Yobu 4:1-21

4  Tsopano Elifazi+ wa ku Temani anayankha kuti:   “Munthu akayesa kukulankhula, kodi utopa?Koma ndani angathe kudziletsa kuti asalankhule?   Iweyo walangiza anthu ambiri,+Ndipo manja ofooka unali kuwalimbitsa.+   Aliyense wofuna kugwa, mawu ako anali kumudzutsa,+Ndipo mawondo olobodoka unali kuwachirikiza.+   Koma panopa zili pa iwe, ndipo watopa nazo,Zakhudza iwe, ndipo wasokonezeka nazo.   Popeza umaopa Mulungu, kodi sukuyenera kulimba mtima?Kodi ulibe chiyembekezo, munthu woti ukuyenda ndi mtima wosagawanika?+   Takumbukira: Kodi ndani wosalakwa amene anawonongedwapo?Ndipo n’kuti kumene anthu owongoka mtima+ anafafanizidwapo?   Malinga ndi zimene ine ndaona, anthu okonzera anzawo zopweteka,Ndi ofesa mavuto, amakolola zomwezo.+   Iwo amawonongeka ndi mpweya wa Mulungu,Ndipo ndi mphamvu ya mkwiyo wake, amatha. 10  Mkango umabangula, ndipo mkango wamphamvu umamveka kulira,Koma ngakhale mano a mkango wamphamvu, amathyoka. 11  Mkango umafa posowa nyama yoti udye,Ndipo ana a mkango amalekanitsidwa. 12  Tsopano mawu anabwera kwa ine mwakachetechete,Ndipo khutu langa linamva kunong’ona kwa mawuwo.+ 13  Ndinakhala ndi malingaliro osautsa chifukwa cha masomphenya amene ndinaona usiku,Pa nthawi imene anthu amakhala ali m’tulo tofa nato. 14  Ndinachita mantha kwambiri ndiponso ndinanjenjemera,Ndipo mafupa anga onse anadzaza mantha. 15  Mzimu unadutsa kumaso kwanga,Ndipo ubweya wa pathupi langa unayamba kuimirira. 16  Mzimuwo unaima chilili,Koma sindinazindikire maonekedwe ake.Chinthu chinaima pamaso panga.Kunali bata, kenako ndinamva mawu akuti: 17  ‘Kodi munthu angakhale wolungama kuposa Mulungu?Kapena kodi munthu angakhale woyera kuposa amene anam’panga?’ 18  Iyetu sakhulupirira atumiki ake,Ndipo angelo* ake amawapezera zifukwa. 19  Nanga kuli bwanji anthu okhala m’nyumba zadothi,Amene maziko awo ali m’fumbi?+Iwo amathudzulidwa mosavuta kuposa kadziwotche. 20  Kuyambira m’mawa mpaka madzulo, amakhala akunyenyedwa.Amawonongeka kwamuyaya, popanda aliyense kukhudzika nazo. 21  Kodi chingwe cha hema wawo chimene chili mkati mwawo, sichinasololedwe?Iwo amafa chifukwa chosowa nzeru.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “amithenga.”