Yobu 33:1-33

33  “Tsopano inu a Yobu, imvani mawu anga,Ndipo tcherani khutu ku zonena zanga zonse.   Inetu nditsegula pakamwa panga,Lilime langa ndi m’kamwa mwanga+ mulankhula.   Zonena zanga zikusonyeza kuwongoka kwa mtima wanga,+Ndipo milomo yanga imanena nzeru moona mtima.+   Mzimu wa Mulungu unandiumba,+Mpweya wa Wamphamvuyonse unandipatsa moyo.+   Ngati mungathe ndiyankheni.Ndifotokozereni mawu anu, ndipo khalani pamalo anu.   Kwa Mulungu woona, ine ndili ngati inu nomwe.+Inenso ndinaumbidwa ndi dongo.+   Mwa ine mulibe chinthu choti muope,Ndipo mawu anga sakulemetsani.+   Komabe inu mwanena m’makutu anga,Ndipo ine ndakhala ndikumva mawu anu akuti,   ‘Ndine woyera, wopanda tchimo,+Ndilibe chondidetsa, ndilibe cholakwa.+ 10  Mulungu amapeza ponditsutsira,Amanditenga ngati mdani wake.+ 11  Amaika mapazi anga m’matangadza,+Amayang’anitsitsa njira zanga zonse.’+ 12  Ndikukuuzani, pamenepa simunalondole.+Chifukwa Mulungu ndi woposa kwambiri munthu.+ 13  N’chifukwa chiyani mumalimbana naye?+Kodi n’chifukwa chakuti sanakuyankheni mawu anu onse?+ 14  Pakuti Mulungu amalankhula koyamba,Kenako kachiwiri,+ ngakhale anthu asamvere. 15  Iye amawalankhula m’maloto+ ndi m’masomphenya+ a usiku,Anthu akakhala m’tulo tofa nato,Akamagona pabedi.+ 16  Pa nthawi imeneyi m’pamene amatsegula anthu makutu,+Pa chilimbikitso chake kwa iwo, amadindapo chidindo, 17  Kuti achotse munthu pa zochita zake,+Ndi kuti mwamuna wamphamvu am’bisire kunyada.+ 18  Amabweza munthu kuti asapite kudzenje,+Ndiponso kuti moyo wake usaphedwe ndi chida.+ 19  Kuwawa kumam’dzudzula iye ali pabedi pake,Mafupa ake amangokhalira kukangana. 20  Moyo wake umanyansitsa chakudya,+Ndipo iye amanyansidwa ndi chakudya chokoma. 21  Mnofu wake umatha, osaonekanso.Mafupa ake amene sanali kuoneka amakhala pamtunda. 22  Iye amayandikira kudzenje,+Ndipo moyo wake umayandikira kwa akupha. 23  Ngati iye ali ndi mthenga,Womulankhulira mmodzi pa omulankhulira 1,000,Kuti auze munthu zimene zili zowongoka, 24  Mulungu amasangalatsidwa naye ndi kunena kuti,‘M’pulumutseni kuti asapite m’dzenje,+Chifukwa ndapeza dipo.*+ 25  Mnofu wake usalale kuposa mmene unalili ali mnyamata.+Abwerere ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.’+ 26  Adzadandaulira Mulungu kuti asangalale naye,+Adzaona nkhope yake akufuula mosangalala,Ndipo Mulungu adzabwezera kwa munthu kulungama kwa Mulunguyo. 27  Adzaimbira anthu n’kunena kuti,‘Ndachimwa,+ ndakhotetsa zimene zinali zowongoka,Ndipo sindinayenere kuchita zimenezi. 28  Iye wandiwombola kuti ndisapite kudzenje,+Ndipo moyo wanga udzaona kuwala.’ 29  Mulungutu amachita zinthu zonsezi.Kawiri kapena katatu konse, amachitira zimenezi mwamuna wamphamvu, 30  Kum’bweza kuti asapite kudzenje,+Kuti aunikiridwe ndi kuwala kwa anthu amene ali moyo.+ 31  Tcherani khutu inu a Yobu. Ndimvereni!Khalani chete, ndipo ine ndipitiriza kulankhula. 32  Ngati muli ndi mawu, ndiyankheni.Lankhulani chifukwa ine ndakondwera ndi kulungama kwanu. 33  Ngati mulibe mawu alionse, mvetserani mawu anga.+Khalani chete, ndipo ine ndikuuzani nzeru.”

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.