Yohane 11:1-57

11  Tsopano panali munthu wina amene anali kudwala, dzina lake Lazaro. Anali wa m’mudzi wa Betaniya, kwawo kwa Mariya ndi m’bale wake Marita.+  Mariyayu ndi yemwe uja amene anathira Ambuye mafuta onunkhira+ ndi kupukuta mapazi awo ndi tsitsi lake.+ Lazaro amene anali kudwalayu anali mlongo wake.  Choncho alongo akewo anatumiza uthenga kwa Yesu, kuti: “Ambuye! amene mumamukonda+ uja akudwala.”  Koma Yesu atamva zimenezi ananena kuti: “Kudwala kumeneku si kwa imfa chabe, koma n’kopatsa Mulungu ulemerero,+ kuti mwa kudwalako, Mwana wa Mulungu alemekezeke.”  Yesu anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro.  Koma atamva kuti Lazaro akudwala, anakhalabe masiku awiri kumalo kumene iye anali.  Pambuyo pake anauza ophunzira ake kuti: “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.”  Ophunzirawo anati: “Rabi,+ posachedwapa Ayudeya anafuna kukuponyani miyala,+ ndiye mukufuna kupitanso komweko kodi?”  Yesu anayankha kuti: “Kodi usana suli ndi maola 12? Munthu akayenda masana+ palibe chimamupunthwitsa, chifukwa amaona kuwala kwa dzikoli. 10  Koma munthu akayenda usiku,+ amapunthwa pa chinachake chifukwa mwa iye mulibe kuwala.” 11  Atanena zimenezi, kenako anauza ophunzira akewo kuti: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa ku tulo take.”+ 12  Pamenepo ophunzirawo anati: “Ambuye, ngati iye akupumula, apeza bwino.” 13  Apa Yesu anali kunena za imfa yake. Koma iwo anaganiza kuti anali kunena za kugona tulo teniteni. 14  Choncho, Yesu tsopano anawauza momveka bwino kuti: “Lazaro wamwalira,+ 15  ndipo ine ndikukondwera chifukwa cha inu kuti sindinali kumeneko, kuti inu mukhulupirire. Tsopano tiyeni tipite kwa iye.” 16  Choncho Tomasi, wotchedwa Didimo, anauza ophunzira anzakewo kuti: “Ifenso tiyeni tipite, kuti tikafere naye limodzi.”+ 17  Tsopano Yesu atafika kumeneko, anapeza kuti Lazaro wakhala kale m’manda achikumbutso masiku anayi.+ 18  Mzinda wa Betaniya unali pafupi ndi Yerusalemu pa mtunda wa makilomita pafupifupi atatu. 19  Tsopano Ayuda ambiri anabwera kwa Marita ndi Mariya kudzawatonthoza+ chifukwa cha imfa ya mlongo wawo. 20  Choncho Marita atamva kuti Yesu akubwera, anakamuchingamira, koma Mariya+ anakhalabe kunyumba. 21  Marita anauza Yesu kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.+ 22  Komabe, ngakhale tsopano ndikudziwa kuti zilizonse zimene mungapemphe Mulungu,+ Mulungu adzakupatsani zonsezo.” 23  Yesu anamuuza kuti: “Mlongo wako adzauka.”+ 24  Marita anati: “Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa+ m’tsiku lomaliza.” 25  Pamenepo Yesu anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo.+ Aliyense wokhulupirira mwa ine, ngakhale amwalire, adzakhalanso ndi moyo.+ 26  Ndipo aliyense amene ali moyo ndi kukhulupirira mwa ine sadzafa ayi.+ Kodi ukukhulupirira zimenezi?” 27  Iye anayankha kuti: “Inde, Ambuye. Ndimakhulupirira kuti ndinu Khristu Mwana wa Mulungu, Amene dziko linali kuyembekezera kubwera kwake.”+ 28  Pamene ananena zimenezi, anapita kukaitana m’bale wake Mariya ndi kumuuza mseri kuti: “Mphunzitsi+ ali pano ndipo akukuitana.” 29  Mariya atamva zimenezo, ananyamuka mwamsanga kupita kumene iye anali. 30  Pa nthawiyi n’kuti Yesu asanalowe kwenikweni m’mudzimo. Anali adakali kumalo kumene Marita anakumana naye. 31  Choncho Ayuda amene anali naye pamodzi m’nyumbamo,+ amene anali kumutonthoza, ataona Mariya akunyamuka mofulumira ndi kutuluka kunja, anamutsatira. Anali kuganiza kuti akupita kumanda achikumbutso+ kukalira kumeneko. 