Yobu 5:1-27

5  “Taitana! Kodi pali aliyense amene akukuyankha?Ndipo kodi utembenukira kwa mngelo* uti?   Chifukwa wopusa, mkwiyo udzamupha,Ndipo nsanje ya munthu wosachedwa kukopeka idzamupha.   Ineyo ndaonapo wopusa akuzika mizu,+Koma mwadzidzidzi ndinayamba kutemberera malo ake okhala.   Ana ake amakhala kutali ndi chipulumutso,+Ndipo amaponderezedwa pachipata, popanda wowapulumutsa.   Zimene iye amakolola, munthu wanjala amazidya.Ngakhale nyama yake imene waipha n’kuikoloweka pangowe, wina amadzaitenga,Ndipo msampha umawalanda zofunika pa moyo wawo.   Pajatu zopweteka sizichokera m’fumbi,Ndipo mavuto satuluka m’nthaka.   Pakuti munthu amabadwa kuti akumane ndi mavuto,Monga momwe mbaliwali zimathethekera m’mwamba kuchokera pamoto.   Koma ndikanakhala ine, ndikanafunsa kwa Mulungu,Ndipo kwa Mulunguyo, ndikanatula mlandu wanga.+   Kwa Iye amene amachita zinthu zazikulu ndi zosatheka kuzifufuza,Zinthu zodabwitsa zosawerengeka.+ 10  Kwa Iye amene amapereka mvula padziko lapansi,+Ndi kupititsa madzi pabwalo.+ 11  Kwa Iye amene amaika anthu onyozeka pamalo okwezeka,+Mwakuti anthu achisoni amakhala pamwamba, pomwe amapezapo chipulumutso. 12  Kwa Iye amene amalepheretsa zolinga za ochenjera,+Mwakuti ntchito imene manja awo amagwira siioneka. 13  Kwa Iye amene amakola anzeru m’kuchenjera kwawo,+Iye amene amachititsa kuti malangizo a ochenjera abweretse chisokonezo.+ 14  Iwo amakumana ndi mdima ngakhale masana,Ndipo amafufuzafufuza masanasana ngati kuti ndi usiku.+ 15  Kwa Iye amene amapulumutsa munthu ku lupanga lochokera m’kamwa mwa oipa,Ndi kupulumutsa wosauka m’manja mwa wamphamvu.+ 16  Mwakuti wonyozeka amapeza chiyembekezo,+Koma anthu opanda chilungamo amatseka pakamwa pawo.+ 17  Tamvera! N’ngodala munthu amene Mulungu amam’dzudzula,+Ndipo chilango* cha Wamphamvuyonse usachikane. 18  Pakuti iye amayambitsa kupweteka, koma amamanga chilonda chopwetekacho.Amaphwanya anthu, koma manja ake ndi amene amawachiritsa. 19  Adzakulanditsa m’masautso 6,+Ndipo m’masautso 7, palibe choipa chimene chidzakukhudze.+ 20  Pa nthawi yanjala, adzakulanditsa ndithu ku imfa,+Ndipo pa nkhondo adzakupulumutsa ku mphamvu ya lupanga. 21  Udzabisidwa ku lilime lomenya ngati chikwapu,+Ndipo sudzachita mantha ikadzafika nthawi yowononga. 22  Pa nthawi yowononga ndi yanjala, iweyo udzaseka,Ndipo nyama zakutchire sudzaziopa. 23  Udzachita pangano ndi miyala yakutchire,Ndipo nyama zakutchire zidzakhala nawe pa mtendere.+ 24  Udzaona ndithu kuti mtendere ndiwo hema wako,Ndipo ukapita kukayendera malo ako odyetserako ziweto, udzaona kuti palibe chimene chikusowa. 25  Ndithu udzaona kuti ana ako ndi ambiri,+Ndipo mbadwa zako zidzakhala ngati zomera za padziko lapansi.+ 26  Udzakhala ndi mphamvube mpaka kulowa m’manda,+Mofanana ndi ngala zokhwima za tirigu, zimene amazisanjikiza pamodzi pamalo opunthira tirigu pa nyengo yake. 27  Izi n’zimene tafufuza ndipo zilidi choncho.Imva zimenezi ndi kuzitsatira.”

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “woyera.”
Onani Mawu a m’munsi pa Miy 1:2.