Yobu 7:1-21
7 “Kodi si paja munthu amagwira ntchito yokakamiza+ padziko lapansi?Ndipo kodi masiku ake sali ngati masiku a munthu waganyu?+
2 Monga kapolo, iye amakhala wefuwefu kufunafuna mthunzi,+Ndipo ngati munthu waganyu, amadikirira malipiro ake.+
3 Chotero ndalandira miyezi yachabechabe ngati cholowa,+Ndipo kuvutika usiku uliwonse+ ndiwo malipiro anga.
4 Ndikagona ndimanena kuti, ‘Kodi ndidzuka nthawi yanji?’+Kukada ndimangokhalira kutembenukatembenuka mpaka m’mawa kuli mbuu.
5 Mnofu wanga wakutidwa ndi mphutsi+ ndipo wamatirira fumbi,+Khungu langa lang’ambika n’kumatuluka mafinya.+
6 Masiku anga akufulumira+ kuposa mmene chimathamangira chowombera nsalu,Iwo afika pamapeto popanda chiyembekezo.+
7 Kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mphepo,+Ndiponso kuti diso langa silidzaonanso zabwino.
8 Diso la iye amene amandiona silidzandionanso,Maso anu adzandiyang’ana, koma ine kudzakhala kulibe.+
9 Mtambo umafika kumapeto ake n’kutha.Chimodzimodzi ndi munthu amene wapita ku Manda,* sadzabwerako.+
10 Sadzabwereranso kunyumba yake,Ndipo anthu a pamalo ake sadzamuzindikiranso.+
11 Choncho, ine sinditseka pakamwa panga.Ndilankhula chifukwa cha kuvutika mumtima,+Ndilankhula za nkhawa zanga, chifukwa moyo wanga ukupweteka.
12 Kodi ine ndine nyanja, kapena chilombo cha m’nyanja,Kuti mundiikire mlonda?+
13 Ndikanena kuti, ‘Bedi langa linditonthoza,Bedi langa lindithandiza kusenza nkhawa zanga,’
14 Inuyo mumandiopseza ndi maloto,Ndipo mumandichititsa mantha ndi masomphenya.
15 Chotero moyo wanga wasankha kubanika,Wasankha imfa+ m’malo mwa mafupa angawa.
16 Moyo ndaukana,+ sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.*Ndisiyeni chifukwa masiku anga ndi ochepa kwambiri.+
17 Kodi munthu ndani+ kuti mumulere,Ndi kuti muzimuganizira?
18 Iye ndani kuti muzimuganizira m’mawa uliwonse,Ndi kuti muzimuyesa nthawi zonse?+
19 N’chifukwa chiyani simukusiya kundiyang’ana,+Kapena kundisiya kuti ndimezeko malovu?
20 Ngati ndachimwa, ndingakuchiteni chiyani Inu amene mumaonetsetsa anthu?+N’chifukwa chiyani mwalunjika ine, kuti ndikhale cholemetsa kwa inu?
21 N’chifukwa chiyani simukundikhululukira machimo anga,+Ndi kunyalanyaza zolakwa zanga?Pakuti tsopano ndigona m’fumbi.+Mudzandifunafuna koma ine kudzakhala kulibe.”