Yohane 19:1-42

19  Tsopano Pilato anatenga Yesu ndi kumukwapula.+  Ndipo asilikali analuka chisoti chachifumu chaminga ndi kumuveka kumutu. Anamuvekanso malaya akunja ofiirira.+  Pamenepo anayamba kubwera kwa iye ndi kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu, inu Mfumu ya Ayuda!” Komanso anali kumumenya mapama.+  Pilato anatulukanso kunja ndi kuwauza kuti: “Onani! Ndikumutulutsa panja pano kwa inu, kuti mudziwe kuti sindikupeza mlandu mwa iye.”+  Pamenepo Yesu anatulukira panja, atavala chisoti chachifumu chaminga chija ndi malaya akunja ofiirira. Ndipo Pilato anati: “Taonani! Mwamuna uja ndi uyu!”  Koma pamene ansembe aakulu ndi alonda anamuona, anafuula kuti: “M’pachikeni! M’pachikeni!”+ Pilato anawauza kuti: “M’tengeni mukamupachike nokha, chifukwa ine sindikupeza mlandu uliwonse mwa iye.”+  Ayudawo anamuyankha kuti: “Tili ndi chilamulo ife,+ ndipo malinga ndi chilamulocho iyeyu ayenera kufa, chifukwa akudziyesa mwana wa Mulungu.”+  Choncho Pilato atamva mawu amenewa, anachita mantha kwambiri.  Analowanso m’nyumba ya bwanamkubwa ndi kufunsa Yesu kuti: “Kodi umachokera kuti?” Koma Yesu sanamuyankhe.+ 10  Pamenepo Pilato anati: “Kodi sukundilankhula?+ Kodi sukudziwa kuti ine ndili ndi mphamvu yokumasula, komanso yokupachika?” 11  Yesu anamuyankha kuti: “Simukanakhala ndi mphamvu iliyonse pa ine mukanapanda kupatsidwa kuchokera kumwamba.+ Ndiye chifukwa chake munthu amene wandipereka ine kwa inu ali ndi tchimo lalikulu kwambiri.” 12  Pa chifukwa chimenechi Pilato anayesetsabe kufunafuna njira kuti amumasule. Koma Ayudawo anafuula kuti: “Mukamumasula ameneyu, ndiye kuti si inu bwenzi la Kaisara. Munthu aliyense wodziyesa yekha mfumu, ameneyo ndi wotsutsana ndi Kaisara.”+ 13  Choncho pamene Pilato anamva mawu amenewa, anatulutsa Yesu panja, ndipo iye anakhala pampando woweruzira milandu, pamalo otchedwa Bwalo Lamiyala, koma pa Chiheberi otchedwa Gabʹba·tha. 14  Ili linali tsiku lokonzekera+ pasika, ndipo nthawi inali cha m’ma 12 koloko masana.* Pamenepo iye anauza Ayudawo kuti: “Taonani! Mfumu yanu imeneyi!” 15  Koma iwo anafuula kuti: “Muthane naye! Muthane naye! M’pachikeni!” Pilato anawafunsa kuti: “Kodi ndipachike mfumu yanu?” Ansembe aakulu anayankha kuti: “Tilibe mfumu ina koma Kaisara.”+ 16  Pamenepo anamupereka kwa iwo kuti akamupachike.+ Tsopano Yesu anakhala m’manja mwawo. 17  Ndipo iye ananyamula yekha mtengo wozunzikirapo*+ ndi kutuluka+ kupita kumalo otchedwa Chibade, koma pa Chiheberi otchedwa, Gologota.+ 18  Kumeneko anamupachika+ pamodzi ndi amuna ena awiri, wina mbali iyi, wina mbali inayi, Yesu pakati.+ 19  Pilato analembanso dzina laudindo ndi kuliika pamtengo wozunzikirapowo. Analemba kuti: “Yesu Mnazareti, Mfumu ya Ayuda.”+ 20  Choncho Ayuda ambiri anawerenga dzina laudindo limeneli, chifukwa malo amene Yesu anapachikidwa anali pafupi ndi mzinda,+ ndipo analilemba m’Chiheberi, Chilatini, ndi Chigiriki. 21  Koma ansembe aakulu a Ayudawo anayamba kuuza Pilato kuti: “Musalembe kuti ‘Mfumu ya Ayuda,’ koma kuti iye ananena kuti, ‘Ndine Mfumu ya Ayuda.’” 22  Pilato anayankha kuti: “Zimene ndalemba, ndalemba.” 23  Tsopano asilikaliwo atamupachika Yesu, anatenga malaya ake akunja ndi kuwagawa m’zigawo zinayi, kuti msilikali aliyense atenge chigawo chimodzi. Panalinso malaya amkati. Koma malaya amkatiwo analibe msoko, anali owombedwa kuchokera pamwamba mpaka pansi.