamati m’Galileya mudzatuluka mneneri.”*+ * Mipukutu ya Codex Sinaiticus, Codex Vaticanus ndi Sinaitic Syriac, inachotsa vesi 53 mpaka chaputala 8, vesi 11. (M’mabuku ambiri Achigiriki mawu a mavesi amenewa amasiyanasiyana.) Ndimezi zili ndi mawu akuti: 53  Zitatero aliyense ananyamuka n’kupita kwawo.

Mawu a M'munsi