32  Tsopano Mariya atafika kumene kunali Yesu kuja ndi kumuona, anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi pafupi ndi mapazi a Yesu. Kenako anamuuza kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.”+ 33  Ndipo Yesu atamuona akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye pamodzi akuliranso, anadzuma povutika mumtima ndi kumva chisoni.+ 34  Kenako anafunsa kuti: “Mwamuika kuti?” Iwo anati: “Ambuye tiyeni mukaone.” 35  Yesu anagwetsa misozi.+ 36  Pamenepo Ayudawo anayamba kunena kuti: “Taonani, anali kumukondadi kwambiri!”+ 37  Koma ena mwa iwo anati: “Kodi iyeyu, amene anatsegula maso+ a munthu wakhungu uja, sakanatha kuchitapo kanthu kuti mnzakeyu asamwalire?” 38  Koma Yesu atadzumanso movutika mtima, anafika kumanda achikumbutsowo.+ Kwenikweni linali phanga, ndipo analitseka ndi chimwala.+ 39  Yesu anati: “Chotsani chimwalachi.”+ Marita, mlongo wa womwalirayo anauza Yesu kuti: “Ambuye, pano ayenera kuti wayamba kununkha, pakuti lero ndi tsiku lachinayi chimuikireni m’manda.” 40  Yesu anati: “Kodi sindinakuuze kuti ngati ukhulupirira udzaona ulemerero wa Mulungu?”+ 41  Pamenepo anachotsa chimwalacho. Tsopano Yesu anakweza maso ake kumwamba+ ndi kunena kuti: “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva.+ 42  Inde, ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse, koma ndikunena izi chifukwa cha khamu la anthu+ aimirira panowa, kuti akhulupirire kuti inu munandituma ine.”+ 43  Atanena zimenezi, anafuula mokweza mawu kuti: “Lazaro, tuluka!”+ 44  Amene anali wakufa uja anatuluka. Mapazi ndi manja ake anali okulungidwa ndi nsalu zamaliro,+ nkhope yakenso inali yomanga ndi nsalu. Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “M’masuleni ndi kumuleka apite.” 45  Pamenepo Ayuda ambiri amene anabwera kwa Mariya ndi kuona zimene Yesu anachitazo anakhulupirira mwa iye.+ 46  Ena a iwo anapita kwa Afarisi ndi kukawauza zimene Yesu wachita.+ 47  Zitatero ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa Khoti Lalikulu la Ayuda*+ ndi kunena kuti: “Kodi tichite chiyani pamenepa, chifukwa munthu uyu akuchita zizindikiro zochuluka?+ 48  Ngati timulekerera, onse adzakhulupirira mwa iye,+ ndipo Aroma+ adzabwera kudzatenga malo athu+ ndi mtundu wathu.” 49  Koma mmodzi wa iwo, Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho,+ anati: “Palibe chimene mukudziwa inu, 50  ndipo simukuona kuti n’kopindulitsa kwa inu kuti munthu mmodzi afere+ anthu onse, kuti mtundu wonse usawonongeke.”+ 51  Zimene ananenazi, kwenikweni sanaziganize mwa iye yekha, koma chifukwa anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho, ananenera kuti Yesu adzafera mtunduwo. 52  Ndipo osati kufera mtundu chabe, komanso kuti asonkhanitse pamodzi+ ana a Mulungu obalalika.+ 53  Choncho kuyambira tsiku limenelo anapangana kuti amuphe.+ 54  Pa chifukwa chimenechi, Yesu sanalinso kuyendayenda moonekera+ kwa Ayuda.+ Koma anachoka kumeneko ndi kupita kudera lina lapafupi ndi chipululu, mumzinda wotchedwa Efuraimu.+ Ndipo anakhala kumeneko pamodzi ndi ophunzira ake. 55  Tsopano pasika+ wa Ayuda anali pafupi, ndipo anthu ochuluka anachoka m’midzi ndi kupita ku Yerusalemu pasikayo asanafike, kuti akachite mwambo wa kudziyeretsa.+ 56  Choncho iwo anayamba kufunafuna Yesu ndipo anali kuima pamalo amodzi m’kachisimo ndi kuyamba kukambirana kuti: “Mukuganiza bwanji? Kodi iye uja sabwera ku chikondwererochi?” 57  Apa n’kuti ansembe aakulu ndi Afarisi atalamula kuti aliyense amene angadziwe kumene kuli Yesu, aulule kuti iwo akamugwire.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”