Yohane 6:1-71

6  Tsopano Yesu anawolokera kutsidya lina la nyanja ya Galileya,* kapena kuti nyanja ya Tiberiyo.+  Koma khamu lalikulu la anthu linali kumutsatira, chifukwa linali kuona zizindikiro zimene iye anali kuchita pa odwala.+  Choncho Yesu anakwera m’phiri.+ Kumeneko anakhala pansi pamodzi ndi ophunzira ake.  Tsopano chikondwerero cha Ayuda cha pasika+ chinayandikira.  Ndiyeno Yesu atakweza maso ake ndi kuona khamu lalikulu la anthu likubwera kwa iye, anafunsa Filipo kuti: “Kodi mitanda ya mkate yodyetsa anthu onsewa tikaigula kuti?”+  Komatu iye ananena izi mongomuyesa, popeza anali atadziwa kale chimene ati achite.  Filipo anamuyankha kuti: “Ngakhale mitanda ya mkate ya ndalama zokwana madinari 200 singawakwanire amenewa. Singawakwanire ngakhale titati aliyense angolandirako pang’ono.”+  Mmodzi wa ophunzira ake, Andireya m’bale wake wa Simoni Petulo, anati:  “Pali kamnyamata pano kamene kali ndi mitanda isanu ya mkate wa balere+ ndi tinsomba tiwiri. Koma nanga zimenezi zingakwanire, poyerekeza ndi chikhamu chonse cha anthuchi?”+ 10  Yesu ananena kuti: “Akhazikeni pansi anthuwa muja amakhalira pa chakudya.”+ Pamalopo panali udzu wambiri. Choncho amuna pafupifupi 5,000 anakhaladi pansi.+ 11  Ndiyeno Yesu anatenga mitanda ya mkate ija. Atayamika, anaigawira kwa anthu onse amene anakhala pansi aja. Chimodzimodzinso ndi tinsomba tija, anatigawira kwa anthuwo mmene aliyense anafunira.+ 12  Anthu onsewo atakhuta,+ iye anauza ophunzira ake kuti: “Sonkhanitsani zotsala zonse, kuti pasawonongeke chilichonse.” 13  Choncho anatolera zonse, ndipo zinadzaza madengu 12 kuchokera pa mitanda ya mkate wa balere isanu ija, imene onse anadya ndi kuilephera.+ 14  Tsopano anthuwo ataona zizindikiro zimene anachitazo, anayamba kunena kuti: “Mosakayika uyu ndi mneneri+ uja amene anati adzabwera padziko.” 15  Choncho Yesu atadziwa kuti iwo akufuna kumugwira kuti amuveke ufumu, anachoka+ ndi kupitanso kuphiri yekhayekha. 16  Chakumadzulo ndithu, ophunzira ake anapita kunyanja.+ 17  Iwo anakwera ngalawa ndi kuyamba kuwoloka nyanja kulowera ku Kaperenao. Pa nthawiyi n’kuti mdima utagwa ndipo Yesu anali asanabwerebe kwa iwo. 18  Komanso nyanja inayamba kuwinduka chifukwa panali kuwomba mphepo yamphamvu.+ 19  Koma atapalasa makilomita pafupifupi 5 kapena 6, anaona Yesu akuyenda panyanja, kuyandikira ngalawayo ndipo iwo anachita mantha.+ 20  Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Ndine, musachite mantha!”+ 21  Pamenepo anamulandira m’ngalawa yawo, ndipo posapita nthawi ngalawa ija inakaima kumtunda kumene anali kupita.+ 22  Tsiku lotsatira, anthu amene anaima kutsidya lina la nyanjayo anaona kuti ngalawa ina palibe koma pali imodzi yokha yaing’ono. Choncho anadziwa kuti Yesu sanakwere ngalawa pamodzi ndi ophunzira ake koma kuti ophunzira akewo anachoka paokha. 23  Ngalawa zochokera ku Tiberiyo zinafika pafupi ndi pamalo amene anthuwo anadyera mkate uja Ambuye atayamika. 