Yobu 24:1-25

24  “N’chifukwa chiyani Wamphamvuyonse sanakhazikitse nthawi yachiweruzo,+Ndipo n’chifukwa chiyani omudziwa sanaone masiku ake achiweruzo?+   Pali anthu amene amasuntha malire,+Iwo alanda gulu la ziweto kuti aziziweta.   Amathamangitsa ngakhale bulu wamphongo wa ana amasiye,*Amalanda ng’ombe yamphongo ya mkazi wamasiye ngati chikole.+   Amapatutsa osauka panjira,+Ndipo pa nthawi yomweyo ozunzika a padziko lapansi amakhala atabisala.   Monga mbidzi+ m’chipululu,Osaukawo amapita kukafunafuna chakudya.Chipululu chimapatsa aliyense chakudya cha ana ake.   M’munda wa munthu wina, osauka amakololamo chakudya cha ziweto,Ndipo iwo amalanda msangamsanga zinthu za m’munda wa mpesa wa munthu woipa.   Osaukawo amakhala usiku wonse ali maliseche,+Amakhala pamphepo opanda chofunda.+   Amanyowa ndi mvula yamkuntho ya m’mapiri,Ndipo chifukwa chakuti alibe pobisala,+ amakupatira thanthwe.   Oipa amalanda mwana wamasiye kum’chotsa pabere.+Amatenga ngati chikole chovala chimene wozunzika wavala.+ 10  Ozunzika amayenda opanda chovala,Amasenza mitolo ya tirigu ali ndi njala.+ 11  Nthawi ya masana amakhala pakati pa migula ya m’minda.Amaponda mphesa koma amakhala ndi ludzu.+ 12  Anthu amene akufa amamveka kubuula kunja kwa mzinda,Moyo wa anthu amene akufa chifukwa chovulala umafuula popempha thandizo,+Ndipo Mulungu saziona ngati zolakwika.+ 13  Oipawo amasonyeza kuti ali pakati pa opanduka omwe amatsutsana ndi kuwala.+Iwo sanazindikire njira zake,Ndipo sanakhale m’misewu yake. 14  Kukangocha, wakupha amadzukaKupita kukapha wozunzika ndi wosauka,+Ndipo usiku iye amakhala wakuba.+ 15  Diso la wachigololo+ limadikira kuti mdima ugwe madzulo.+Iye amati, ‘Palibe diso limene lindione,’+Ndipo amaphimba kumaso kwake. 16  Mu mdima iye amathyola nyumba za anthu,Masana iwo amadzitsekera m’nyumba,Ndipo saona kuwala kwa masana.+ 17  Kwa iwo m’mawa n’chimodzimodzi ndi mdima wandiweyani,+Chifukwa zoopsa zadzidzidzi za mu mdima wandiweyani amazidziwa. 18  Woipa amatengedwa mwamsanga ndi madzi.Malo awo adzakhala otembereredwa padziko lapansi.+Sadzapatukira kunjira yopita kuminda ya mpesa. 19  Chilala ndi kutentha zimatenga madzi a chipale chofewa.Ndi mmenenso Manda amachitira ndi anthu amene achimwa.+ 20  Mimba idzamuiwala, mphutsi zidzamumva kutsekemera pomuyamwa,+Ndipo iye sadzakumbukiridwanso.+Kupanda chilungamo kudzathyoledwa ngati mtengo.+ 21  Woipa amachita zoipa ndi mkazi wouma amene sabereka,Komanso ndi mkazi wamasiye+ amene woipayo sam’chitira zabwino. 22  Ndi mphamvu zake, Mulungu adzakoka anthu anyonga.Oipa adzakhala apamwamba n’kumakayikira za moyo wawo. 23  Mulungu adzachititsa oipawo kuti azidzidalira+ n’cholinga choti azitha kudzisamalira.Maso ake adzakhala panjira zawo.+ 24  Oipawo amakhala okwezeka kwa kanthawi, kenako n’kutha.+Iwo amatsitsidwa,+ ndipo mofanana ndi wina aliyense amathotholedwa.Amadulidwa mofanana ndi nsonga ya ngala za tirigu. 25  Choncho ndani amene anganene kuti ndine wabodza?Kapena kunena kuti mawu anga ndi achabechabe?”

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”