Yohane 2:1-25

2  Tsopano tsiku lachitatu kunali phwando la ukwati ku Kana+ ku Galileya. Mayi+ a Yesu analinso komweko.  Yesunso ndi ophunzira ake anaitanidwa ku phwando la ukwatilo.  Vinyo atatha, mayi+ a Yesu anamuuza kuti: “Vinyo waathera.”  Koma Yesu anauza mayi akewo kuti: “Kodi ndili nanu chiyani mayi?+ Nthawi yanga sinafike.”+  Mayi akewo anauza amene anali kutumikira kuti: “Chilichonse chimene angakuuzeni, chitani chimenecho.”+  Pamalopo panali mbiya zamwala zokwanira 6 malinga ndi malamulo a Ayuda a kudziyeretsa.+ Mbiya iliyonse inali ya malita pafupifupi 44 mpaka 66.  Choncho Yesu anawauza kuti: “Dzazani mbiyazi ndi madzi.” Iwo anazidzazadi mpaka pakamwa.  Ndiyeno anawauza kuti: “Tunganimo tsopano mupereke kwa woyang’anira phwandoli.” Iwo anaperekadi.  Tsopano woyang’anira phwando analawa madzi amene anawasandutsa vinyowo.+ Iye sanadziwe kumene wachokera, ngakhale kuti otumikira amene anatunga madziwo anadziwa. Atatero woyang’anira phwando uja anaitana mkwati 10  ndi kumuuza kuti: “Munthu aliyense amatulutsa vinyo wabwino choyamba,+ ndipo anthu akaledzera, m’pamene amatulutsa wosakoma kwenikweni. Koma iwe wasunga vinyo wabwino mpaka nthawi ino.” 11  Yesu anachita zimenezi ku Kana mu Galileya monga chiyambi cha zizindikiro zake. Pamenepo anaonetsa ulemerero wake,+ ndipo ophunzira ake anakhulupirira mwa iye. 12  Izi zitatha, iye, mayi ake, abale ake+ ndi ophunzira ake anapita ku Kaperenao,+ koma kumeneko sanakhaleko masiku ambiri. 13  Tsopano pasika+ wa Ayuda anali pafupi. Choncho Yesu ananyamuka kupita ku Yerusalemu.+ 14  Kumeneko anapeza ogulitsa ng’ombe, nkhosa ndi nkhunda+ komanso osintha ndalama ali m’kachisi atakhala m’mipando yawo. 15  Choncho anapanga mkwapulo wazingwe, n’kuthamangitsa onse amene anali ndi nkhosa ndi ng’ombe ndipo anawatulutsa m’kachisimo. Anakhuthula makobidi a osintha ndalama ndi kugubuduza matebulo awo.+ 16  Tsopano anauza ogulitsa nkhundawo kuti: “Chotsani izi muno! Mulekeretu kusandutsa nyumba+ ya Atate wanga kukhala nyumba ya malonda!”+ 17  Pamenepo ophunzira ake anakumbukira zimene Malemba amanena, kuti amati: “Kudzipereka kwambiri panyumba yanu kudzandidya.”+ 18  Koma Ayudawo anati: “Utionetsa chizindikiro+ chotani tsopano chosonyeza kuti uli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi?” 19  Yesu anawayankha kuti: “Gwetsani kachisi uyu,+ ndipo ine ndidzamumanga m’masiku atatu.” 20  Pamenepo Ayudawo anati: “Kachisi ameneyu anamumanga zaka 46, ndiye iwe udzamumanga m’masiku atatu?” 21  Komatu iye anali kunena za kachisi+ wa thupi lake. 22  Choncho pamene anauka kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira+ kuti anali kunena zimenezi, ndipo anakhulupirira Malemba ndi mawu amene Yesu ananena. 23  Tsopano pamene anali mu Yerusalemu pa chikondwerero+ cha pasika, anthu ambiri anakhulupirira m’dzina lake,+ ataona zizindikiro zimene anali kuchita.+ 24  Koma Yesu sanawakhulupirire+ kwenikweni chifukwa onsewo anali kuwadziwa. 25  Komanso, iye sanafunikire wina woti achite kumuuza za munthu, chifukwa payekha anali kudziwa zimene zili m’mitima ya anthu.+

Mawu a M'munsi