Yobu 39:1-30

39  “Kodi ukudziwa nthawi yoikidwiratu imene mbuzi za m’mapiri zokhala m’matanthwe zimabereka?+Kodi unaona nthawi imene mphoyo zimabereka+ ndi zowawa za pobereka?   Kodi umawerenga miyezi imene zimakwanitsa,Kapena ukudziwa nthawi yoikidwiratu imene zimabereka?   Zimagwada zikamaswa ana awo,Ululu wawo ukamatha.   Ana awo amakhala amphamvu ndi athanzi, ndipo amakulira m’tchire.Amachoka osabwereranso kwa makolo awo.   Ndani anapatsa mbidzi+ ufulu wongodziyendera,Ndipo ndani anamasula zingwe za bulu wam’tchire,   Amene ndinam’patsa chipululu monga nyumba yake,Ndiponso amene amakhala kudera la nthaka yamchere?+   Amaseka chipwirikiti cha m’mudzi.Samva phokoso la wowenda nyama.+   Amayendayenda m’mapiri pofunafuna msipu,+Ndipo amafunafuna chomera chilichonse chobiriwira.+   Kodi ng’ombe yamphongo yam’tchire* imafuna kukutumikira,+Kapena ingagone pafupi ndi chodyeramo ziweto zako? 10  Kodi ungaimange zingwe kuti ilime mizere,Kapena kodi ingasalaze+ zigwa pambuyo pako? 11  Kodi ungaikhulupirire chifukwa ili ndi mphamvu zochuluka,Kapena ungaisiyire ntchito yako? 12  Kodi ungaidalire kuti ikubweretsere mbewu zako,Ndi kuti izitutire popunthira? 13  Kodi nthiwatiwa yaikazi imakupiza mapiko ake mosangalala,Kapena kodi ili ndi mapiko ndi nthenga zofanana ndi za dokowe?+ 14  Pakuti imasiya mazira ake munthaka,Ndipo imawatenthetsa m’fumbi. 15  Imaiwala kuti phazi linalake likhoza kuwaphwanya,Kapenanso kuti nyama yakutchire ikhoza kuwaponda. 16  Imachitira nkhanza ana ake ngati kuti si ake,+Ndipo imagwira ntchito pachabe chifukwa ilibe mantha. 17  Pakuti Mulungu waichititsa kuiwala nzeru,Ndipo sanaigawireko kuzindikira.+ 18  Ikatambasula mapiko ake ndi kuwakupiza,Imaseka hatchi ndi wokwerapo wake. 19  Kodi hatchi ungaipatse mphamvu?+Kodi ungaveke khosi lake manyenje awirawira? 20  Kodi ungaichititse kudumpha ngati dzombe?Ulemerero wa kumina kwake n’ngoopsa.+ 21  Imachita mgugu+ m’chigwa, ndipo imadumpha mwamphamvu.Imapita kukakumana ndi zida zankhondo.+ 22  Imaseka zoopsa ndipo sichita mantha.+Sibwerera ikaona lupanga. 23  Kachikwama koika mivi kamachita phokoso kakamagunda m’nthiti mwakeLimodzi ndi mkondo ndi nthungo.* 24  Imatha mtunda mwamgugu ndiponso mosangalala.Ikamva kulira kwa lipenga sikhulupirira chifukwa cha chisangalalo. 25  Lipenga likangolira, imati eyaa!Imanunkhiza nkhondo ili kutali,Imamva phokoso la mafumu ndi mfuu yankhondo.+ 26  Kodi kuzindikira kwako n’kumene kumachititsa kabawi kuuluka pamwamba,Ndi kutambasulira mapiko ake mphepo yakum’mwera? 27  Kapena kodi lamulo lako n’limene limachititsa chiwombankhanga+ kuulukira m’mwamba,Ndi kumanga chisa chake pamwamba kwambiri,+ 28  Kukhala pathanthwe ndi kugona pomwepo usiku,Pansonga penipeni pa thanthwe ndi pamalo povuta kufikapo? 29  Chimafunafuna chakudya kuchokera pamenepo.+Maso ake amaona kutali kwambiri. 30  Ana ake amakhalira kumwa magazi.Kumene kuli zakufa, icho chimakhala komweko.”+

Mawu a M'munsi

Mwina nyama imeneyi inali yooneka ngati njati.
Tikati “nthungo” tikutanthauza mkondo waung’ono, wopepukirako.