Yobu 34:1-37

34  Elihu anapitiriza kulankhula kuti:   “Mvetserani mawu anga, anthu anzeru inu.Ndipo anthu odziwa zinthu inu, ndimvereni.   Pakuti khutu limasiyanitsa mawu,+Monga mmene m’kamwa mumasiyanitsira kakomedwe ka chakudya.+   Tiyeni tidzisankhire chiweruzo.Tidziwe tokha pakati pathu chimene chili chabwino.   Pakuti Yobu wanena kuti, ‘Ndithu ine si ine wolakwa,+Koma Mulungu wapotoza chiweruzo changa.+   Kodi ndikunama za mmene chiweruzo changa chiyenera kukhalira?Chilonda changa chachikulu sichikupola ngakhale kuti sindinachimwe.’+   Kodi ndi mwamuna wamphamvu uti amene ali ngati Yobu,+Yemwe amamwa mnyozo ngati madzi?+   Iye ndithu ali pa ulendo wokachita ubwenzi ndi anthu ochita zopweteka ena,Komanso ali pa ulendo wokayenda ndi anthu oipa.+   Chifukwa wanena kuti, ‘Mwamuna wamphamvu sapindula kanthu+Akamachita zosangalatsa Mulungu.’ 10  Choncho inu amuna a mtima+ womvetsa zinthu, ndimvereni.Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe,+Ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.+ 11  Pakuti iye amapereka mphoto kwa munthu wochokera kufumbi malinga ndi zochita zake,+Ndipo amam’bweretsera zinthu zogwirizana ndi njira yake. 12  Ndithudi, Mulungu sachita zoipa,+Ndipo Wamphamvuyonse sakhotetsa chilungamo.+ 13  Ndani wam’patsa dziko lapansi?Ndipo ndani wam’patsa ulamuliro panthaka yonse? 14  Akaika mtima wake pa munthu aliyense,Akatenga mzimu* ndi mpweya wa munthuyo,+ 15  Zamoyo zonse zimafera limodzi,Ndipo munthu amabwerera kufumbi.+ 16  Choncho ngati mumamvetsa zinthu, mvetserani izi.Mvetserani mawu anga. 17  Kodi zoonadi munthu wodana ndi chilungamo angalamulire?+Ngati munthu wamphamvu ali wolungama, kodi munganene kuti ndi woipa?+ 18  Kodi munthu anganene kwa mfumu kuti, ‘Ndinu wopanda pake’?Kapena angauze anthu olemekezeka kuti, ‘Ndinu oipa’?+ 19  Alipo amene sanakonderepo akalonga,Ndipo saganizira kwambiri wolemekezeka kuposa wonyozeka,+Chifukwa onsewo anapangidwa ndi manja ake.+ 20  Iwo amafa mwadzidzidzi,+ ngakhale pakati pa usiku.+Anthuwo amagwedezeka uku ndi uku n’kufa,Ndipo amphamvu amachoka popanda dzanja lowachotsa.+ 21  Pakuti maso ake amayang’anitsitsa njira za munthu,+Ndipo amaona mayendedwe ake onse. 22  Kulibe mdima wandiweyaniWoti amene akuchita zopweteka ena abisaleko.+ 23  Pakuti iye saikiratu nthawi yoti munthu aliyenseApite kukaweruzidwa ndi Mulungu. 24  Iye amaphwanya amphamvu+ popanda kuwafufuza,Ndipo amachititsa ena kuima m’malo mwawo.+ 25  Chotero iye amazindikira ntchito zawo.+Amawagwetsa usiku ndipo iwo amatswanyidwa.+ 26  Amawamenya monga oipa,Pamalo pomwe ena akuonerera.+ 27  Chifukwa asiya kumutsatira,+Ndipo sasamala za njira zake zonse,+ 28  Kuti achititse kulira kwa wonyozeka kupita kwa iye.Choncho iye amamva kulira kwa osautsika.+ 29  Iye akachititsa bata, ndani angamudzudzule?Ndipo akabisa nkhope yake,+ ndani angamuone?Kaya abisire nkhope yake mtundu+ kapena munthu, n’chimodzimodzi. 30  Kuti munthu wopanduka asalamulire,+Ndi kuti pasakhale misampha+ ya anthu. 31  Kodi munthu ndithu anganene kwa Mulungu kuti,‘Ndapirira ngakhale kuti sindinachite cholakwa?+ 32  Ngakhale kuti sindikuona chilichonse, inuyo ndiphunzitseni?Ngati ndachita chosalungama chilichonse,Sindidzachichitanso?’+ 33  Kodi iye angakulipire mogwirizana ndi mmene ukuganizira, chifukwa chakuti ukukana chiweruzo chake?Chifukwa chakuti iweyo wasankha wekha, osati ine?Tsopano nena zimene ukudziwa. 34  Anthu a mtima womvetsa zinthu+ adzandiuza,Ngakhale munthu wanzeru komanso wamphamvu amene akundimvetsera adzandiuza kuti, 35  ‘Yobu sadziwa zimene akunena,+Ndipo amanena mawu osonyeza kuti iye ndi wosazindikira.’ 36  Atate anga, Yobu ayesedwe mpaka pamapetoChifukwa cha zimene anali kuyankha pakati pa amuna ochita zopweteka anzawo.+ 37  Chifukwa pa tchimo lake akuwonjezerapo kupanduka.+Akuwomba m’manja pakati pathu ndipo akuchulutsa zonena zake zotsutsana ndi Mulungu woona.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 4.