Yobu 26:1-14

26  Tsopano Yobu anayankha kuti:   “Koma ndiyetu wathandiza munthu wopanda mphamvu!Ukuona ngati wapulumutsa dzanja lopanda nyonga,+   Walangiza munthu wopanda nzeru.+Komanso ukuona ngati anthu ochuluka wawadziwitsa nzeru zopindulitsa.   Kodi wauza ndani mawu ako,Ndipo zimene ukunenazi zachokera kuti?   Akufa amangokhalira kunjenjemeraPansi pa nyanja ndi pansi pa zimene zili m’nyanjamo.+   Manda ndi ovundukuka pamaso pake,+Ndipo malo a chiwonongeko n’ngosavundikira.   Iye anatambasula kumpoto pamwamba pa malo opanda kanthu,+Ndipo anakoloweka dziko lapansi m’malere.   Iye anakulunga madzi m’mitambo yake,+Moti mitamboyo sing’ambika pansi pa madziwo.   Anaphimba mpando wake wachifumu,Poukuta ndi mtambo wake.+ 10  Anaika malire ozungulira pamwamba pa madzi,+Kumene kuwala kumakathera mu mdima. 11  Zipilala za kumwamba zimagwedezeka,Ndipo zimadabwa chifukwa cha kudzudzula kwake. 12  Ndi mphamvu zake wavundula nyanja,+Ndipo ndi kuzindikira kwake wathyolathyola+ wachiwawa.*+ 13  Ndi mphepo yake wapukuta kumwamba,+Ndipo dzanja lake labaya* njoka yokwawa.+ 14  Komatu zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita zake,+Ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake.Koma kodi mabingu ake amphamvu, angawamvetse ndani?”+

Mawu a M'munsi

Mwina “wachiwawa” ameneyu ndi chilombo cha m’nyanja.
Ena amati “kulasa.”