Yobu 21:1-34

21  Tsopano Yobu anayankha kuti:   “Amuna inu, mvetserani mwatcheru mawu anga.Zimenezi zikhale zokutonthozani.   Ndilezereni mtima kuti ndilankhule.Ndikamaliza kulankhula, aliyense wa inu akhoza kuyamba kunyoza.+   Kodi ineyo ndauza munthu nkhawa zanga?Kapena n’chifukwa chiyani mzimu wanga sukukwiya?   Tembenuzirani nkhope zanu kwa ine n’kundiyang’ana modabwa,Ndipo muike dzanja lanu pakamwa.+   Ndikakumbukira, zikundisokoneza maganizo,Ndipo thupi langa lonse likumanjenjemera.   N’chifukwa chiyani oipa amakhalabe ndi moyo,+Amakalamba komanso amalemera kwambiri?+   Ana awo akhazikika nawo limodzi pamaso pawo,Ndiponso mbadwa zawo zakhazikika iwo akuona.   Nyumba zawo zili pa mtendere, zosaopa chilichonse,+Ndipo ndodo ya Mulungu sili pa iwo. 10  Ng’ombe zawo zamphongo zimapereka bere, ndipo siziwononga mphamvu zobereketsa.Ng’ombe zawo zazikazi zimabereka+ ndipo sizibereka ana akufa. 11  Iwo amalola ana awo kutuluka panja ngati nkhosa,Ndipo anawo amakhala akudumphadumpha pabwalo. 12  Iwo amafuula nthawi zonse poimba maseche ndi azeze.+Amakhala akusangalala poimba zitoliro. 13  Masiku awo onse amakhala moyo wabwino,+Ndipo posakhalitsa amatsikira ku Manda. 14  Amauza Mulungu woona kuti, ‘Chokani kwa ife!+Sitikufuna kudziwa njira zanu.+ 15  Kodi Wamphamvuyonse ndani kuti tim’tumikire?+Ndipo kulankhula naye kungatipindulitse chiyani?’+ 16  Komatu, ulemerero wawo saupeza chifukwa cha mphamvu zawo.+Malangizo a anthu oipa atalikirana nane.+ 17  Kodi nyale ya oipa imazimitsidwa kangati?+Ndipo tsoka lawo limawagwera kangati? Kodi ndi kangati pamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga?+ 18  Kodi iwo amakhala ngati udzu wouluzika ndi mphepo?+Kapena ngati mankhusu* ouluka ndi mphepo yamkuntho? 19  Zoipa zimene munthu anachita, Mulungu adzazisungira ana ake omwe,+Adzam’patsa mphoto yake, ndipo iye adzaidziwa.+ 20  Maso ake adzaona kuwola kwake,Ndipo iye adzamwa mkwiyo wa Wamphamvuyonse.+ 21  Kodi adzatha kusangalala ndi ana ake iyeyo atapita,Chiwerengero cha miyezi yake chitadulidwa pakati?+ 22  Kodi adzaphunzitsa Mulungu nzeru,+Pamene Mulunguyo azidzaweruza anthu apamwamba?+ 23  Munthu ameneyo adzafa ali wokhutira.+Adzafa ali pa mtendere ndiponso wosatekeseka. 24  Ntchafu zake zitadzaza mafuta,Ndiponso mafuta a m’mafupa mwake akadali ofewa. 25  Winanso adzafa ali wokwiya,Asanadye zinthu zabwino.+ 26  Iwo adzagona limodzi m’fumbi,+Ndipo mphutsi zidzawakuta.+ 27  Inetu ndikudziwa bwino maganizo anu amuna inu,Ndiponso zachiwawa zimene mungapangane kuti mundichitire.+ 28  Popeza mukuti, ‘Kodi nyumba ya wolemekezeka ili kuti,Ndipo hema wa oipa ali kuti? Kodi malo awo okhala ali kuti?’+ 29  Kodi simunafunse anthu oyenda m’misewu,Ndipo simuonetsetsa zizindikiro zawo, 30  Kuti pa tsiku la tsoka woipa amapulumuka,+Ndipo pa tsiku la mkwiyo amawomboledwa? 31  Ndani angamuuze za njira yake pamasom’pamaso,+Ndipo ndani adzam’patse mphoto ya zimene wachita?+ 32  Iyeyo anthu adzam’tengera kumanda,+Ndipo anthu adzachezera pamanda ake. 33  Kwa iye zibuma za dothi lochokera m’chigwa* zidzakhala zotsekemera.+Pambuyo pake adzakoka anthu onse,+Ndipo amene anapita iye asanapite n’ngosawerengeka. 34  Choncho, amuna inu mukungodzivuta poyesa kunditonthoza,+Ndipo mayankho anu ndi mabodza okhaokha.”

Mawu a M'munsi

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.