Yohane 5:1-47

5  Pambuyo pa zonsezi, kunali chikondwerero+ cha Ayuda, ndipo Yesu ananyamuka kupita ku Yerusalemu.  Tsopano mu Yerusalemu pachipata cha nkhosa+ pali dziwe limene m’Chiheberi limatchedwa Betesida. M’mbali mwa dziwelo muli makonde asanu amene ali ndi zipilala.  Mmenemu munagona anthu ambiri odwala, akhungu, olumala ndi ena opuwala ziwalo. 4 * ——  Pamenepo panalinso mwamuna wina amene anakhala akudwala zaka 38.  Ataona munthu ameneyu ali chigonere, komanso podziwa kuti wakhala akudwala nthawi yaitali,+ Yesu anamufunsa kuti: “Kodi ukufuna kuchira?”+  Wodwalayo anamuyankha kuti: “Bambo, ndilibe munthu wondiviika m’dziwemu madzi akawinduka, ndipo ndikati ndikalowemo wina amandipitirira n’kulowamo.”  Yesu anati: “Nyamuka, nyamula machira akowa ndi kuyamba kuyenda.”+  Nthawi yomweyo munthu uja anachira. Pamenepo ananyamula machira akewo n’kuyamba kuyenda. Komano limenelo linali tsiku la sabata.+ 10  Choncho Ayuda anayamba kuuza munthu wochiritsidwa uja kuti: “Lero ndi Sabata, n’kosaloleka+ kuti unyamule machirawa.” 11  Iye anawayankha kuti: “Amene wandichiritsayo wandiuza kuti, ‘Nyamula machira akowa ndi kuyamba kuyenda.’” 12  Iwo anamufunsa kuti: “Ndiye ndani amene wakuuza kuti, ‘Nyamula machira ndi kuyamba kuyenda’?” 13  Koma munthu wochiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani, pakuti Yesu anali atalowa m’chikhamu cha anthu amene anali pamalopo. 14  Kenako Yesu anapeza munthu uja m’kachisi ndi kumuuza kuti: “Onatu wachira tsopano. Usakachimwenso, kuti chinachake choopsa kuposa matenda chisadzakuchitikire.” 15  Munthu uja anachoka ndi kukauza Ayuda aja kuti Yesu ndi amene wamuchiritsa. 16  Atamva zimenezi Ayudawo anayamba kuvutitsa+ Yesu, chifukwa anali kuchita zinthu zimenezi pa Sabata. 17  Koma iye anawauza kuti: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.”+ 18  Pa chifukwa chimenechi, Ayudawo anayamba kufunafuna njira yomuphera,+ chifukwa kuwonjezera pa kuphwanya Sabata, anali kunenanso kuti Mulungu ndi Atate wake,+ kudziyesa wofanana+ ndi Mulungu. 19  Ndipo Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mwanayo sangachite chilichonse chongoganiza payekha, koma chokhacho chimene waona Atate wake akuchita.+ Pakuti zilizonse zimene Atatewo amachita, Mwana amachitanso zomwezo. 20  Atatewo amakonda Mwana wake.+ Amamuonetsa zonse zimene iwo akuchita, ndipo adzamuonetsa ntchito zazikulu kuposa izi, kuti inu mudabwe.+ 21  Pakuti monga Atate amaukitsa akufa ndi kuwapatsa moyo,+ nayenso Mwana amapereka moyo kwa amene iye wafuna kuwapatsa.+ 22  Atate saweruza munthu aliyense, koma wapereka udindo wonse woweruza kwa Mwana,+ 23  kuti onse alemekeze Mwana+ monga mmene amalemekezera Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamutuma.+ 24  Ndithudi ndikukuuzani, Iye wakumva mawu anga ndi kukhulupirira amene anandituma ine ali nawo moyo wosatha,+ ndipo salowa m’chiweruzo koma wachoka ku imfa, waolokera ku moyo.+ 25  “Ndithudi ndikukuuzani, Nthawi idzafika, ndipo ndi inoyi, pamene akufa+ adzamva mawu+ a Mwana wa Mulungu, ndipo olabadirawo adzakhala ndi moyo.+ 26  Pakuti monga Atate ali nawo moyo mwa iwo wokha,+ alolanso Mwana kukhala nawo moyo mwa iye yekha.+ 27  Amupatsanso mphamvu zoweruza,+ chifukwa iye ndi Mwana wa munthu.+ 28  Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso+ adzamva mawu ake 29  ndipo adzatuluka. Amene anali kuchita zabwino adzauka kuti alandire moyo.+ Amene anali kuchita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.+ 30  Ine sindingachite chilichonse chongoganiza ndekha. Ndimaweruza malinga ndi mmene ndamvera, ndipo chiweruzo chimene ndimapereka n’cholungama,+ chifukwa sinditsatira chifuniro changa, koma chifuniro+ cha amene anandituma. 31  “Ngati ndidzichitira umboni+ ine ndekha, ndiye kuti umboni wanga suli woona.+ 32  Alipo wina amene akuchitira umboni za ine, ndipo ndikudziwa kuti umboni umene akundichitirawo+ ndi woona. 33  Inu munatumiza anthu kwa Yohane, ndipo iye anachitira umboni choonadi.+ 34  Komatu ine sindivomereza umboni wochokera kwa munthu, koma ndikunena izi kuti inu mupulumuke.+ 35  Munthu ameneyu anali nyale yoyaka ndi yowala, ndipo kwa kanthawi kochepa inu munali ofunitsitsa kusangalala m’kuwala kwakeko.+ 36  Koma ine ndili ndi umboni woposa wa Yohane, pakuti ntchito zenizenizo zimene Atate wanga anandipatsa kuti ndizikwaniritse, ntchito zimene ine ndikuchita,+ zikundichitira umboni kuti Atate ananditumadi. 37  Komanso Atate amene anandituma andichitira umboni.+ Inu simunamvepo mawu ake nthawi ina iliyonse, kapena kuona thupi lake.+ 38  Mawu akenso sanakhazikike mwa inu, chifukwa simukhulupirira amene Atatewo anamutumiza. 39  “Inu mumafufuza m’Malemba,+ chifukwa mumaganiza kuti kudzera m’Malembawo mudzapeza moyo wosatha, ndipo Malemba omwewo ndi amenenso amachitira umboni za ine.+ 40  Koma simufuna kubwera kwa ine kuti mupeze moyo.+ 41  Sindikufuna ulemerero wochokera kwa anthu,+ 42  koma ndikudziwa bwino ndithu kuti mwa inu mulibe chikondi cha Mulungu.+ 43  Ndabwera m’dzina la Atate wanga,+ ndipo simunandilandire, koma wina akanabwera m’dzina lake, mukanamulandira ameneyo. 44  Mungakhulupirire bwanji, pamene mumalandira ulemerero+ kuchokera kwa anthu anzanu, koma osayesetsa kupeza ulemerero wochokera kwa Mulungu yekhayo?+ 45  Musaganize kuti ine ndikunenezani kwa Atate. Alipo amene amakunenezani, ndiye Mose+ amene munaika chiyembekezo chanu mwa iye. 46  Ndipo ngati mukanakhulupirira Mose, mukanakhulupiriranso ine, pakuti iyeyo analemba za ine.+ 47  Koma ngati simukhulupirira zolemba za ameneyo,+ mungakhulupirire bwanji mawu anga?”

Mawu a M'munsi

Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.