Yohane 4:1-54

4  Tsopano Ambuye atazindikira kuti Afarisi anamva kuti Yesu anali kuphunzitsa anthu ambiri kuposa Yohane ndipo anali kuwabatiza+ kuti akhale ophunzira,  ngakhale kuti kwenikweni si Yesu amene anali kubatiza koma ophunzira ake,  anachoka ku Yudeya ndi kupitanso ku Galileya.  Koma anafunika kuti adzere ku Samariya.+  Choncho anafika mumzinda wa Samariya wotchedwa Sukari pafupi ndi munda umene Yakobo anapatsa mwana wake Yosefe.+  Ndipotu kumeneko kunali kasupe+ wa Yakobo. Yesu atatopa ndi ulendowo, anakhala pansi pakasupepo. Nthawi n’kuti ili cha m’ma 12 koloko masana.*  Ndiyeno mayi wina wa mu Samariya anafika kudzatunga madzi. Yesu anapempha mayiyo kuti: “Mundipatseko madzi akumwa mayi.”  (Ophunzira ake anali atalowa mumzinda kukagula chakudya.)  Mayi wachisamariyayo anafunsa Yesu kuti: “Popeza inu ndinu Myuda, bwanji mukupempha madzi akumwa kwa ine, mayi wachisamariya?” (Pakuti Ayuda ndi Asamariya sayanjana.)+ 10  Poyankha Yesu anauza mayiyo kuti: “Mukanadziwa mphatso+ yaulere ya Mulungu ndi amene+ akukuuzani kuti, ‘Mundipatseko madzi akumwa,’ mukanam’pempha iyeyo, ndipo akanakupatsani madzi amoyo.”+ 11  Mayiyo anati: “Bambo, mulibe n’chotungira chomwe, ndipo chitsimechinso n’chozama. Nanga madzi amoyowo mwawatenga kuti? 12  Kodi inu ndinu wamkulu+ kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi, chimenenso iyeyo, ana ake ndi ng’ombe zake anali kumwa?” 13  Poyankha, Yesu anamuuza kuti: “Aliyense wakumwa madzi awa adzamvanso ludzu. 14  Koma amene adzamwa madzi amene ine ndidzam’patse sadzamvanso ludzu m’pang’ono pomwe.+ Ndipo madzi amene ndidzam’patse, adzasanduka kasupe wa madzi+ otuluka mwa iye, opatsa moyo wosatha.”+ 15  Mayiyo anauza Yesu kuti: “Bambo, ndipatseni madzi amenewo, kuti ndisadzamvenso ludzu komanso kuti ndisamabwerenso kuno kudzatunga madzi.” 16  Iye anauza mayiyo kuti: “Pitani, kaitaneni mwamuna wanu abwere kuno.” 17  Mayiyo anayankha kuti: “Ndilibe mwamuna.” Yesu anati: “Mwanena zoona mmene mukuti, ‘Ndilibe mwamuna.’ 18  Pakuti mwakwatiwapo ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene muli naye panopa si mwamuna wanu. Apa mwanenadi zoona.” 19  Mayiyo anati: “Bambo, ndazindikira kuti ndinu mneneri.+ 20  Makolo athu anali kulambira m’phiri ili,+ koma anthu inu mumanena kuti Yerusalemu ndiwo malo kumene anthu ayenera kulambirirako.”+ 21  Yesu anauza mayiyo kuti: “Mayi, Ndithu nthawi idzafika pamene anthu inu simudzalambira+ Atate m’phiri ili kapena ku Yerusalemu.+ 22  Inu mumalambira chimene simuchidziwa.+ Ife timalambira chimene tikuchidziwa, chifukwa chipulumutso chikuchokera kwa Ayuda.+ 23  Komabe nthawi idzafika, ndipo ndi yomwe ino, pamene olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu+ ndi choonadi,+ pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.+ 24  Mulungu ndiye Mzimu,+ ndipo onse omulambira ayenera kumulambira motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.”+ 25  Pamenepo mayiyo anati: “Ndikudziwa kuti Mesiya+ akubwera, wotchedwa Khristu.+ Ameneyo akadzafika, adzatifotokozera zonse poyera.” 26  Yesu anamuuza kuti: “Munthu ameneyo ndi ineyo amene ndikulankhula nanu.”+ 27  Tsopano ophunzira ake anafika, ndipo anayamba kudabwa chifukwa anali kulankhula ndi munthu wamkazi. Komabe palibe amene ananena kuti: “Mukufuna chiyani kwa iye?” kapena kuti, “N’chifukwa chiyani mukulankhula ndi mayiyu?” 