Yobu 35:1-16

35  Elihu anapitiriza kulankhula kuti:   “Kodi mukuona ngati chimenechi n’chilungamo?Inuyo mwanena kuti, ‘Ndine wolungama kuposa Mulungu.’+   Mwanena kuti, ‘Kodi kulungamako n’kwantchito yanji kwa inu?+Kodi kundipindulitsa chiyani kuposa chimene ndikanapindula pochimwa?’+   Ineyo ndikuyankhani inuyoNdi mabwenzi+ anu muli nawowo.   Yang’anani kumwamba+ muone.Muona kuti mitambo+ ili pamwamba kuposa inu.   Mukachimwa, kodi mumapindula chiyani chotsutsana naye?+Ndipo kupanduka kwanu kukawonjezeka, kodi mumam’chitira chiyani chomuipira?   Ngati ndinudi wosalakwa, kodi mumam’patsa chiyani?Kodi amalandira chiyani kuchokera m’manja mwanu?+   Kuipa kwanu kungapweteke munthu ngati inu nomwe,+Ndipo chilungamo chanu chingakomere mwana wa munthu wochokera kufumbi.+   Chifukwa cha kuchuluka kwa kuponderezedwa, iwo amangokhalira kufuula popempha thandizo.+Amangokhalira kulirira thandizo chifukwa cha dzanja la amphamvu.+ 10  Koma palibe wanena kuti, ‘Kodi Mulungu, Wondipanga Wamkulu,+ ali kuti,Amene amapatsa anthu nyimbo usiku?’+ 11  Iye ndiye amatiphunzitsa+ zambiri kuposa nyama zakutchire,+Ndipo amatipatsa nzeru kuposa ngakhale zolengedwa zouluka m’mlengalenga. 12  Iwo amangokhalira kulirira thandizo, koma iye sawayankha+Chifukwa cha kunyada+ kwa anthu oipa. 13  Koma Mulungu samva kufuula kwa anthu olankhula zinthu zonama,+Ndipo Wamphamvuyonse sawaona.+ 14  Nanga kuli bwanji mukanena kuti simumuona?+Mlanduwo uli pamaso pake, choncho muzimuyembekezera ndi nkhawa.+ 15  Tsopano popeza sanakulangeni chifukwa cha mkwiyo wake,+Iye sanaonenso kupupuluma kwanu.+ 16  Yobu akatsegula pakamwa pake amalankhula zopanda pake.Amachulukitsa mawu osonyeza kuti palibe chimene akudziwa.”+

Mawu a M'munsi