Yobu 28:1-28

28  “Zoonadi, siliva ali ndi malo amene amapezekako,Ndiponso kuli malo a golide yemwe amayengedwa.+   Chitsulo chimatengedwa m’fumbi,+Ndipo mkuwa umakhuthulidwa kuchokera m’miyala.   Anthu aika malire a mdima,Ndipo amafufuza miyala mpaka pamapeto,+Mu mdima wandiweyani.   Amakumba mgodi kutali ndi kumene anthu amakhala monga alendo,+Kumalo oiwalika, kutali ndi phazi.Anthu ena amatsikira pansi n’kumagwira ntchito cholendewera.   Padziko lapansi pamamera chakudya,+Koma pansi pake pasandulizidwa ngati kuti pasakazidwa ndi moto.   M’miyala yake mumapezeka miyala ya safiro,+Ndipo dzikolo lili ndi fumbi la golide.   Imeneyi ndi njira imene mbalame yodya nyama+ sikuidziwa,Ndipo diso la mphamba+ silinaionepo.   Zilombo zamphamvu zakutchire sizinapondepondemo,Mkango wamphamvu sunayendeyendemo.   Anthu amatenga mwala wolimba,Amagwetsa mapiri kuyambira pansi penipeni. 10  M’miyala amakumbamo ngalande zodzaza ndi madzi,+Ndipo maso awo aona zinthu zonse zamtengo wapatali. 11  Kumalo kumene kumayambira mitsinje, amakumbako madamu.+Ndipo chinthu chobisika amachibweretsa poyera. 12  Koma kodi nzeru zingapezeke kuti?+Ndipo kumvetsa zinthu, malo ake ali kuti? 13  Munthu sadziwa mtengo wake,+Ndipo nzeru sizipezeka m’dziko la amoyo. 14  Madzi akuya anena kuti,‘Sizili mwa ine.’Nayonso nyanja yanena kuti, ‘Sizili ndi ine.’+ 15  Golide woyenga bwino sangaperekedwe mosinthana nazo,+Ndipo sangayeze siliva monga mtengo wake. 16  Sangazigule ndi golide wa ku Ofiri,+Kapena mwala wosowa wa onekisi ndi wa safiro. 17  Golide ndi galasi sizingayerekezedwe ndi nzeru,Ndipo sangazisinthanitse ndi chiwiya chilichonse cha golide woyengeka bwino. 18  Mwala wamtengo wapatali wa korali+ ndi wa kulusitalo sizingayerekezedwe n’komwe ndi nzeruzo.Ndipo thumba lodzaza ndi nzeru ndi lamtengo wapatali kuposa thumba lodzaza ndi ngale.+ 19  Sizingayerekezedwe ndi miyala ya topazi+ ya ku Kusi,Ngakhale golide woyenga bwino sangagulire nzeru. 20  Koma kodi nzeru zimachokera kuti?+Ndipo kumvetsa zinthu malo ake ali kuti? 21  Zabisika ngakhale kumaso kwa munthu aliyense wamoyo,+Ndipo n’zobisika kwa zolengedwa zouluka m’mlengalenga. 22  Chiwonongeko ndi imfa zanena kuti,‘Ndi makutu athu, tamva nkhani zokhudza nzeruzo.’ 23  Mulungu ndi amene amamvetsa njira zake,+Ndipo iye ndiye amadziwa malo ake. 24  Pakuti iye amayang’ana kumapeto kwenikweni kwa dziko lapansi.+Amaona pansi ponse pa thambo, 25  Kuti mphepo aipatse mphamvu.+Ndipo iye amagawa madzi ndi choyezera.+ 26  Pamene ankapangira mvula lamulo,+Ndiponso pamene ankapangira njira mtambo wa mvula ya mabingu, 27  M’pamene anaona nzeru n’kuyamba kulankhula zinthu zokhudza nzeruzo.Iye anazikonza n’kuzifufuza bwinobwino. 28  Ndiyeno anauza munthu kuti,‘Tamvera, kuopa Yehova ndiko nzeru,+Ndipo kupatuka pa choipa ndiko kumvetsa zinthu.’”+

Mawu a M'munsi