Yobu 9:1-35

9  Tsopano Yobu anayankha kuti:   “Ndikudziwa bwino kuti zili choncho.Koma kodi munthu angakhale bwanji wosalakwa pa mlandu wotsutsana ndi Mulungu?+   Ngati Mulunguyo akufuna kutsutsana naye,+Munthuyo sangamuyankhe n’kamodzi komwe pamafunso 1,000.   Iye ali ndi mtima wanzeru ndiponso mphamvu zambiri.+Ndani angachite naye makani,* koma osavulala?+   Iye amasuntha mapiri,+ anthu osadziwa n’komwe.Amawachotsa chifukwa cha mkwiyo.+   Amachititsa dziko lapansi kunjenjemera pamalo ake,Mwakuti zipilala+ zake zimagwedezeka.   Amauza dzuwa kuti lisawale,Ndipo amaphimba nyenyezi.+   Kumwamba anakutambasula yekha,+Ndipo amayenda pamafunde aatali a m’nyanja.+   Anapanga gulu la nyenyezi la Asi, gulu la nyenyezi la Kesili,Gulu la nyenyezi la Kima+ ndi zipinda zamkati za Kum’mwera. 10  Amachita zinthu zazikulu ndi zosatheka kuzifufuza,+Ndiponso zinthu zodabwitsa zosawerengeka.+ 11  Iyetu amadutsa pafupi nane koma ine osamuona,Amandipitirira koma ine osamuzindikira.+ 12  Ndithu iye amalanda. Ndani angamuletse?Ndani angamufunse kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+ 13  Mulungu sadzabweza mkwiyo wake.+Anthu othandiza munthu wachiwawa+ amagwa pansi pa mapazi ake. 14  N’chifukwa chake ndikamamuyankha,Ndiyenera kusankha bwino mawu anga.+ 15  Choncho, sindingamuyankhe ngakhale nditakhala kuti ndikunena zoona.+Ndingachonderere amene akutsutsana nane pa mlandu.+ 16  Nditamuitana, kodi angandiyankhe?+Sindikukhulupirira kuti angandimvetsere. 17  Iye amene wandikantha ndi mavuto onga mphepo yamkuntho,Wachulukitsa zilonda zanga popanda chifukwa.+ 18  Sadzalola kuti ndipumeko mpweya wabwino,+Chifukwa akungondikhuthulira zinthu zowawa. 19  Ngati kuli wamphamvu kwambiri, ndi iyeyo.+Ngati pali wolimbikitsa chilungamo, ndikufuna andiitane. 20  Ndikanakhala kuti ndikulondola, pakamwa panga pomwe pakanandinena kuti ndine wolakwa.Ndikanakhala wosalakwa, iye akanandinena kuti ndine wachinyengo. 21  Ngakhale ndikanakhala wosalakwa, sindikanadziwa zimenezo,Ndipo ndikanakana moyo wanga. 22  N’chifukwa chake ndikunena kuti zonsezo mfundo yake ndi imodzi, yakuti:‘Iye amapha osalakwa komanso oipa.’+ 23  Anthu atati afe mwadzidzidzi chifukwa cha kusefukira kwa madzi,Iye angaseke anthu osalakwa akuvutika. 24  Dziko lapansi laperekedwa m’manja mwa woipa.+Iye amaphimba nkhope za oweruza ake.Ngati si iyeyo, ndiye ndi ndani? 25  Komanso masiku anga akufulumira kwambiri kuposa munthu wothamanga.+Iwo athawa ndipo ndithu sadzaona zabwino. 26  Ayenda ngati ngalawa za bango,Ngati chiwombankhanga chimene chimauluka uku ndi uko pofunafuna chakudya.+ 27  Ngati ndanena kuti, ‘Ndiiwale nkhawa zanga,+Ndisinthe maonekedwe anga+ ndi kusangalala,’ 28  Ndachita mantha ndi zopweteka zanga zonse.+Ndikudziwa kuti mundiona kuti ndine wolakwa. 29  Ndithu ndidzapezeka kuti ndine wolakwa.N’chifukwa chiyani ndikuvutika pachabe?+ 30  Nditati ndisambe madzi a chipale chofewa,Ndi kusamba m’manja ndi sopo,+ 31  Inuyo mungandiviike m’dzenje,Ndipo zovala zanga zinganyansidwe nane ndithu. 32  Pakuti iye si munthu+ ngati ine kuti ndimuyankhe,Kapena kuti tizengane mlandu. 33  Palibe munthu woti agamule mlandu wathu,+Woti akhale woweruza wathu. 34  Iye achotse ndodo yake pa ine,+Ndipo kuopsa kwake kusandichititse mantha. 35  Ndilankhule ndipo ndisachite naye mantha,Chifukwa ine sindiopa kulankhula naye.

Mawu a M'munsi

Ena amati “nthota.”