Yohane 12:1-50

12  Kutangotsala masiku 6 kuti pasika ayambike, Yesu anafika ku Betaniya+ kumene kunali Lazaro,+ uja amene Yesu anamuukitsa kwa akufa.  Choncho anamukonzera chakudya chamadzulo kumeneko, ndipo Marita+ anali kutumikira.+ Lazaro anali mmodzi wa anthu amene anali kudya naye.+  Pamenepo Mariya anatenga mafuta onunkhira. Mafutawa anali nado+ weniweni, okwera mtengo kwambiri okwana magalamu 327. Mariya anathira mafutawo pamapazi a Yesu ndi kupukuta mapaziwo ndi tsitsi lake.+ M’nyumba monsemo munangoti guu kafungo kabwino ka mafutawo.  Koma Yudasi Isikariyoti,+ mmodzi wa ophunzira ake, amene anali pafupi kumupereka anati:  “N’chifukwa chiyani mafuta onunkhirawa+ sanagulitsidwe madinari 300 ndi kupereka ndalamazo kwa anthu osauka?”+  Koma iye ponena izi sikuti anali kudera nkhawa osauka ayi, koma chifukwa anali wakuba.+ Iye anali wosunga bokosi la ndalama,+ ndipo anali kutengamo ndalama zimene zinali kuponyedwa m’bokosilo.  Choncho Yesu anati: “M’lekeni, achite mwambo umenewu pokonzekera tsiku limene ndidzaikidwe m’manda.+  Pakuti osaukawo+ muli nawo nthawi zonse, koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.”  Tsopano khamu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti Yesu ali kumeneko. Choncho linafika, osati chifukwa cha Yesu yekha ayi, komanso kuti lidzaone Lazaro, amene iye anamuukitsa kwa akufa.+ 10  Pamenepo ansembe aakulu anasonkhana pamodzi ndi kupangana zakuti aphenso Lazaro,+ 11  chifukwa Ayuda ambiri anali kupita kumeneko ndi kukhulupirira Yesu chifukwa cha Lazaroyo.+ 12  Tsiku lotsatira, khamu lalikulu la anthu amene anabwera ku chikondwererocho, atamva kuti Yesu akubwera ku Yerusalemuko, 13  anatenga nthambi za kanjedza+ ndi kutuluka kukamuchingamira. Ndipo anayamba kufuula kuti:+ “M’pulumutseni!+ Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova,+ amenenso ndi mfumu+ ya Isiraeli!” 14  Koma pamene Yesu anapeza bulu wamng’ono,+ anakwera pa iye monga mmene Malemba amanenera kuti: 15  “Usaope mwana wamkazi wa Ziyoni. Taona! Mfumu yako ikubwera.+ Ikubwera itakwera bulu wamng’ono wamphongo.”+ 16  Poyamba ophunzira akewo sanazindikire zimenezi.+ Koma pamene Yesu analandira ulemerero,+ iwo anakumbukira kuti zimenezi zinalembedwa ponena za iye. Anakumbukiranso kuti anamuchitira zimenezi.+ 17  Tsopano anthu ambiri amene analipo pamene iye anaitana Lazaro+ kuti atuluke m’manda achikumbutso ndi kumuukitsa, anali kumuchitira umboni.+ 18  Pa chifukwa chimenechi, anthu onsewo anamuchingamira, chifukwa anamva kuti anachita chizindikiro+ chimenechi. 19  Pamenepo Afarisi+ anayamba kuuzana kuti: “Apa ndiye mukudzionera nokha kuti palibiretu chimene tikuphulapo. Onani! Dziko lonse lakhamukira kwa iye.”+ 20  Pakati pa obwera kudzalambira ku chikondwereroko panalinso Agiriki.+ 21  Amenewa anafika kwa Filipo+ wa ku Betsaida ku Galileya, ndipo anayamba kumupempha kuti: “Bambo, ife tikufuna kuona Yesu.”+ 22  Filipo anapita kukauza Andireya zimenezo. Andireya ndi Filipo anapita kukauza Yesu. 23  Koma Yesu anawayankha kuti: “Nthawi yafika yakuti Mwana wa munthu alemekezedwe.+ 24  Ndithudi ndikukuuzani, Kambewu ka tirigu kakapanda kugwa m’nthaka ndi kufa, kamakhalabe kamodzi komweko. Koma kakafa,+ kamadzabala zipatso zambiri. 25  Aliyense wokonda moyo wake akuuwononga, koma wodana ndi moyo wake+ m’dziko lino akuusungira moyo wosatha.