Yohane 13:1-38
13 Tsopano Yesu anadziwiratu chikondwerero cha pasika chisanafike, kuti nthawi yake yochoka m’dzikoli kupita kwa Atate+ yakwana.+ Ndipo popeza kuti anali kuwakonda akewo amene anali m’dzikoli,+ anawakonda mpaka pa mapeto a moyo wake.
2 Chakudya chamadzulo chili mkati, Mdyerekezi anali ataika kale maganizo ofuna kupereka Yesu+ mumtima mwa Yudasi Isikariyoti,+ mwana wa Simoni.
3 Yesu anali kudziwa kuti Atate anapereka zinthu zonse m’manja mwake.+ Analinso kudziwa kuti anabwera kuchokera kwa Mulungu ndi kuti anali kupita kwa Mulungu.+
4 Choncho anaimirira pa chakudya chamadzulocho ndi kuvula malaya ake akunja. Kenako anatenga thaulo ndi kumanga m’chiuno mwake.+
5 Atatero anathira madzi m’beseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi+ a ophunzira ndi kuwapukuta ndi thaulo limene anamanga m’chiuno lija.
6 Kenako anafika pa Simoni Petulo. Koma Petulo anauza Yesu kuti: “Ambuye, inuyo mukufuna musambitse mapazi anga?”+
7 Yesu anayankha kuti: “Zimene ndikuchitazi sungazimvetse padakali pano, koma pambuyo pake udzamvetsa.”+
8 Petulo anati: “Ndithu, sizitheka kuti inu musambitse mapazi anga.” Yesu anamuyankha kuti: “Ndikapanda kukusambitsa,+ palibe chako kwa ine.”
9 Simoni Petulo anati: “Ambuye, musandisambitse mapazi okha, komanso manja ndi mutu womwe.”
10 Yesu anati: “Amene wasamba m’thupi+ amangofunika kusamba mapazi okha basi, chifukwa thupi lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, koma osati nonsenu.”
11 Iye anadziwa ndithu za munthu amene wakonza zomupereka.+ N’chifukwa chake ananena kuti: “Sikuti nonsenu ndinu oyera ayi.”
12 Tsopano atasambitsa mapazi awo ndi kuvalanso malaya ake akunja aja, anakhalanso patebulo. Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi mukudziwa zimene ndachita kwa inu?
13 Inu mumanditcha kuti ‘Mphunzitsi’+ ndi ‘Ambuye,’+ mumalondola, pakuti ndinedi.+
14 Choncho ngati ine, wokhala Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu,+ inunso muyenera kusambitsana mapazi.+
15 Pakuti ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.+
16 Ndithudi ndikukuuzani, Kapolo saposa mbuye wake, ndiponso wotumidwa saposa amene wamutuma.+
17 Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.+
18 Sindikunena nonsenu, ndikudziwa amene ndawasankha.+ Koma zili choncho kuti Malemba akwaniritsidwe,+ paja amati, ‘Munthu amene anali kudya chakudya changa wanyamula chidendene chake kundiukira.’+
19 Kuyambira tsopano ndikukuuziranitu zisanachitike,+ kuti zikadzachitika mudzakhulupirire kuti ine ndinedi amene munali kumuyembekezera uja.
20 Ndithudi ndikukuuzani, Wolandira aliyense amene ine ndamutuma walandiranso ine.+ Ndipo amene walandira ine, walandiranso amene anandituma.”+
21 Atanena zimenezi, Yesu anasautsika mu mzimu, ndipo anachitira umboni kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mmodzi wa inu andipereka.”+
22 Ophunzirawo anayamba kuyang’anizana posadziwa kuti anali kunena ndani.+
23 Mmodzi wa ophunzira ake amene Yesu anali kumukonda,+ anakhala patsogolo pa Yesu, pachifuwa chake.
24 Chotero Simoni Petulo anamukodola ndi mutu ndi kumuuza kuti: “Tiuze kuti akunena ndani.”
25 Pamenepo winayo anatsamira pachifuwa pa Yesu ndi kumufunsa kuti: “Ambuye, mukunena ndani?”+
26 Yesu anayankha kuti: “Ndi amene ndimupatse chidutswa cha mkate chimene ndisunse.”+ Choncho atasunsa chidutswa cha mkate chija, anapatsa Yudasi, mwana wa Simoni Isikariyoti.
27 Atamupatsa chidutswa cha mkatecho, pamenepo Satana analowa mwa Yudasi.+ Chotero Yesu anamuuza kuti: “Zimene wakonza kuchita, zichite mwamsanga.”
28 Koma panalibe aliyense mwa okhala patebulowo amene anadziwa chifukwa chimene anamuuzira zimenezi.
29 Popeza kuti Yudasi anali kusunga bokosi la ndalama,+ ena anali kuganiza kuti Yesu anali kumuuza kuti: “Ugule zofunikira zonse za chikondwerero,” kapena kuti apereke kenakake kwa osauka.+
30 Choncho atalandira chidutswa cha mkate chija, anatuluka nthawi yomweyo. Umenewu unali usiku.+
31 Yudasi atatuluka, Yesu anati: “Tsopano Mwana wa munthu walemekezedwa,+ ndipo Mulungu walemekezedwa kudzera mwa iye.
32 Mulungunso payekha amulemekeza iye,+ ndipo amulemekeza nthawi yomwe ino.
33 Ana apamtima inu,+ ndikhala nanu kanthawi kochepa chabe. Mudzandifunafuna, ndipo monga ndinauzira Ayuda aja kuti, ‘Kumene ine ndikupita simungathe kukafikako,’+ tsopano ndikuuzanso inuyo.
34 Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani,+ inunso muzikondana.+
35 Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”+
36 Simoni Petulo anafunsa kuti: “Ambuye, mukupita kuti?” Yesu anayankha kuti: “Kumene ndikupita sunganditsatire padakali pano, koma udzanditsatira m’tsogolo.”+
37 Petulo anafunsanso kuti: “Ambuye, n’chifukwa chiyani sindingakutsatireni padakali pano? Ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha inu.”+
38 Yesu anayankha kuti: “Kodi udzapereka moyo wako chifukwa cha ine? Ndithudi ndikukuuza iwe, Tambala asanalire undikana katatu.”+