Yobu 6:1-30

6  Tsopano Yobu anayankha kuti:   “Zikanakhala bwino masautso anga+ onse akanayezedwa kulemera kwake,Ndiponso pa nthawi yomweyo mavuto anga akanaikidwa pasikelo.   Chifukwa panopa akulemera kuposa mchenga wam’nyanja.N’chifukwa chake ndalankhula zopanda pake.+   Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilasa,+Ndipo ine ndikumwa poizoni wa miviyo.+Zoopsa zochokera kwa Mulungu zasonkhana kuti zilimbane nane.+   Kodi mbidzi+ imalira ikudya msipu?Kapena ng’ombe yamphongo imalira ikudya chakudya chake?   Kodi chakudya chosakoma chingadyedwe chopanda mchere?Kapena kodi utomoni* wa zomera umakoma?   Moyo wanga wakana kukhudza zinthu zoterozo.Zili ngati matenda m’chakudya changa.   Zikanakhala bwino pempho langa likanayankhidwa,Ndiponso Mulungu akanandipatsa chiyembekezo.   Zikanakhala bwino Mulungu akanati angondiphwanya,Akanati atambasule dzanja lake n’kundipha.+ 10  Ngakhale zimenezo, bwenzi zili zonditonthoza.Ndikadadumpha ndi chisangalalo+ ngakhale kuti ndikumva ululu wosalekeza,Chifukwa sindinabise mawu+ a Woyerayo,+ ngakhale kuti iye sakanandichitira chisoni. 11  Kodi ndili ndi mphamvu zochuluka motani, kuti ndizidikirabe?+Ndipo kodi mapeto anga ndi otani, kuti ndipitirize kutalikitsa moyo wanga? 12  Kodi mphamvu zanga ndi mphamvu za miyala?Kapena kodi mnofu wanga ndi wamkuwa? 13  Ndilibenso mphamvu zodzithandizira,Ndipo sindingathenso kugwira ntchito bwinobwino. 14  Aliyense wosasonyeza mnzake kukoma mtima kosatha,+Adzasiyanso kuopa Wamphamvuyonse.+ 15  Ngakhale abale anga amene, achita zachinyengo+ ngati mtsinje woyenda nthawi yozizira,Ngati makwawa a mitsinje yoyenda nthawi yozizira, imene imauma. 16  Mitsinjeyo imakhala ndi madzi akuda chifukwa cha kusungunuka kwa madzi oundana,Ndipo chipale chofewa nachonso chimasungunukira momwemo. 17  Pa nyengo yake imakhala yopanda madzi,+ imakhala chete.Kukatentha, imauma.+ 18  Njira zawo zimakhala zokhotakhota.Mitsinjeyo imapita kumalo opanda kanthu, n’kutha. 19  Magulu a amtengatenga a ku Tema+ amaifunafuna,Asabeya+ apaulendo amaidikirira. 20  Amachita manyazi chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro,Amafika pamalowo n’kukhumudwa.+ 21  Mofanana ndi zimenezi, amuna inu mwakhala opanda pake,+Mwaona zoopsa n’kuyamba kuchita mantha.+ 22  Kodi ndinanena kuti, ‘Mundipatse kanthu,Kapena mutapeko pa chuma chanu n’kundiperekera mphatso? 23  Kapena mundipulumutse m’manja mwa mdani,+Ndi kundiwombola m’manja mwa anthu ankhanza?’+ 24  Mundilangize, ndipo ine ndikhala chete.+Zimene ndalakwitsa, mundidziwitse.+ 25  Mawu olungama, ndithu sapweteka.+Koma kodi kudzudzula kwanu kuli ndi phindu lanji?+ 26  Kodi mwapangana kuti mudzudzule mawu anga,Chonsecho mawu a munthu wopanda chiyembekezo+ amatengedwa ndi mphepo?+ 27  Inutu mukhoza kuchita maere kuti mutenge mwana wamasiye,+Ndipo mnzanu mukhoza kumugulitsa.+ 28  Tsopano tandimvetserani,Ndipo muone ngati ndilimbe mtima kukunamizani.+ 29  Chonde sinthani maganizo anu, kuti pachitike chilungamo.Ndithu sinthani maganizo. Inetu ndikadali wolungama.+ 30  Kodi palilime panga pali zosalungama?Kapena kodi m’kamwa mwanga simuzindikira mavuto?

Mawu a M'munsi

Ena amati “manthova,” kapena “mambidza.”