Yobu 27:1-23

27  Tsopano Yobu anayambanso kulankhula mwandakatulo+ kuti:   “Pali Mulungu wamoyo+ amene wandimana chilungamo,+Ndiponso pali Wamphamvuyonse wamoyo amene wachititsa moyo wanga kupweteka,+   Pamene mpweya wanga udakali wonse mwa ine,Ndiponso pamene mzimu wa Mulungu udakali m’mphuno mwanga,+   Milomo yanga sidzalankhula zopanda chilungamo,Ndipo lilime langa silidzalankhula zachinyengo.   Inetu sindingayerekeze n’komwe kunena kuti amuna inu ndinu olungama.+Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.+   Ndagwira chilungamo changa ndipo sindichitaya.+Mtima wanga sudzandinyoza masiku anga onse.+   Mdani wanga akhale munthu woipa m’zonse,+Ndipo wondiukira akhaledi wochita zoipa.   Kodi chiyembekezo cha wampatuko n’chiyani Mulungu akachotsa moyo wake,+Akamulanda moyo wake?+   Kodi Mulungu angamumvere kulira kwakeZowawa zikamugwera?+ 10  Kodi iye angasangalale ndi Wamphamvuyonse?Kodi angapemphere kwa Mulungu nthawi zonse? 11  Ndikuphunzitsani ndi thandizo la Mulungu amuna inu.Sindibisa maganizo a Wamphamvuyonse.+ 12  Nonsenutu mwaona masomphenya.Nanga n’chifukwa chiyani mukuoneka kuti ndinu opanda nzeru?+ 13  Gawo la munthu woipa lochokera kwa Mulungu,+Zomwe adzalandire kwa Wamphamvuyonse monga cholowa cha ozunza anzawo, ndi izi: 14  Ana ake akachuluka, amachulukira lupanga.+Mbadwa zake sizidzakhala ndi chakudya chokwanira. 15  Opulumuka ake adzaikidwa m’manda pa nthawi ya mliri wakupha,Ndipo akazi awo amasiye sadzalira.+ 16  Iye akaunjika siliva ngati fumbi,Ndipo akakonza zovala zake ngati dothi, 17  Ngakhale akonze zovalazo, wolungama ndi amene adzazivale.+Ndipo silivayo, wosalakwa ndi amene adzam’tenge. 18  Iye wamanga nyumba yake ngati kadziwotche,Ndiponso ngati chisimba*+ chimene mlonda wamanga. 19  Adzagona ali wolemera, koma palibe chimene chidzasonkhanitsidwe.Adzatsegula maso ake, koma sipadzakhala kalikonse.+ 20  Zoopsa zadzidzidzi zidzam’tenga ngati madzi.+Usiku chimphepo chamkuntho chidzamuba ndithu. 21  Mphepo ya kum’mawa idzamunyamula n’kumusowetsa,+Ndipo idzamuchotsa pamalo pake.+ 22  Idzamukuntha, ndipo sidzamumvera chisoni.+Adzayesera kuthawa mphamvu ya mphepoyo koma sadzatha.+ 23  Anthu adzamuwombera m’manja monyoza.+Ndipo adzamuimbira mluzu+ ali pamalo pake.

Mawu a M'munsi

Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”