Yobu 37:1-24

37  “Chifukwa cha zimenezi, mtima wanga wayamba kunjenjemera,+Ndipo ukudumpha kuchoka m’malo mwake.   Amuna inu mvetserani mwatcheru kugunda kwa mawu a Mulungu,+Ndi kubangula kochokera m’kamwa mwake.   Amakuchititsa kumveka pansi ponse pa thambo,Ndipo mphezi yake+ imafika kumalekezero a dziko lapansi.   Pambuyo pake pamamveka phokoso.Iye amabangula+ ndi mawu ake amphamvu.+Mawu ake akamveka, iye saletsa mphezizo.+   Mulungu amabangula ndi mawu ake+ mochititsa chidwi kwambiri.Amachita zinthu zazikulu zimene sitingazidziwe.+   Chifukwa chipale chofewa amachiuza kuti, ‘Gwera padziko lapansi.’+Amauzanso mvula zimenezi, ngakhalenso mvula yamphamvu ikamakhuthuka.+   Iye amatseka dzanja la munthu aliyense,Kuti anthu onse adziwe ntchito ya Mulungu.   Nyama yakutchire imapita kukabisala,Ndipo imakhala m’malo ake obisala.+   Mphepo yamkuntho imachokera m’chipinda chamkati,+Ndipo kuzizira kumachokera mumphepo yakum’mawa.+ 10  Mpweya wa Mulungu umapereka madzi oundana,+Ndipo malo aakulu a madzi ndi oundana.+ 11  Iye amalemetsa mitambo ndi chinyontho.Kuwala kwake+ kumamwaza mitambo younjikana pamodzi. 12  Amaizunguliza ndi kuiwongolera kuti igwire ntchito yakeKulikonse kumene amailamula+ panthaka ya padziko lapansi. 13  Amagwiritsa ntchito mitamboyo kuti ipereke chilango,+ kuti inyowetse dziko lake,+Komanso kuti iye asonyeze kukoma mtima kwake kosatha.+ 14  Mvetserani izi inu a Yobu:Imani chilili ndi kuganizira mozama ntchito zodabwitsa za Mulungu.+ 15  Kodi mukudziwa nthawi imene Mulungu anapangana nazo,+Komanso pamene anachititsa kuunika kwa mtambo wake kuti kuwale? 16  Kodi mukudziwa mmene mtambo umaimira,+Ndiponso ntchito zodabwitsa za yemwe amadziwa zinthu bwino kwambiri?+ 17  Kodi mukudziwa momwe zovala zanu zimatenthera,Dziko likakhala chete kuyambira kum’mwera?+ 18  Kodi limodzi ndi iyeyo mungagangate* kuthambo,+Komwe kuli ngati galasi lolimba lopangidwa ndi chitsulo chosungunula? 19  Tidziwitseni zoti timuuze.Sitingathe kutulutsa mawu chifukwa cha mdima. 20  Kodi auzidwe kuti ndikufuna kulankhula?Kapena kodi munthu wina wanena kuti mawu alankhulidwa?+ 21  Tsopano iwo sakuona kuwala.Kuthambo kumanyezimira,Mphepo ikadutsa n’kuyeretsako. 22  Kunyezimira ngati kwa golide kumachokera kumpoto.Ulemu+ wa Mulungu ndi wochititsa mantha. 23  Wamphamvuyonse sitikumudziwa.+Iye ali ndi mphamvu zambiri,+Ndipo sadzanyoza+ chilungamo+ ndi kulungama kochuluka.+ 24  Choncho anthu amuope.+Iye saganizira aliyense amene amadziona kuti ndi wanzeru.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “kutchaya,” kapena “kutsendera.”