Yohane 20:1-31

20  Tsiku loyamba+ la mlunguwo, Mariya Mmagadala anabwera kumanda achikumbutsowo m’mawa kwambiri, kudakali mdima, ndipo anaona kuti mwala wachotsedwa kale pamanda achikumbutsowo.+  Pamenepo iye anathamanga ndi kukafika kwa Simoni Petulo ndi kwa wophunzira wina,+ amene Yesu anali kumukonda kwambiri uja. Iye anawauza kuti: “Ambuye awachotsa m’manda achikumbutso+ aja, ndipo sitikudziwa kumene awaika.”  Pamenepo Petulo+ ndi wophunzira wina uja ananyamuka kupita kumanda achikumbutsowo.  Onse awiri anayambira pamodzi kuthamanga, koma wophunzira winayo anapitirira Petulo ndi liwiro lalikulu ndipo anali woyambirira kukafika kumanda achikumbutsowo.  Atawerama ndi kuyang’anitsitsa, anangoona nsalu zokulungira mtembo zokha zija zili pansi,+ koma sanalowe mkatimo.  Kenako Simoni Petulo anafikanso m’mbuyo mwake, ndipo analowa m’manda achikumbutsowo. Mmenemo anaona nsalu zokulungira mtembozo zili pansi.+  Anaonanso nsalu ina imene anamukulungira kumutu ataipindapinda ndi kuiika payokha. Imeneyi sinaikidwe pamodzi ndi nsalu zokulungira mtembozo.  Pamenepo, wophunzira winayo, amene anali woyambirira kufika kumanda achikumbutso uja analowanso mkatimo, ndipo anaona ndi kukhulupirira zimene Mariya anawauza.  Iwo anali asanazindikire malemba akuti Yesu ayenera kuuka kwa akufa.+ 10  Pamenepo ophunzirawo anabwerera kunyumba kwawo. 11  Koma Mariya anatsala atangoima panja pafupi ndi manda achikumbutsowo akulira. Akulira choncho, anawerama kuti aone m’manda achikumbutsowo. 12  Atatero, anaona angelo awiri+ ovala zoyera, mmodzi atakhala pansi kumutu, winanso atakhala pansi kumiyendo, pamalo amene panagona mtembo wa Yesu. 13  Iwo anamufunsa kuti: “Mayi iwe, n’chifukwa chiyani ukulira?” Iye anati: “Atenga Ambuye wanga, ndipo sindikudziwa kumene awaika.” 14  Atanena zimenezi, anatembenuka ndi kuona Yesu ali chilili, koma sanam’zindikire kuti ndi Yesu.+ 15  Ndiyeno Yesu anafunsa mayiyo kuti: “Mayi iwe, n’chifukwa chiyani ukulira? Kodi Ukufuna ndani?”+ Poganiza kuti ndi wosamalira mundawo, iye anamuyankha kuti: “Bambo, ngati mwamuchotsa ndinu, ndiuzeni chonde kumene mwamuika, ndipo ine ndikamutenga.” 16  Pamenepo Yesu anati: “Mariya!”+ Pamene anatembenuka, ananena kwa iye m’Chiheberi kuti: “Rab·boʹni!”+ (kutanthauza kuti “Mphunzitsi!”) 17  Yesu anati: “Usandikangamire. Pakuti sindinakwerebe kwa Atate. Koma pita kwa abale anga+ ukawauze kuti, ‘Ine ndikukwera kwa Atate+ wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga+ ndi Mulungu wanu.’”+ 18  Mariya Mmagadala anafika ndi kuuza ophunzira uthengawo. Anati: “Ambuye ndawaona ine!” Ndipo anawauza zimene iye anamuuza zija.+ 19  Pa tsiku limenelo, tsiku loyamba la mlunguwo,+ ophunzirawo anasonkhana pamodzi madzulo. Iwo anali atakhoma zitseko m’nyumba imene analimo chifukwa choopa+ Ayuda, ndipo Yesu anafika+ n’kuimirira pakati pawo ndi kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 20  Atanena zimenezi, anawaonetsa manja ake ndi pambali pa mimba paja.+ Pamenepo ophunzirawo anasangalala+ poona Ambuyewo. 21  Kenako Yesu anawauzanso kuti: “Mtendere ukhale nanu. Mmene Atate ananditumira,+ inenso ndikutumani.”+ 22  Atanena zimenezi, anauzira mpweya pa iwo ndi kuwauza kuti: “Landirani mzimu woyera.+ 23  Mukakhululukira munthu amene wachita tchimo,+ ndiye kuti Mulungu wamukhululukira kale. Koma mukapanda kukhululukira munthu amene wachita tchimo, ndiye kuti Mulungu sanamukhululukire.”+ 24  Koma Tomasi,+ wotchedwa Didimo, mmodzi wa ophunzira 12 aja sanali pamodzi nawo pamene Yesu anafika. 25  Choncho ophunzira enawo anamuuza kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Koma iye anati: “Ndithu ndikapanda kuona mabala a misomali m’manja mwawo ndi kuika chala changa m’mabala a misomaliwo, ndiponso kuika dzanja langa m’mbali mwa mimba yawo,+ ine sindikhulupirira ayi.”+ 26  Tsopano patapita masiku 8, ophunzira akewo analinso m’nyumba, ndipo Tomasi anali nawo pamodzi. Yesu anafika ngakhale kuti zitseko zinali zokhoma. Iye anaimirira pakati pawo ndi kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 27  Kenako anauza Tomasi kuti: “Ika chala chako apa, ndiponso ona m’manja mwangamu. Gwiranso ndi dzanja lako+ m’mbali mwa mimba yangamu, kuti usakhalenso wosakhulupirira, koma wokhulupirira.” 28  Poyankha Tomasi anati: “Mbuyanga ndi Mulungu wanga!”+ 29  Yesu anamufunsa kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona? Odala ndi amene amakhulupirira ngakhale sanaone.”+ 30  Kunena zoona, Yesu anachita zizindikiro zinanso zambiri pamaso pa ophunzirawo, zimene sizinalembedwe mumpukutu uno.+ 31  Koma izi zalembedwa+ kuti mukhulupirire kuti Yesu alidi Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kutinso, mwa kukhulupirira,+ mukhale ndi moyo m’dzina lake.

Mawu a M'munsi