Yohane 16:1-33

16  “Ndalankhula zimenezi kwa inu kuti musapunthwe.+  Anthu adzakuchotsani m’sunagoge.+ Ndipo nthawi ikubwera pamene aliyense wakupha inu adzaganiza kuti wachita utumiki wopatulika kwa Mulungu.+  Koma adzachita zimenezi chifukwa sanadziwe Atate kapena ine.+  Ine ndalankhula zinthu zimenezi kwa inu, kuti nthawi yake ikadzafika, mudzakumbukire kuti ndinakuuzani zimenezi.+ “Zinthu izi sindinakuuzeni pa chiyambi pomwe, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu.  Koma tsopano ndikupita kwa amene anandituma,+ ndipo palibe aliyense wa inu amene akundifunsa kuti, ‘Mukupita kuti?’  Koma chifukwa ndalankhula zimenezi kwa inu, chisoni+ chadzaza m’mitima yanu.  Koma kunena zoona, ndikupita kuti inu mupindule. Pakuti ngati sindipita, ndiye kuti mthandizi+ uja sabwera kwa inu. Koma ndikapita, ndikamutumiza kwa inu.  Ndipo iye akadzafika adzapereka umboni wotsimikizika ku dzikoli wonena za tchimo, za chilungamo, ndi za chiweruzo.+  Koma choyamba adzapereka umboni wonena za tchimo,+ chifukwa iwo sakundikhulupirira.+ 10  Kenako adzapereka umboni wonena za chilungamo,+ chifukwa ine ndikupita kwa Atate ndipo inu simudzandionanso. 11  Pomaliza adzapereka umboni wonena za chiweruzo,+ chifukwa wolamulira wa dziko lino waweruzidwa.+ 12  “Ndili ndi zambiri zakuti ndikuuzeni, koma padakali pano simungathe kuzimvetsa zonsezo.+ 13  Koma mthandiziyo akadzafika, amene ndi mzimu wa choonadi,+ adzakutsogolerani m’choonadi chonse. Pakuti sadzalankhula zongoganiza mwa iye yekha, koma adzalankhula zimene wazimva, ndipo adzalengeza kwa inu zinthu zimene zikubwera.+ 14  Iyeyo adzandilemekeza,+ chifukwa adzalandira za ine ndipo adzazilengeza kwa inu.+ 15  Zonse zimene Atate ali nazo ndi zanga.+ N’chifukwa chake ndikunena kuti adzalandira za ine ndi kuzilengeza kwa inu. 16  Kwa kanthawi simudzandionanso,+ ndipo kwa kanthawi mudzandiona.” 17  Pamenepo ena mwa ophunzira akewo anayamba kufunsana kuti: “Kodi akutanthauza chiyani mmene akutiuza kuti, ‘Kwa kanthawi simudzandionanso, ndipo kwa kanthawi mudzandiona,’ ndi kuti, ‘chifukwa ndikupita kwa Atate’?” 18  Kwenikweni anali kunena kuti: “Kodi akutanthauza chiyani mmene akuti, ‘kwa kanthawi’? Sitikudziwa zimene akunena.” 19  Yesu anadziwa+ kuti akufuna kumufunsa, choncho iye anawafunsa kuti: “Kodi mukufunsana nokhanokha zimenezi, chifukwa ndanena kuti, Kwa kanthawi simudzandiona, ndipo kwa kanthawi mudzandiona? 20  Ndithudi ndikukuuzani, Mudzagwetsa misozi ndi kulira mofuula, koma dzikoli lidzasangalala. Mudzamva chisoni,+ koma chisoni chanu adzachisandutsa chimwemwe.+ 21  Pamene mayi akubereka amazunzika kwambiri, chifukwa nthawi yake yafika.+ Koma mwana akabadwa, sakumbukiranso kupweteka konse kuja chifukwa cha chimwemwe kuti munthu wabadwa padziko. 22  Choncho inunso muli ndi chisoni panopa. Koma ndidzakuonaninso, ndipo mitima yanu idzasangalala.+ Palibenso amene adzathetse chimwemwe chanu. 23  Pa tsiku limenelo+ simudzandifunsanso mafunso. Ndithudi ndikukuuzani, Ngati mupempha chilichonse+ kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.+ 24  Kufikira nthawi ino simunapemphepo chilichonse m’dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chisefukire.+ 25  “Ndalankhula zimenezi kwa inu m’mafanizo.+ Nthawi ikubwera pamene sindidzalankhulanso ndi inu m’mafanizo, koma ndidzakuuzani za Atate m’njira yosavuta kumva. 26  Pa tsikulo mudzapempha m’dzina langa, sindikunena kuti ndidzakupempherani kwa Atate ayi. 27  Pakuti Atateyo amakukondani, chifukwa munandikonda+ ine ndipo mwakhulupirira kuti ine ndinabwera monga nthumwi ya Atate.+ 28  Ndinachokera kwa Atate ndipo ndinabwera m’dziko. Tsopano ndikuchoka m’dziko kupita kwa Atate.”+ 29  Ophunzira akewo anati: “Eya! Tsopano mukulankhula m’njira yosavuta kumva, ndipo simukulankhulanso mwa mafanizo. 30  Tadziwa tsopano kuti inu mukudziwa zonse+ ndipo m’posafunikanso kuti munthu akufunseni mafunso.+ Pa chifukwa chimenechi tikukhulupirira kuti munachokeradi kwa Mulungu.”+ 31  Yesu anawayankha kuti: “Kodi panopa mukukhulupirira? 32  Taonani! Nthawi ikubwera, ndipo yafika kale. Mubalalika aliyense kupita kunyumba kwake,+ ndipo mundisiya ndekha. Koma sindikhala ndekha, chifukwa Atate ali ndi ine.+ 33  Ndanena zimenezi kwa inu kuti mukhale mu mtendere chifukwa cha ine.+ M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.”+

Mawu a M'munsi