Yobu 32:1-22

32  Choncho amuna atatuwa anasiya kumuyankha Yobu, chifukwa iye anali kudziona kuti ndi wolungama.+  Koma Elihu mwana wa Barakeli mbadwa ya Buza+ wa m’banja la Ramu anakwiya kwambiri. Anakwiyira Yobu chifukwa Yobuyo ankanena kuti anali wolungama, osati Mulungu.+  Iye anakwiyiranso anzake atatu aja chifukwa chakuti iwo sanapeze yankho koma ankanena kuti Mulungu ndi woipa.+  Elihu anali ndi mawu koma anadikira kuti Yobu amalize, chifukwa anthuwo anali aakulu kwa Elihuyo.+  M’kupita kwa nthawi, Elihu anaona kuti amuna atatuwo analibe choyankha+ ndipo mkwiyo wake unakulirakulira.  Kenako Elihu mwana wa Barakeli mbadwa ya Buza anati:“Ine ndine wamng’onoNdipo amuna inu ndinu achikulire.+N’chifukwa chake ndinabweza mawu anga ndipo ndinaopaKukuuzani zimene ndikudziwa.   Choncho ndinati, ‘Masiku alankhule.Zaka zambiri n’zimene ziyenera kudziwitsa anthu nzeru.’+   Ndithudi, mzimu wa anthuNdiponso mpweya wa Wamphamvuyonse n’zimene zimawachititsa kumvetsa zinthu.+   Si anthu a masiku ambiri okha amene amakhala ndi nzeru,+Ndipo si okalamba okha amene amadziwa kuweruza.+ 10  Chotero ndinati, ‘Ndimvereni.Ndikufuna kunena zimene ndikudziwa.’ 11  Inetu ndimadikira kuti inu mulankhule.Ndakhala ndikumvetsera maganizo anu,+Kufikira mutapeza mawu oti munene. 12  Ndakhala ndikukumvetserani mwachidwi,Ndipo palibe aliyense amene akum’dzudzula Yobu.Palibe aliyense wa inu amene akuyankha zonena zake, 13  Kuti musanene kuti, ‘Tapeza nzeru.+Mulungu ndiye akumuthamangitsa, osati munthu.’ 14  Popeza sanalankhule mawu ondinena,Ine sindimuyankha ndi mawu anu. 15  Iwo achita mantha, sakuyankhanso.Mawu awathera. 16  Ine ndadikira, chifukwa sakupitiriza kulankhula.Pakuti anangoima chilili, sanayankhenso. 17  Ine ndifotokozapo maganizo anga.Ndinena zimene ndikudziwa, 18  Chifukwa ndili ndi mawu ambiri.Mzimu wandikanikiza+ m’mimba mwanga. 19  Mimba yanga ili ngati vinyo amene alibe potulukira,Ngati matumba atsopano, ikufuna kuphulika.+ 20  Ndiloleni ndilankhule kuti ndipeze mpumulo.Nditsegula pakamwa panga kuti ndiyankhe.+ 21  Sindikondera munthu,+Ndipo sindipereka dzina laulemu kwa munthu aliyense wochokera kufumbi.+ 22  Chifukwa sindikudziwa kuti ndingapereke bwanji dzina laulemu kwa munthu.Pakuti amene anandipanga+ angandichotse mosavuta.

Mawu a M'munsi