Yobu 29:1-25

29  Yobu anayambanso kulankhula mwandakatulo kuti:   “Ndikulakalaka ndikanakhala ngati mmene ndinalili m’miyezi yakale,+Ngati mmene ndinalili m’masiku amene Mulungu anali kundiyang’anira,+   Pamene anachititsa nyale yake kuwala pamutu panga,Pamene ndinkayenda mu mdima iye akundiunikira ndi kuwala kwake.+   Ngati mmene ndinalili m’masiku amene ndinali mnyamata,+Pamene Mulungu anali bwenzi langa lapamtima, ndipo anali pahema wanga,+   Pamene Wamphamvuyonse anali nane,Pamene antchito anga onse anandizungulira,   Pamene ndinkasambitsa mapazi anga m’mafuta a mkaka,Ndiponso pamene miyala inkanditulutsira mitsinje ya mafuta.+   Ndikapita kuchipata cha mzinda,+Ndinkakonzako malo anga okhala pabwalo la mzinda.+   Anyamata akandiona, ankabisala.Ngakhale okalamba ankanyamuka n’kuima chilili.+   Akalonga ankabweza mawu,Ndipo ankagwira pakamwa.+ 10  Mawu a atsogoleri ankabisika,Ndipo lilime lawo linkamamatira m’kamwa mwawo.+ 11  Khutu likamva, linkanena kuti ndine wodala,Ndipo diso likaona, linkandichitira umboni. 12  Pakuti ndinkapulumutsa wosautsika wopempha thandizo,+Ndiponso mwana wamasiye* ndi aliyense amene analibe womuthandiza.+ 13  Madalitso+ a munthu amene watsala pang’ono kuwonongedwa ankabwera kwa ine,Ndipo ndinkasangalatsa mtima wa mkazi wamasiye.+ 14  Ndinkavala chilungamo, ndipo icho chinkandiveka.+Chilungamo changa chinali ngati malaya akunja odula manja, ndi nduwira.* 15  Ndinali ngati maso kwa wakhungu,+Ndipo ndinali mapazi kwa wolumala. 16  Ndinali bambo weniweni kwa osauka,+Ndipo mlandu wa munthu amene sindinali kumudziwa ndinkaufufuza.+ 17  Ndinkaphwanya nsagwada za wochita zoipa,+Ndipo wogwidwa, ndinkamulanditsa kukamwa kwa wochita zoipayo. 18  Ndinkati, ‘Ndidzafera m’chisa changa,+Ndidzachulukitsa masiku anga ngati mchenga.+ 19  Muzu wanga ndi wotseguka kuti uyamwe madzi,+Ndipo mame akhala usiku wonse panthambi yanga. 20  Ulemerero wanga ndili nawobe,Ndipo uta umene uli m’manja mwanga uziponya mivi mobwerezabwereza.’ 21  Anthu ankandimvera ndipo ankandidikirira.Ankakhala phee kuti amve malangizo anga.+ 22  Ndikamaliza kulankhula, iwo sankalankhulanso.Ndipo mawu anga ankadonthera pa iwo.+ 23  Iwo ankandidikirira ngati akudikira mvula,+Ndipo ankayasama kuti m’kamwa mwawo mugwere mvula yomalizira.+ 24  Ndinkawamwetulira, koma iwo sankakhulupirira,Ndipo kuwala kwa pankhope+ panga sankakuzimitsa. 25  Ndinkawasankhira njira, ndipo ndinkakhala pansi patsogolo pawo.Ndinali ngati mfumu pakati pa asilikali ake,+Ndiponso ngati wotonthoza olira.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”
“Nduwira” ndi chovala chansalu chakumutu chimene amachimanga ngati duku.