Yobu 36:1-33

36  Elihu anapitiriza kunena kuti:   “Ndilezereni mtima kwa kanthawi kochepa ndipo ndikuuzaniKuti mawu alipobe oti ndinene m’malo mwa Mulungu.   Zimene ndinene ndizitenga kutali,Ndipo ndilengeza kuti amene anandipanga, ndiye mwiniwake wa chilungamo.+   Chifukwa mawu anga ndithu si onama.Wodziwa bwino zinthu kwambiri+ ali ndi inu.   Mulungutu ndi wamphamvu+ ndipo sadzakana munthu.Iye ali ndi mphamvu zazikulu zomvetsa zinthu.   Iye sadzasiya woipa aliyense ali wamoyo,+Koma adzapereka chiweruzo cholungama kwa osautsika.+   Sadzachotsa maso ake pa aliyense wolungama.+Adzaika mafumu pamipando yachifumu,+Adzawachititsa kuti alamulire kwamuyaya, ndipo iwo adzakhala ndi mphamvu zambiri.   Anthu akamangidwa m’matangadza,+Amagwidwa ndi zingwe za masautso.   Ndiyeno iye adzawauza za momwe iwo amachitira zinthuNdiponso zolakwa zawo, chifukwa iwo amadzikuza. 10  Iye adzatsegula makutu awo kuti iwo amve pamene iye akuwalimbikitsa,+Ndipo adzawauza kuti asiye kuchita zopweteka ena.+ 11  Akamumvera ndi kumutumikira,Adzamaliza bwino masiku awo,Ndipo adzamaliza zaka zawo mosangalala.+ 12  Koma akapanda kumvera, adzaphedwa+ ndi chida.+Iwo adzafa ali osadziwa. 13  Anthu ampatuko adzaunjika mkwiyo.+Iwo sadzalirira thandizo chifukwa chakuti iye wawamanga. 14  Iwo adzafa ali anyamata,+Ndipo moyo wawo udzathera pakati pa mahule aamuna a pakachisi.+ 15  Iye adzapulumutsa wozunzika m’masautso ake,Ndipo adzatsegula makutu awo pamene akuponderezedwa. 16  Ndithu iye adzakukopani n’kukuchotsani pakamwa pa zowawa.+M’malomwake padzakhala malo otakasuka,+ osati opanikiza,Ndipo chitonthozo cha patebulo panu chidzakhala chodzaza ndi mafuta.+ 17  Ndithu mudzakhutira woipa+ akadzaweruzidwa.Chiweruzo ndi chilungamo zidzakhazikika. 18  Samalani kuti mkwiyo+ usakuchititseni kuwomba m’manja chifukwa cha njiru,Ndipo dipo lalikulu+ lisakusocheretseni. 19  Kodi kulira kwanu kopempha thandizo kudzakupindulirani?+ Ayi, sikudzakupindulirani ngakhalenso pa mavuto,Ngakhale muyesetse mwamphamvu bwanji.+ 20  Musapumire m’mwamba polakalaka usiku,Pamene anthu amabwera kuchokera kumene anali. 21  Samalani kuti musabwerere ku zinthu zopweteka ena,+Chifukwa mwasankha zimenezi m’malo mwa masautso.+ 22  Mulungutu amachita zinthu zapamwamba ndi mphamvu zake.Kodi mphunzitsi winanso ndani wofanana naye? 23  Ndani wam’funsa kuti afotokoze za njira yake,+Ndipo ndani wamuuza kuti, ‘Mwachita zosalungama’?+ 24  Kumbukirani kuti muyenera kutamanda ntchito zake,+Zimene anthu amaziimba.+ 25  Anthu onse amaziyang’anitsitsa.Munthu amaziyang’ana ali patali.+ 26  Mulungu ndi wokwezeka kuposa mmene tikudziwira.+Zaka zake n’zosawerengeka.+ 27  Pakuti iye amakoka madontho a madzi.+Madonthowo amasefeka n’kutsika ngati mvula ndi nkhungu, 28  Moti mitambo imakha,+Imakhetsa madzi ochuluka pa anthu. 29  Zoonadi, ndani angamvetse mmene mitambo imatambasukira?Komanso kugunda kochokera kumsasa wake?+ 30  Amaikuta ndi kuwala kwake,+Ndipo waphimba mizu ya nyanja. 31  Ndi zimenezi, iye amaweruza mokomera mitundu ya anthu.+Amapereka chakudya chochuluka.+ 32  Iye wafumbata mphezi m’manja mwake,Ndipo amailamula kuti igwere woukira.+ 33  Kugunda kwake+ kumanena za iye.Ziwetonso zimanena za amene akubwera.

Mawu a M'munsi