Yobu 41:1-34

41  “Kodi ungawedze ng’ona*+ ndi mbedza?Kapena ungamange lilime lake ndi chingwe?   Kodi ungaike chingwe cha udzu* m’mphuno mwake?+Kapena kodi ungaboole nsagwada zake ndi minga?   Kodi iyo ingachonderere kambirimbiri kwa iwe,Kapena kodi ingalankhule nawe mofatsa?   Kodi ingachite nawe pangano,Kuti uitenge ngati kapolo mpaka kalekale?   Kodi ungasewere nayo ngati mbalame,Kapena kodi ungaimange kuti izisangalatsa ana ako aakazi?   Kodi ochita malonda angaigule posinthanitsa ndi chinthu china?Kodi angaigawe pakati pa amalonda?   Kodi ungadzaze khungu lake ndi ntcheto,*+Kapena mutu wake ndi mikondo yophera nsomba?   Ika dzanja lako pa iyo.Kumbukira nkhondoyo. Usadzachitenso.   Ndithu, zimene munthu anali kuyembekezera adzakhumudwa nazo,Komanso adzagwa pansi akangoiona. 10  Palibe angalimbe mtima kuti aipute.Kodi ndani angaimitsane nane?+ 11  Ndani wayamba kundipatsa kanthu, kuti ndim’patse mphoto?+Zinthu zonse za pansi pa thambo ndi zanga.+ 12  Sindikhala chete osanena za ziwalo zake,Kapena za mphamvu zake ndi kukongola kwa thupi lake loumbidwa bwino. 13  Ndani angaivule chovala chake?Ndani angalowe pakati pa nsagwada zake? 14  Ndani watsegula zitseko za kumaso kwake?Mano ake onse ndi ochititsa mantha. 15  Mizere ya mamba ake ndiyo kudzikuza kwake.Iwo ndi otsekeka ngati anachita kuwamatirira pamodzi. 16  Ndi othithikana kwambiri,Moti ngakhale mpweya sungadutse pakati pawo. 17  Onse anamatirirana.Anagwirana ndipo sizingatheke kuwalekanitsa. 18  Ikamatulutsa mpweya, pamaoneka kuwala.Maso ake ali ngati kuwala kwa m’bandakucha. 19  M’kamwa mwake mumatuluka kung’anima kwa mphezi,Ngakhale moto wothetheka umatulukamo. 20  M’mphuno mwake mumatuluka utsi,Ngati ng’anjo imene yayatsidwa ndi udzu. 21  Moyo wake umayatsa makala.Ngakhale lawi la moto limatuluka m’kamwa mwake. 22  M’khosi mwake mumakhala mphamvu,Ndipo pamaso pake, kutaya mtima kumadumpha. 23  Minofu yake yokwinyika imamatana.Imakhala ngati anaiumbira pomwepo ndipo sisunthika. 24  Mtima wake anauumba kuti ukhale wolimba ngati mwala.Anauumbadi ngati mwala wapansi wa mphero. 25  Ikadzuka, amphamvu amachita mantha.+Ikathedwa nzeru, amadabwa kwambiri. 26  Lupanga silitha kuigonjetsa,Ngakhalenso mkondo, mpaliro, kapena muvi.+ 27  Chitsulo+ imangochiona ngati udzu,Ndipo mkuwa imangouona ngati mtengo wowola. 28  Muvi suithamangitsa.Miyala yoponya ndi gulaye*+ imasanduka mapesi kwa iyo. 29  Chibonga imangochiona ngati phesi.+Imaseka ikamva phokoso la nthungo. 30  Kumimba kwake kuli ngati timapale tosongoka.Imayala chopunthira mbewu+ pamatope. 31  Imachititsa madzi akuya kuwira ngati mphika.Imachititsa nyanja kukhala ngati mphika wa mafuta onunkhira. 32  Imachititsa njira kuwala m’mbuyo mwake.Munthu angaone madzi akuya ngati kuti ndi imvi. 33  Pafumbi palibe chofanana nayo.Iyo inapangidwa kuti isamachite mantha. 34  Imaona chilichonse chokwezeka.Iyo ndi mfumu ya zilombo zonse zakutchire.”

Mawu a M'munsi

M’Chiheberi, “Leviyatani.”
Mawu ake enieni, “mlulu.”
Umenewu ndi mpaliro umene mwina unali ndi mano oyang’ana kumbuyo ngati dzino la mbedza.
Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala ndi dzanja chimene amachita kupukusa. M’madera ena amati mvuluma kapena ulaya.