+ 26  Ngati munthu wafuna kunditumikira ine, anditsatire, ndipo kumene ine ndidzakhala, mtumiki wanga adzakhalanso komweko.+ Aliyense wonditumikira ine, Atate adzamulemekeza.+ 27  Moyo wanga ukusautsika tsopano,+ ndinene chiyani kodi? Atate ndipulumutseni ku nthawi yosautsayi.+ Komabe nthawi imeneyi iyenera kundifikira pakuti ndiye chifukwa chake ndinabwera. 28  Atate lemekezani dzina lanu.” Pamenepo mawu+ anamveka kuchokera kumwamba kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”+ 29  Chotero khamu la anthu amene anali ataimirira pamenepo ndi kumva zimenezi anayamba kunena kuti kwagunda bingu. Ena anayamba kunena kuti: “Mngelo walankhula naye.” 30  Poyankha Yesu anati: “Sikuti mawu amenewa amveka chifukwa cha ine ayi, koma chifukwa cha inu.+ 31  Tsopano dziko ili likuweruzidwa, wolamulira wa dzikoli+ aponyedwa kunja tsopano.+ 32  Koma ine ndikadzakwezedwa+ m’mwamba padziko lapansi, ndidzakokera anthu osiyanasiyana kwa ine.”+ 33  Kwenikweni ananena izi pofuna kusonyeza mtundu wa imfa imene anali pafupi kufa.+ 34  Pamenepo khamu la anthulo linamuyankha kuti: “Ife tinamva m’Chilamulo kuti Khristu adzakhala kosatha.+ Nanga inu mukunena bwanji kuti Mwana wa munthu adzakwezedwa m’mwamba?+ Kodi Mwana wa munthu ameneyo ndani?”+ 35  Pamenepo Yesu anati: “Kuwala kukhalabe pakati panu kanthawi pang’ono. Yendani pamene kuwalako mudakali nako, kuti mdima+ usakugwereni, pakuti woyenda mu mdima sadziwa kumene akupita.+ 36  Pamene kuwala mudakali nako, sonyezani chikhulupiriro mwa kuwalako, kuti mukhale ana ake a kuwala.”+ Yesu atanena zimenezi, anachoka ndi kuwabisalira. 37  Koma ngakhale kuti anachita zizindikiro zambiri pamaso pawo, iwo sanali kukhulupirira iye, 38  moti mawu a mneneri Yesaya anakwaniritsidwa. Iye anati: “Yehova,* kodi ndani wakhulupirira zimene ife tamva?+ Ndipo kodi dzanja la Yehova laonetsedwa kwa ndani?”+ 39  Chifukwa chimene sanakhulupirire n’chimenenso Yesaya ananena kuti: 40  “Wachititsa khungu maso awo ndipo waumitsa mitima yawo,+ kuti asamaone ndi maso awowo, asazindikire ndi mitima yawo ndi kutembenuka kuti ine ndiwachiritse.”+ 41  Yesaya ananena zimenezi chifukwa anaona ulemerero wa Khristu,+ ndipo ananena za iye. 42  Komabe ambiri, ngakhalenso olamulira anamukhulupirira,+ koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze poyera, poopa kuti angawachotse musunagoge.+ 43  Pakuti anakonda kwambiri ulemerero wa anthu kuposa ulemerero wa Mulungu.+ 44  Koma Yesu anafuula kuti: “Wokhulupirira ine sakhulupirira ine ndekha, komanso amakhulupirira iye amene anandituma ine.+ 45  Amene wandiona ine waonanso amene anandituma.+ 46  Ndabwera monga kuwala m’dziko,+ kuti aliyense wokhulupirira ine asapitirize kukhala mumdima.+ 47  Ngati munthu wamva mawu anga koma osawasunga, ine sindiweruza woteroyo, pakuti sindinabwere kudzaweruza dziko,+ koma kudzalipulumutsa.+ 48  Aliyense wondinyalanyaza ndi kusalandira mawu anga, ali naye mmodzi womuweruza. Mawu+ amene ine ndalankhula ndi amene adzamuweruze pa tsiku lomaliza. 49  Chifukwa sindinalankhulepo zongoganiza pandekha, koma Atate amene ananditumawo anandipatsa lamulo pa zimene ndiyenera kunena ndi zimene ndiyenera kulankhula.+ 50  Komanso ndikudziwa kuti lamulo lake limatanthauza moyo wosatha.+ Choncho zimene ndimalankhula, monga mmene Atate anandiuzira, ndimazilankhula momwemo.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.