+ 24  Choncho iwo anayamba kukambirana kuti: “Malaya awa tisawang’ambe, koma tiyeni tichite maere kuti tidziwe amene angatenge malaya amenewa.” Izi zinachitika kuti lemba likwaniritsidwe, limene linati: “Iwo anagawana malaya anga akunja pakati pawo, ndipo anachita maere pa malaya anga amkati.”+ Chotero asilikaliwo anachitadi zimenezi. 25  Koma chapafupi ndi mtengo wozunzikirapo wa Yesu, panaimirira mayi ake+ ndi m’bale wa mayi akewo, Mariya+ mkazi wa Kulopa, ndi Mariya Mmagadala.+ 26  Choncho Yesu, poona mayi akewo ndi wophunzira amene anali kumukonda+ uja ataima chapafupi, anauza mayi akewo kuti: “Mayi, kuyambira lero, uyu akhala mwana wanu.” 27  Kenako anauza wophunzirayo kuti: “Kuyambira lero awa akhala mayi ako.” Ndipo kuyambira nthawi imeneyo wophunzirayo anatenga mayiwo ndi kupita nawo kunyumba kwake. 28  Pambuyo pake, Yesu atadziwa kuti tsopano zonse zachitika, kuti malemba akwaniritsidwe anati: “Ndikumva ludzu.”+ 29  Pamalopo panali chiwiya chodzaza vinyo wowawasa. Pamenepo anatenga chinkhupule chimene anachiviika m’vinyo wowawasayo n’kuchisomeka kukamtengo ka hisope ndi kuchifikitsa pakamwa pake.+ 30  Atalandira vinyo wowawasayo, Yesu anati: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!”+ ndipo anaweramitsa mutu, ndi kupereka mzimu wake.+ 31  Popeza linali Tsiku Lokonzekera,+ Ayudawo sanafune kuti mitembo ikhalebe+ pamitengo yozunzikirapo tsiku la Sabata, (pakuti Sabata la tsiku limeneli linali lalikulu,)+ choncho anapempha Pilato kuti opachikidwawo awathyole miyendo ndi kutsitsa mitemboyo. 32  Chotero asilikali anafika ndi kuthyola miyendo ya munthu woyamba ndiponso ya wina uja amene anapachikidwa naye pamodzi. 33  Koma atafika pa Yesu, sanamuthyole miyendo poona kuti wafa kale. 34  Koma mmodzi wa asilikaliwo anamulasa ndi mkondo m’mbalimu cham’mimba,+ ndipo nthawi yomweyo panatuluka magazi ndi madzi. 35  Munthu amene anaona zimenezo akuchitira umboni, ndipo umboni wakewo ndi woona. Munthu ameneyu akudziwa kuti amanena zoona, kuti inunso mukhulupirire.+ 36  Kwenikweni izi zinachitika kuti lemba likwaniritsidwe, pamene linati: “Sadzathyola fupa lake ndi limodzi lomwe.”+ 37  Ndiponso lemba lina limati: “Iwo adzayang’ana kwa munthu amene anamulasa.”+ 38  Tsopano zitatha izi, Yosefe wa ku Arimateya, amene anali wophunzira wa Yesu koma wamseri chifukwa anali kuopa Ayuda,+ anapempha Pilato kuti amulole kuti akachotse mtembo wa Yesu, ndipo Pilato anamupatsa chilolezo.+ Choncho anafika ndi kuchotsa mtembowo.+ 39  Nayenso Nikodemo, munthu amene anabwera kwa iye usiku poyamba paja, anabwera atatenga mule wosakaniza ndi aloye, wopitirira makilogalamu 32.+ 40  Choncho iwo anatenga mtembo wa Yesu n’kuukulunga ndi nsalu zamaliro zonunkhira,+ malinga ndi mwambo umene Ayuda anali kutsatira poika maliro. 41  Tsopano kumalo kumene anamupachikirako kunali munda. M’munda umenewo munali manda achikumbutso+ atsopano, mmene anali asanaikemo munthu chikhalire. 42  Choncho, popeza linali tsiku lokonzekera+ chikondwerero cha Ayuda, iwo anaika Yesu mmenemo, chifukwa manda achikumbutsowo anali pafupi.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Onani Zakumapeto 9.