Yohane 3:1-36

3  Tsopano panali Mfarisi wina dzina lake Nikodemo,+ wolamulira wa Ayuda.  Iyeyu anabwera kwa Yesu usiku+ ndi kumuuza kuti: “Rabi,+ tikudziwa kuti inu ndinu mphunzitsi+ wochokera kwa Mulungu,+ chifukwa munthu sangathe kuchita zizindikiro+ zimene inu mumachita ngati Mulungu sali naye.”+  Poyankha Yesu anati:+ “Ndithudi ndikukuuza, Munthu sangathe kuona ufumu wa Mulungu atapanda kubadwanso.”+  Nikodemo anafunsa kuti: “Munthu angabadwe bwanji ali wamkulu kale? Kodi angathe kulowa m’mimba mwa mayi ake ndi kubadwanso?”  Yesu anayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuza, Munthu sangathe kulowa mu ufumu wa Mulungu atapanda kubadwa mwa madzi+ ndi mzimu.+  Chobadwa mwa thupi n’chanyama, ndipo chobadwa mwa mzimu n’chauzimu.+  Usadabwe chifukwa ndakuuza kuti, Anthu inu muyenera kubadwanso.+  Mphepo+ imawombera kumene ikufuna, ndipo munthu amamva mkokomo wake, koma sadziwa kumene ikuchokera ndi kumene ikupita. N’chimodzimodzinso aliyense wobadwa mwa mzimu.”+  Poyankha Nikodemo anati: “Zimenezi zingatheke bwanji?” 10  Yesu anamufunsa kuti: “Kodi iwe sudziwa zinthu zimenezi, chikhalirecho ndiwe mphunzitsi wa Isiraeli?+ 11  Ndithudi ndikukuuza, Zimene ife timadziwa timazilankhula, ndipo zimene taona timazichitira umboni.+ Koma anthu inu simulandira umboni umene timapereka.+ 12  Ngati ndakuuzani zinthu za padziko lapansi koma inu osakhulupirira, mudzakhulupirira bwanji ndikakuuzani zinthu zakumwamba?+ 13  Ndipo palibe munthu amene anakwera kumwamba+ koma Mwana wa munthu+ yekha, amene anatsika kuchokera kumwambako.+ 14  Ndiponso, monga mmene Mose anakwezera njoka m’mwamba+ m’chipululu, momwemonso Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa m’mwamba,+ 15  kuti aliyense wokhulupirira iye akhale nawo moyo wosatha.+ 16  “Pakuti Mulungu anakonda+ kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha,+ kuti aliyense wokhulupirira+ iye asawonongeke,+ koma akhale ndi moyo wosatha.+ 17  Pakuti Mulungu anatumiza Mwana wake m’dziko, osati kuti mwanayo adzaweruze+ dziko, koma kuti mwa iye, dziko lipulumutsidwe.+ 18  Wokhulupirira mwa iye sayenera kuweruzidwa.+ Wosakhulupirira waweruzidwa kale, chifukwa sanakhulupirire m’dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.+ 19  Tsopano maziko operekera chiweruzo ndi awa, kuwala+ kwafika m’dziko+ koma anthu akonda mdima m’malo mwa kuwala,+ pakuti ntchito zawo n’zoipa. 20  Amene amachita zinthu zoipa+ amadana ndi kuwala ndipo safika pamene pali kuwala, kuti ntchito zake zisadzudzulidwe.+ 21  Koma amene amachita chimene chili chabwino amabwera pamene pali kuwala,+ kuti ntchito zake zionekere kuti anazichita mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.” 22  Izi zitatha, Yesu ndi ophunzira ake anapita m’dera la Yudeya, ndipo anakhala nawo kumeneko ndi kubatiza anthu.+ 23  Koma Yohane+ analinso kubatiza ku Ainoni pafupi ndi Salimu, chifukwa kunali madzi ambiri+ kumeneko, ndipo anthu anali kubwera kudzabatizidwa.+ 24  Pa nthawiyi n’kuti Yohane asanaponyedwe m’ndende.+ 25  Tsopano ophunzira a Yohane anayambitsa mkangano ndi Myuda wina pa nkhani yokhudza mwambo wa kuyeretsa.+ 26  Pamenepo anafika kwa Yohane ndi kumuuza kuti: “Rabi, munthu amene munali naye kutsidya kwa Yorodano uja, amene munali kumuchitira umboni uja,+ iyenso akubatiza ndipo anthu onse akupita kwa iye.”+ 27  Poyankha Yohane anati: “Munthu sangalandire kanthu kalikonse akapanda kupatsidwa kuchokera kumwamba.+ 28  Inu nomwe ndinu mboni zanga pamawu amene ndinanena kuti, Ine sindine Khristu,+ koma, ndinatumizidwa monga kalambulabwalo wake.+ 29  Iye amene ali ndi mkwatibwi ndiye mkwati.+ Koma mnzake wa mkwati, akaimirira ndi kumvetsera zimene akunena, amakhala n’chimwemwe chochuluka chifukwa cha mawu a mkwatiyo. Choncho chimwemwe changa chasefukiradi.+ 30  Ameneyo ayenera kumawonjezereka, koma ine ndiyenera kucheperachepera.” 31  Wochokera kumwamba ali woposa ena onse.+ Wochokera padziko lapansi ndi wa padziko lapansi, ndipo amalankhula zinthu za padziko lapansi.+ Koma wochokera kumwamba ali woposa ena onse.+ 32  Zimene iye waziona ndi kuzimva, akuchitira umboni zimenezo,+ koma palibe munthu amene akulandira umboni wake.+ 33  Amene walandira umboni wakewo waika chisindikizo chake pa umboniwo chakuti Mulungu amanena zoona.+ 34  Wotumidwa ndi Mulungu amalankhula mawu a Mulungu,+ pakuti akafuna kupereka mzimu sachita kuyeza pamuyezo.+ 35  Atate amakonda Mwana wake+ ndipo anapereka zinthu zonse m’manja mwake.+ 36  Iye wokhulupirira+ mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha.+ Wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu,+ koma mkwiyo wa Mulungu ukhalabe pa iye.+

Mawu a M'munsi