Yobu 30:1-31

30  “Tsopano anthu amene ndi ana aang’ono poyerekeza ndi ine,+Akundiseka.+Anthu amene abambo awo sindikanalolaKuwaika pamodzi ndi agalu oweta nkhosa zanga.   Ngakhale mphamvu za manja awo zinali zopanda ntchito kwa ine.Ndiponso nyonga zawo zatha.+   Chifukwa cha njala ndiponso kusowa, iwo ali ngati akufa.Amatafuna dera lopanda madzi,+Limene dzulo kunali mphepo yamkuntho ndi chiwonongeko.   Iwo anali kubudula chitsamba cha mchere m’tchire,Ndipo mizu ya timitengo ndiyo inali chakudya chawo.   Ankathamangitsidwa m’mudzi.+Anthu ankawakuwiza ngati mbala.   Iwo amakhala m’malo otsetsereka a m’zigwa,*M’maenje a m’nthaka ndi m’matanthwe.   Amalira mokuwa ali pakati pa zitsamba,Amaunjikana pansi pa zitsamba zaminga.   Ana a munthu wopusa,+ komanso ana a munthu wopanda dzina.Iwo akwapulidwa n’kuthamangitsidwa m’dziko.   Tsopano ine ndakhala mutu wa nyimbo yawo,+Ndipo kwa iwo ndine chinthu choseketsa.+ 10  Akunyansidwa nane, ndipo akukhala patali ndi ine.+Sakuzengereza kundilavulira kumaso.+ 11  Pakuti iye anakhwefula chingwe cha uta wanga n’kunditsitsa,Ndipo zingwe za pakamwa pa hatchi,* iwo anazisiya zomasula chifukwa cha ine. 12  Iwo aimirira kudzanja langa lamanja ngati kagulu ka anthu oipa.Amasula mapazi anga,Koma andiikira zopinga zovulaza kwambiri.+ 13  Iwo awononga njira zanga.Anangondibweretsera mavuto,+Popanda aliyense wowathandiza. 14  Amabwera ngati akudutsa pampata waukulu,Amakokoloka ndi madzi a mvula yamkuntho. 15  Zoopsa zadzidzidzi zandibwerera.Ulemerero wanga wachoka ngati kuti wauluzika ndi mphepo,Ndipo chipulumutso changa chapita ngati mtambo. 16  Tsopano moyo wanga ukukhuthuka mwa ine.+Masiku a masautso+ ali pa ine. 17  Usiku mafupa anga+ amabooledwa n’kugwa pansi.Zowawa zonditafuna sizipuma.+ 18  Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu, chovala* changa chimasintha,Ndipo chimandithina ngati kolala yothina. 19  Iye wanditsitsa mpaka m’dothi,Moti ndikukhala ngati fumbi ndi phulusa. 20  Ndimafuulira kwa inu kuti mundithandize, koma simundiyankha.+Choncho ndaimirira kuti mundimvere. 21  Mwasintha n’kukhala wankhanza kwa ine.+Ndi mphamvu yonse ya dzanja lanu, mwandisungira chidani. 22  Mwandiuluza ndi mphepo, mwandinyamula nayo.Kenako mwandisungunula ndi mkokomo wake. 23  Pakuti ndikudziwa bwino kuti mudzandibwezera ku imfa,+Kunyumba yosonkhanako aliyense wamoyo. 24  Koma palibe amene amatambasula dzanja lake polimbana ndi mulu wa zinthu zowonongeka.+Komanso pa kuwonongeka kwa munthu, palibe amene amapempha thandizo la zinthu zimenezo. 25  Ndithu, ndalirira munthu amene zinthu sizikumuyendera bwino.+Moyo wanga walirira munthu wosauka.+ 26  Ngakhale kuti ndinkadikirira zabwino, zoipa n’zimene zinabwera.+Ndinkadikirira kuwala, koma kunabwera mdima. 27  Matumbo anga anawira ndipo sanakhale chete.Masiku a masautso anandipeza. 28  Ndinayendayenda mwachisoni+ pamene kunalibe kuwala.Ndinaimirira mumpingo, ndipo ndinkangofuula popempha thandizo. 29  Ndinakhala m’bale wake wa mimbulu,Ndi mnzawo wa ana aakazi a nthiwatiwa.+ 30  Khungu langa linakhala lakuda+ ndipo linayoyoka pathupi panga.Mafupa anga anatentha chifukwa chouma. 31  Zeze wanga anangokhala wolirirapo,Ndipo chitoliro changa chinangokhala choimbapo mawu a anthu olira.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Ena amati “hosi,” kapena “kavalo.”
N’kutheka kuti akutanthauza “khungu.”