Yobu 38:1-41

38  Tsopano Yehova anamuyankha Yobu kuchokera mumphepo yamkuntho+ kuti:   “Kodi amene akuphimba malangizo angaNdi mawu ake opanda nzeruyu ndani?+   Takokera chovala chako n’kuchimanga m’chiuno ngati mwamuna wamphamvu.Ndikufuna ndikufunse mafunso ndipo iweyo undiyankhe.+   Kodi unali kuti pamene ndinkaika maziko a dziko lapansi?+Ndiuze ngati uli womvetsa zinthu.   Ndani anaika miyezo yake, ngati ukudziwa,Kapena ndani anatambasulirapo chingwe choyezera?   Kodi maziko ake anazikidwa pa chiyani?+Kapena ndani anaika mwala wake wapakona,   Pamene nyenyezi za m’mawa+ zinafuula pamodzi mokondwera,Ndiponso pamene ana onse a Mulungu+ anayamba kufuula ndi chisangalalo?   Ndani anatseka nyanja ndi zitseko,+Imene inayamba kuyenda ngati kuti ikutumphuka m’mimba?   Pamene ndinaika mtambo ngati chovala chake,Ndi mdima wandiweyani ngati nsalu yoikulungira. 10  Ndipo ndinaiikira lamulo,Ndinaiikiranso mpiringidzo ndi zitseko.+ 11  Kenako ndinaiuza kuti, ‘Ukhoza kufika apa, koma usapitirirepo,+Ndipo mafunde ako aatali azilekezera pamenepa.’+ 12  Kodi kuyambira masiku ako oyambirira unalamula m’mawa?+Kodi ndiwe unachititsa m’bandakucha kudziwa malo ake, 13  Kuti kuwala kwake kufike mpaka kumalekezero a dziko lapansi,Kuti anthu oipa asansidwe n’kuchotsedwamo?+ 14  Dzikolo limadzisintha ngati dongo+ pansi pa chodindira,Ndipo zinthu zimakhala pamalo awo ngati kuti zavala zovala. 15  Kuwala kwa oipa kumachotsedwa,+Ndipo dzanja lokwezedwa m’mwamba limathyoledwa.+ 16  Kodi unafika ku akasupe a nyanja,Kapena kodi unayamba wakafunafunapo madzi akuya?+ 17  Kodi anakuvundukulira zipata za imfa,+Kapena zipata za mdima wandiweyani,+ kodi ungathe kuziona? 18  Kodi unaganizapo mozama za kukula kwa dziko lapansi?+Ndiuze ngati ukudziwa zonse. 19  Kodi njira yopita kumene kuwala kumakhala ili kuti?+Nanga mdima, kwawo n’kuti, 20  Kuti uzipititse kumalire awo,Ndi kuti udziwe njira zopita kunyumba kwawo? 21  Kodi ukudziwa popeza pa nthawiyo unali utabadwa,+Ndiponso chifukwa chakuti masiku ako ndi ochuluka? 22  Kodi unalowapo munkhokwe ya chipale chofewa,+Kapena umaziona nkhokwe za matalala,+ 23  Zimene ndazisungira nthawi ya zowawa,Ndi tsiku lomenyana komanso lankhondo?+ 24  Kodi njira imene kuwala kumadzigawira ili kuti,Ndiponso njira imene mphepo ya kum’mawa+ imamwazikira padziko lapansi ili kuti? 25  Ndani anagawa ngalande ya madzi osefukira,Ndi njira ya mtambo wa mvula yamabingu,+ 26  Kuti achititse mvula kugwa padziko pamene palibe munthu,+Ndi kuchipululu kumene kulibe munthu aliyense, 27  Kuti inyowetse malo owonongeka ndi mvula yamkuntho ndiponso ouma,Komanso kuti imeretse udzu?+ 28  Kodi mvula ili ndi tate wake,+Kapena ndani anabereka mame?+ 29  Kodi madzi oundana amachokera m’mimba mwa ndani,Ndipo mame oundana+ a m’mlengalenga anawabereka ndani? 30  Madzi amadzibisa ngati kuti ali pansi pa mwala,Ndipo pamwamba pa madzi akuya pamauma.+ 31  Kodi ungamange zingwe gulu la nyenyezi la Kima,Kapena kodi ungamasule zingwe za gulu la nyenyezi la Kesili?+ 32  Kodi ungatulutse gulu la nyenyezi la Mazaroti pa nthawi yake?Ndipo kodi ungatsogolere gulu la nyenyezi la Asi pamodzi ndi ana ake? 33  Kodi malamulo akuthambo ukuwadziwa,+Kapena kodi ulamuliro wake ungauike padziko lapansi? 34  Kodi ungafuulire mtamboKuti madzi ochuluka akukhuthukire?+ 35  Kodi ungauze mphezi kuti zibwere kwa iweN’kudzakuuza kuti, ‘Ndife pano, tabwera’? 36  Ndani anaika nzeru+ m’mitambo,Kapena zinthu zochitika kuthambo, ndani anazipatsa kuzindikira?+ 37  Ndani amene ali ndi nzeru zoti angathe kudziwa chiwerengero cholondola cha mitambo,Kapena zosungira madzi akumwamba, ndani angathe kuzipendeketsa,+ 38  Fumbi likasanduka matope n’kumayenderera ngati chitsulo chosungunula,Ndiponso zibuma zadothi zikamatana? 39  Kodi mkango ungausakire nyama,Ndipo kodi ungakhutiritse mikango yamphamvu yanjala kwambiri,+ 40  Ikamyata m’malo amene imabisala,+Kapena ikabisala patchire kuti igwire nyama? 41  Ndani amakonzera khwangwala chakudya,+Ana ake akamalirira Mulungu kuti awathandize,Akamadzandira chifukwa chosowa chakudya?

Mawu a M'munsi