Yobu 40:1-24

40  Tsopano Yehova anafunsa Yobu kuti:   “Kodi munthu ayenera kum’tola chifukwa Wamphamvuyonse, n’kutsutsana naye?+Amene akudzudzula Mulungu ayankhe.”+  Ndiyeno Yobu anamuyankha Yehova kuti:   “Ine tsopano ndakhala wopanda pake.+Kodi ndingakuyankheni chiyani?Ndaika dzanja langa pakamwa.+   Ndalankhula kamodzi ndipo sindiyankhanso.Sindionjezera chilichonse pa mawu amene ndalankhula kawiri.”  Tsopano Yehova anamuyankha Yobu kuchokera mumphepo yamkuntho+ kuti:   “Takokera chovala chako n’kuchimanga m’chiuno ngati mwamuna wamphamvu.+Ndikufuna ndikufunse mafunso ndipo iweyo undiyankhe.+   Kodi ndithu ukuchititsa chilungamo changa kukhala chopanda pake?Kodi ukunena kuti ine ndine wolakwa kuti iweyo ukhale wolondola?+   Kapena kodi uli ndi dzanja ngati la Mulungu woona?+Kodi ungachititse mabingu kugunda ndi mawu ngati a Mulungu?+ 10  Tadziveka ukulu+ ndiponso kukwezeka,+Ndipo uvale ulemu+ ndi ulemerero.+ 11  Mkwiyo wako wosefukira utuluke,+Ndipo uone aliyense wodzikweza n’kumutsitsa. 12  Uone wodzikweza aliyense n’kumuchepetsa,+Ndipo oipa uwaponderezere pamalo pomwe alilipo. 13  Uwabise pamodzi m’fumbi,+Uphimbe nkhope zawo m’malo obisika, 14  Ndipo ineyo ndidzakuyamikira,Chifukwa chakuti dzanja lako lamanja lingakupulumutse. 15  Ine ndinapanga mvuu* ndipo ndinapanganso iweyo.Iyo imadya udzu wobiriwira+ ngati ng’ombe yamphongo. 16  Mphamvu zake zili m’chiuno mwake,Ndipo minofu ya pamimba pake ndi yamphamvu kwambiri.+ 17  Imapindira pansi mchira wake ngati mtengo wa mkungudza,Mitsempha ya m’ntchafu mwake ndi yolukanalukana. 18  Mafupa ake ali ngati mapaipi amkuwa,Mafupa ake olimba ali ngati ndodo zachitsulo. 19  Iyo ndiyo chiyambi cha njira za Mulungu.Amene anaipanga+ akhoza kubweretsa pafupi lupanga lake. 20  Pakuti mapiri amaberekera iyoyo mbewu zawo,+Ndipo nyama zonse zakutchire zimasewera pamenepo. 21  Imagona pansi pa mitengo yaminga,Pamalo obisika m’mabango+ ndi m’madambo.+ 22  Mitengo yaminga imaitchinga ndi mthunzi wawo.Mitengo ya msondodzi ya kuchigwa* imazungulira mvuuyo. 23  Mtsinje ukakalipa iyo sichita mantha n’kuthawa.Sitekeseka ngakhale madzi a mu Yorodano+ asefukire n’kumainyowetsa kumaso. 24  Kodi alipo amene angaigwire iyo ikuona?Kodi alipo amene angakole mphuno yake ndi ngowe?

Mawu a M'munsi

M’Chiheberi, “Behemoti.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.