Yohane 18:1-40

18  Atanena zimenezi, Yesu anatuluka pamodzi ndi ophunzira ake ndi kuwoloka khwawa la Kidironi,+ kupita kumene kunali munda. Ndipo iye ndi ophunzira akewo analowa m’mundamo.+  Yudasi womupereka uja, analinso kuwadziwa malowo, chifukwa nthawi zambiri Yesu anali kukumana ndi ophunzira ake kumeneko.+  Choncho Yudasi anatenga gulu la asilikali ndi alonda ochokera kwa ansembe aakulu ndi kwa Afarisi. Iwo anafika kumeneko atanyamula miyuni, nyale ndi zida.+  Chotero Yesu, podziwa zonse zimene zinali pafupi kumuchitikira,+ anawayandikira ndi kuwafunsa kuti: “Mukufuna ndani?”  Iwo anamuyankha kuti: “Yesu Mnazareti.”+ Iye anati: “Ndine amene.” Yudasi womupereka uja,+ analinso nawo pamenepo.  Koma pamene anawauza kuti: “Ndine amene,” iwo anafutuka+ ndi kugwa pansi.  Kenako anawafunsanso kuti: “Mukufuna ndani?” Iwo anati: “Yesu Mnazareti.”  Yesu anati: “Ndakuuzani kuti ndine amene. Choncho ngati mukufuna ine, awa alekeni azipita,”  kuti mawu amene iye ananena akwaniritsidwe, akuti: “Mwa onse amene munandipatsa sindinatayepo ngakhale mmodzi.”+ 10  Pamenepo Simoni Petulo, popeza anali ndi lupanga, analisolola ndi kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe ndi kuduliratu khutu lake lakumanja.+ Dzina la kapoloyo anali Makasi. 11  Koma Yesu anauza Petulo kuti: “Bwezera lupangalo m’chimake.+ Kodi sindiyenera kumwa za m’kapu imene Atate wandipatsa,+ zivute zitani?” 12  Pamenepo gulu la asilikali lija, mkulu wa asilikali ndi alonda a Ayuda anagwira Yesu ndi kumumanga. 13  Choyamba anapita naye kwa Anasi, pakuti anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho.+ 14  Kayafa ameneyu ndi amene analangiza Ayuda uja kuti kunali kopindulitsa kwa iwo kuti munthu mmodzi afere anthu onse.+ 15  Tsopano Simoni Petulo ndiponso wophunzira wina anali kutsatira Yesu.+ Wophunzira winayu anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe, chotero analowa pamodzi ndi Yesu m’bwalo lamkati kunyumba ya mkulu wa ansembe. 16  Koma Petulo anaimirira kunja pakhomo.+ Choncho wophunzira winayu, amene anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe uja, anapita kukalankhula ndi mlonda wa pakhomo ndipo analowetsa Petulo. 17  Pamenepo mtsikana wantchito, amene anali mlonda wa pakhomopo, anafunsa Petulo kuti: “Kodi inunso si inu mmodzi wa ophunzira a munthu ameneyu?” Iye anati: “Ayi si ine.”+ 18  Akapolo ndi alonda anali ataima chapomwepo, pakuti anali atakoleza moto wamakala,+ chifukwa kunali kuzizira ndipo anali kuwotha motowo. Nayenso Petulo anaimirira pamodzi ndi iwo n’kumawotha nawo. 19  Ndiyeno wansembe wamkulu uja anafunsa Yesu za ophunzira ake ndi za chiphunzitso chake. 20  Yesu anamuyankha kuti: “Ndalankhula poyera ku dzikoli. Nthawi zonse ndinali kuphunzitsa m’masunagoge ndi m’kachisi,+ kumene Ayuda onse anali kusonkhana, ndipo sindinalankhule kanthu mseri. 21  N’chifukwa chiyani mukufunsa ine? Funsani amene anamva zimene ndinali kunena kwa iwo. Onani! Onsewa akudziwa zimene ndinali kunena.” 22  Atanena zimenezi, mmodzi wa alonda amene anaimirira chapafupi anamenya Yesu mbama,+ ndi kunena kuti: “Ungamuyankhe choncho wansembe wamkulu?” 23  Yesu anamuyankha kuti: “Ngati ndalankhula molakwika, pereka umboni wa cholakwikacho. Koma ngati ndalankhula moyenera, n’chifukwa chiyani ukundimenya?” 24  Kenako Anasi anatumiza Yesu ali womangidwa kwa Kayafa mkulu wa ansembe.+ 25  Pa nthawiyi Simoni Petulo anali ataimirira akuwotha moto. Pamenepo iwo anamufunsa kuti: “Kodi iwenso si iwe mmodzi wa ophunzira ake?” Iye anakana n’kunena kuti: “Ayi si ine.”+ 26  Mmodzi wa akapolo a mkulu wa ansembe, amenenso anali wachibale wa munthu amene Petulo anamudula khutu uja,+ anati: “Ndinakuona iwe m’munda muja uli naye limodzi, ndikunama kapena?” 27  Koma Petulo anakananso. Nthawi yomweyo tambala analira.+ 28  Ndiyeno iwo anatenga Yesu kuchoka kwa Kayafako ndi kupita naye kunyumba ya bwanamkubwa.+ Umenewu unali m’mawa kwambiri. Koma iwo sanalowe m’nyumba ya bwanamkubwayo poopa kuipitsidwa.+ Iwo anali kufuna kuti akathe kudya pasika. 29  Choncho Pilato anatuluka ndi kuwafunsa kuti: “Kodi mukumuimba mlandu wanji munthu ameneyu?”+ 30  Iwo anayankha kuti: “Munthu uyu akanakhala wosachita zoipa, sitikanabwera naye kwa inu.” 31  Pamenepo Pilato anati: “M’tengeni eniakenu mukamuweruze mogwirizana ndi chilamulo chanu.”+ Ayudawo anati: “N’zosaloleka kwa ife kupha munthu aliyense.”+ 32  Zinali choncho kuti mawu a Yesu akwaniritsidwe. Mawuwo anawanena pofuna kusonyeza mtundu wa imfa imene iye amayembekezeka kufa.+ 33  Choncho Pilato analowanso m’nyumba ya bwanamkubwa n’kuitana Yesu ndi kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?”+ 34  Yesu anayankha kuti: “Kodi zimenezi mukunena nokha, kapena ena akuuzani za ine?”+ 35  Pilato anayankha kuti: “Kodi ine ndine Myuda ngati? Anthu a mtundu wako omwe ndi ansembe aakulu ndi amene akupereka kwa ine.+ Kodi unachita chiyani?” 36  Yesu anayankha kuti:+ “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.+ Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo+ kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.” 37  Pamenepo Pilato anati: “Chabwino, koma kodi ndiwe mfumu?” Yesu anayankha kuti: “Mukunena nokha kuti ndine mfumu.+ Chimene ndinabadwira, ndiponso chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi.+ Aliyense amene ali kumbali ya choonadi+ amamvera mawu anga.”+ 38  Pilato anafunsa kuti: “Choonadi n’chiyani?” Atangofunsa funso limeneli, anatuluka ndi kupitanso kumene kunali Ayuda kuja, ndi kuwauza kuti: “Ineyo sindikupeza cholakwa chilichonse mwa munthu ameneyu.+ 39  Pajanso inu muli ndi mwambo wakuti ndizikumasulirani munthu mmodzi pa pasika.+ Kodi mukufuna ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?” 40  Pamenepo iwo anafuulanso kuti: “Ameneyo ayi, koma Baraba!” Koma Baraba ameneyu anali wachifwamba.+

Mawu a M'munsi