Yobu 25:1-6

25  Tsopano Bilidadi+ wa ku Shuwa anayankha kuti:   “Ulamuliro ndi wake ndipo iye ndi wochititsa mantha.+Iye amakhazikitsa mtendere kumwamba.   Kodi asilikali ake angatheke kuwawerenga?Ndipo ndani amene kuwala kwake sikum’fika?   Choncho, kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu?+Kapena kodi munthu wobadwa kwa mkazi angakhale bwanji woyera?+   Kulitu mwezi koma si wowala.Ndipo nyenyezi si zoyera m’maso mwake.   Nanga kuli bwanji munthu yemwe ndi mphutsi,Komanso mwana wa munthu yemwe ndi nyongolotsi?”+

Mawu a M'munsi