28  Choncho mayi uja anasiya mtsuko wake wa madzi ndi kukalowa mumzinda ndipo anauza anthu kuti: 29  “Tiyeni kuno mukaone munthu amene wandiuza zonse zimene ndakhala ndikuchita. Kodi ameneyu n’kukhala Khristu+ kapena?” 30  Iwo anatuluka mumzindawo ndi kubwera kumene kunali Yesu. 31  Apa n’kuti ophunzira ake akumupempha kuti: “Rabi,+ idyani.” 32  Koma iye anawauza kuti: “Chakudya ndili nacho chimene inu simukuchidziwa.” 33  Pamenepo ophunzirawo anayamba kufunsana kuti: “Pali amene wamubweretsera chakudya ngati?” 34  Yesu anati: “Chakudya+ changa ndicho kuchita chifuniro+ cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.+ 35  Kodi inu simunena kuti kwatsala miyezi inayi kuti tiyambe kukolola? Koma ndikuti: Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.+ Moti pano 36  wokolola akulandira kale malipiro ndipo akusonkhanitsa zipatso ku moyo wosatha,+ kuti wofesa mbewu+ ndi wokolola asangalalire pamodzi.+ 37  Ndiye chifukwa chake mawu aja ali oona akuti, Wina ndi wofesa ndipo wina ndi wokolola. 38  Ine ndakutumizani kukakolola zimene simunakhetsere thukuta. Ena anagwira ntchito mwakhama,+ ndipo inu mwalowa kukapindula ndi ntchito imene iwo anaigwira mwamphamvu.” 39  Pamenepo Asamariya ambiri ochokera mumzindawo anakhulupirira+ mwa iye chifukwa cha mawu a mayi uja amene pochitira umboni anati: “Iyeyu anandiuza zinthu zonse zimene ndakhala ndikuchita.”+ 40  Choncho Asamariya atafika kwa iye, anayamba kumupempha kuti akhalebe nawo, ndipo anakhala nawo masiku awiri.+ 41  Zotsatira zake, anthu ochuluka anakhulupirira chifukwa cha zimene iye anali kunena.+ 42  Iwo anayamba kuuza mayi uja kuti: “Sikuti tikukhulupirira chifukwa cha mawu ako ajanso ayi, pakuti tadzimvera tokha+ ndipo tadziwa ndithu kuti munthu uyu ndi mpulumutsi+ wa dziko.” 43  Masiku awiriwo atatha, iye anachoka kumeneko ndi kupita ku Galileya.+ 44  Yesu mwiniyo anachitira umboni kuti mneneri salemekezedwa kwawo.+ 45  Choncho pamene anafika ku Galileya, Agalileyawo anamulandira, chifukwa anali ataona zonse zimene anachita pa chikondwerero ku Yerusalemu,+ pakuti nawonso anapita ku chikondwereroko.+ 46  Kenako anafikanso ku Kana+ wa ku Galileya, kumene anasandutsa madzi kukhala vinyo kuja.+ Tsopano kumeneku kunali munthu wina mtumiki wa mfumu, amene mwana wake wamwamuna anali kudwala ku Kaperenao.+ 47  Munthuyu atamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, anapita kwa iye ndi kuyamba kumupempha kuti apiteko ndi kukachiritsa mwana wakeyo, pakuti anali pafupi kumwalira. 48  Koma Yesu anamuuza kuti: “Ngati anthu inu simunaone zizindikiro+ ndi zodabwitsa,+ simungakhulupirire ngakhale pang’ono.” 49  Mtumiki wa mfumu uja anati: “Ambuye, tiyeni mwana wanga asanafe.” 50  Yesu anati: “Pita,+ mwana wako ali moyo.”+ Munthuyo anakhulupirira mawu amene Yesu anamuuzawo ndipo anapitadi. 51  Ali m’njira, akapolo ake anamuchingamira kudzamuuza kuti mnyamata wake ali moyo.+ 52  Choncho iye anayamba kuwafunsa ola limene anachira. Iwo anamuuza kuti: “Malungo* ake anatha dzulo cha m’ma 1 koloko masana.”*+ 53  Pamenepo bamboyo anadziwa kuti linali ola lomwelo+ pamene Yesu anamuuza kuti: “Mwana wako ali moyo.” Ndipo iye ndi banja lake lonse anakhulupirira.+ 54  Ichi chinalinso chizindikiro+ chachiwiri chimene Yesu anachita atatuluka mu Yudeya ndi kulowa mu Galileya.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”
Mawu ake enieni, “ola la 7,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.