24  Ndiyeno khamu la anthulo litaona kuti Yesu komanso ophunzira ake kulibe, linakwera ngalawa zawo zing’onozing’ono ndi kupita ku Kaperenao kukafunafuna+ Yesu. 25  Atamupeza kutsidya kwa nyanjayo anamufunsa kuti: “Rabi,+ mwafika nthawi yanji kuno?” 26  Yesu anawayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mukundifunafuna osati chifukwa munaona zizindikiro ayi, koma chifukwa munadya mikate ndi kukhuta.+ 27  Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka,+ koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha,+ chimene Mwana wa munthu adzakupatsani. Pakuti Atate, Mulungu yekhayo, waika chisindikizo pa iye chomuvomereza.”+ 28  Pamenepo iwo anati: “Tichite chiyani kuti tigwire ntchito za Mulungu?” 29  Yesu anawauza kuti: “Ntchito ya Mulungu ndi iyi, musonyeze chikhulupiriro+ mwa amene Iyeyo anamutuma.”+ 30  Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Ndiye inuyo muchita chizindikiro+ chotani, kuti ife tichione, ndi kukukhulupirirani? Muchita ntchito yotani? 31  Makolo athu anadya mana+ m’chipululu, monga mmene Malemba amanenera kuti, ‘Anawapatsa chakudya chochokera kumwamba kuti adye.’”+ 32  Pamenepo Yesu anati: “Ndithudi ndikukuuzani, Mose sanakupatseni chakudya chochokera kumwamba, koma Atate wanga amakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba.+ 33  Iye wotsika kuchokera kumwamba, amene amapereka moyo kudziko ndiye chakudya chimene Mulungu amapereka.” 34  Choncho iwo anati: “Ambuye, muzitipatsa chakudya chimenechi nthawi zonse.”+ 35  Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Ine ndine chakudya chopatsa moyo. Aliyense wobwera kwa ine sadzamva njala ngakhale pang’ono, ndipo wokhulupirira mwa ine sadzamva ludzu.+ 36  Koma ndakuuzani kuti, Ngakhale mwandiona, simukukhulupirirabe.+ 37  Chilichonse chimene Atate adzandipatse chidzabwera kwa ine, ndipo wobwera kwa ine sindidzamukana.+ 38  Chifukwa ndinatsika kuchokera kumwamba+ kudzachita chifuniro cha iye amene anandituma, osati chifuniro changa.+ 39  Chifuniro cha amene anandituma ine n’chakuti, ndisataye aliyense mwa onse amene iye wandipatsa, koma kuti ndidzawaukitse+ pa tsiku lomaliza. 40  Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi chakuti, aliyense woona Mwana ndi kukhulupirira mwa iye akhale nawo moyo wosatha,+ ndipo ine ndidzamuukitsa pa tsiku lomaliza.”+ 41  Pamenepo Ayudawo anayamba kung’ung’udza za iye chifukwa ananena kuti: “Ine ndine chakudya chotsika kumwamba.”+ 42  Iwo anayamba kunena kuti:+ “Kodi uyu si Yesu mwana wa Yosefe,+ amene bambo ake ndi mayi ake tikuwadziwa? Nanga bwanji pano akunena kuti, ‘Ndinatsika kumwamba’?” 43  Poyankha Yesu anati: “Musang’ung’udze inu. 44  Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine,+ ndipo ine ndidzamuukitsa tsiku lomaliza.+ 45  Zinalembedwa m’Mabuku a Aneneri kuti, ‘Ndipo onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.’*+ Aliyense amene wamva kwa Atate ndipo waphunzira amabwera kwa ine.+ 46  Sikuti alipo munthu amene anaonapo Atate ayi,+ kupatulapo yekhayo amene anachokera kwa Mulungu, ameneyu anaona Atate.+ 47  Ndithudi ndikukuuzani, Wokhulupirira ali nawo moyo wosatha.