Yobu 3:1-26

3  Pambuyo pa zimenezi m’pamene Yobu anatsegula pakamwa pake n’kuyamba kutemberera tsiku limene anabadwa.+  Tsopano Yobu anati:   “Liwonongeke tsiku limene ndinabadwa,+Ndiponso usiku umene wina ananena kuti, ‘Mwamuna wamphamvu wapangika m’mimba.’   Tsiku limenelo likhale mdima.Mulungu asaliganizirenso ali kumwamba,Ndipo kuwala kusalifikire.   Mdima wandiweyani ulitenge.Mtambo wa mvula uliphimbe.Zinthu zimene zimadetsa tsiku ziliopseze.+   Usiku umenewo utengedwe ndi mdima.+Usasangalale pakati pa masiku a pachaka,Pachiwerengero cha miyezi, usalowe nawo.   Ndithu usiku umenewo ukhale wosabereka.Mfuu yachisangalalo isamveke usikuwo.+   Otemberera masiku alitemberere tsikulo,Iwo amene ali okonzeka kudzutsa ng’ona.*+   Nyenyezi za m’chisisira cha m’mawa mwake zizime.Lidikire kuwala koma lisakuone,Ndipo lisaone kuwala kwa m’bandakucha. 10  Chifukwa silinatseke zitseko za mimba ya mayi anga,+Kuti ndisaone mavuto. 11  Bwanji sindinafere m’chiberekero?+Bwanji sindinamwalire nditangotuluka m’mimba? 12  N’chifukwa chiyani mawondo anakumana nane,Ndipo mabere+ ndinakumana nawo chifukwa chiyani kuti ndiyamwe? 13  Panopa bwenzi nditagona kuti ndisasokonezedwe,+Bwenzi ndili m’tulo pa nthawiyo, ndipo bwenzi pano ndikupuma+ 14  Limodzi ndi mafumu ndi aphungu a padziko lapansi,+Amene anadzimangira malo omwe tsopano ali bwinja.+ 15  Kapena ndi akalonga amene ali ndi golide,Amene amadzaza nyumba zawo ndi siliva. 16  Kapena ngati pakati pomwe papita pachabe mosadziwa,+ bwenzi ine kulibe,Mofanana ndi ana amene sanaone kuwala.+ 17  Kumandako oipa asiya kusautsika,+Ndipo kumeneko anthu omwe mphamvu zawo zatha, akupuma.+ 18  Akaidi onse pamodzi ali pa mtendere.Iwo samvanso mawu a munthu wowakusira ku ntchito.+ 19  Aang’ono ndi aakulu amakhala chimodzimodzi kumeneko,+Ndipo kapolo amamasuka kwa mbuye wake. 20  N’chifukwa chiyani Mulungu amapereka kuwala kwa munthu amene ali ndi mavuto,Ndiponso moyo kwa opwetekedwa mtima?+ 21  N’chifukwa chiyani anthu ena amadikirira imfa, koma siwabwerera,+Ngakhale amakumba pansi poifunafuna, kuposa mmene amakumbira chuma chobisika? 22  Amenewa amasangalala kwadzaoneni,Amakondwera akapeza manda. 23  N’chifukwa chiyani Mulungu amapereka kuwala kwa mwamuna wamphamvu amene njira yake yabisika,+Amene Mulungu akum’pingapinga?+ 24  Pakuti chakudya changa chimabwera limodzi ndi kuusa moyo,*+Ndipo ngati madzi, kubuula kwanga kumakhuthuka.+ 25  Chinthu chochititsa mantha chimene ndinali kuchita nacho mantha, chandibwerera,Ndipo chimene ndinali kuchiopa chabwera kwa ine.+ 26  Sindinali wopanda nkhawa kapena wopanda mavuto,Komanso sindinali pa mtendere, komabe zosautsa mtima zandibwerera.”

Mawu a M'munsi

M’Chiheberi, “Leviyatani.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.