+ 48  “Ine ndine chakudya+ chopatsa moyo. 49  Makolo anu anadya mana+ m’chipululu koma anamwalirabe. 50  Ichi ndi chakudya chochokera kumwamba, choti aliyense adyeko kuti asamwalire. 51  Ine ndine chakudya chamoyo chotsika kumwamba. Ngati wina adyako chakudya chimenechi adzakhala ndi moyo kosatha. Ndipotu chakudya chimene ndidzapereke kuti dzikoli lipeze moyo,+ ndicho mnofu wangawu.”+ 52  Pamenepo Ayudawo anayamba kutsutsana okhaokha, kuti: “Kodi munthu uyu angathe bwanji kutipatsa mnofu wake kuti tidye?” 53  Choncho Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mukapanda kudya mnofu+ wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake,+ mulibe moyo+ mwa inu. 54  Wakudya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga ali nawo moyo wosatha, ndipo ndidzamuukitsa+ kwa akufa tsiku lomaliza. 55  Pakuti mnofu wanga ndi chakudya chenicheni, ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. 56  Munthu wakudya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga, iyeyo ndi ine timakhala ogwirizana.+ 57  Monga Atate wamoyo+ anandituma ine, ndipo ine ndili ndi moyo chifukwa cha Atate, momwemonso amene akudya ine, nayenso adzakhala ndi moyo chifukwa cha ine.+ 58  Chimenechi ndiye chakudya chotsika kumwamba. N’chosiyana ndi chakudya chimene makolo anu anadya koma anamwalirabe. Iye wakudya chakudya ichi adzakhala ndi moyo kosatha.”+ 59  Zinthu zimenezi anazinena pamene anali kuphunzitsa m’bwalo losonkhanira ku Kaperenao. 60  Pamenepo ambiri mwa ophunzira ake atamva zimenezi anati: “Mawu amenewa ndi ozunguza. Ndani angamvetsere zimenezi?”+ 61  Koma Yesuyo, pakuti anadziwa payekha kuti ophunzira ake akung’ung’udza pa mawuwo, anafunsa kuti: “Kodi mawuwa mwakhumudwa+ nawo? 62  Nanga zidzakhala bwanji mukadzaona Mwana wa munthu akukwera kupita kumene anali poyamba?+ 63  Mzimu ndi umene umapatsa moyo,+ mnofu n’ngopanda phindu. Mawu amene ndakuuzaniwa ndiwo mzimu+ ndiponso ndiwo moyo.+ 64  Koma pali ena mwa inu amene sakukhulupirira.” Pakuti kuchokera pa chiyambi, Yesu anadziwa amene sanali kukhulupirira komanso amene adzamupereka.+ 65  Choncho anapitiriza kunena kuti: “N’chifukwa chake ndinakuuzani kuti, Munthu sangabwere kwa ine popanda Atate kumulola.”+ 66  Pa chifukwa chimenechi ophunzira ake ambiri anamusiya ndi kubwerera ku zinthu zakumbuyo,+ ndipo sanayendenso naye.+ 67  Tsopano Yesu anafunsa ophunzira ake 12 aja kuti: “Inunso mukufuna kupita kapena?” 68  Simoni Petulo+ anayankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani?+ Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.+ 69  Ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera wa Mulungu.”+ 70  Pamenepo Yesu anati: “Ine ndinakusankhani inu 12,+ si choncho kodi? Komatu mmodzi wa inu ndi wonenera anzake zoipa.”+ 71  Kwenikweni iye anali kunena za Yudasi mwana wa Simoni Isikariyoti, pakuti ameneyu anali kudzamupereka,+ ngakhale anali mmodzi wa ophunzira 12 amenewo.

Mawu a M'munsi

M’Baibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, “nyanja ya Kinereti,” “nyanja ya Genesarete,” komanso “nyanja ya Tiberiyo.”
Onani Zakumapeto 2.