Yobu 20:1-29

20  Tsopano Zofari wa ku Naama anayankha kuti:   “N’chifukwa chake malingaliro anga osautsa akundiyankha,Chifukwa cha mkwiyo wa mumtima mwanga.   Ndikumva mawu ondinyoza,Ndipo munthu wa mtima wopanda nzeru ngati zimene ine ndili nazo, akundiyankha.   Kodi wakhala ukudziwa zimenezi kuyambira kalekale,Kuyambira pamene munthu anaikidwa padziko lapansi?+   Kuti mfuu yachisangalalo ya anthu oipa sikhalitsa,+Ndiponso kuti kusangalala kwa wampatuko kumakhala kwa kanthawi?   Ngakhale kuti ulemerero wake umafika mpaka kumwamba,+Ndipo mutu wake umafika m’mitambo?   Adzatheratu mofanana ndi ndowe zake.+Amene ankamuona adzati, ‘Ali kuti kodi?’+   Iye adzauluka ngati loto, ndipo sadzam’peza.Adzathamangitsidwa ngati masomphenya a usiku.+   Diso limene lamuona silidzam’penyanso,+Ndipo malo ake sadzamuonanso.+ 10  Ana ake adzafunafuna kuti anthu onyozeka awachitire chifundo.Manja ake adzabweza zinthu zake zamtengo wapatali.+ 11  Mafupa ake anali odzaza ndi mphamvu zake zaunyamata,Koma adzagona nazo limodzi m’fumbi.+ 12  Ngati zoipa zimatsekemera* m’kamwa mwake,Ngati amazibulumunya kuseri kwa lilime lake, 13  Ngati amazikonda ndipo sazisiya,Ngati amazivumata m’kamwa mwake, 14  Chakudya chake chidzasintha m’matumbo mwake.Chidzakhala poizoni wa mamba m’thupi mwake. 15  Wameza chuma, koma adzachisanza.Mulungu adzachithamangitsa m’mimba mwake. 16  Adzayamwa poizoni wa mamba,Lilime la mphiri lidzamupha.+ 17  Sadzaona ngalande za madzi,+Mitsinje yosefukira ndi uchi ndi mafuta a mkaka. 18  Adzabweza chuma chimene anachipeza ndipo sadzachimeza.Chumacho chidzakhala ngati chuma chochokera ku malonda ake chimene sadzachidyerera.+ 19  Pakuti watswanyatswanya onyozeka n’kuwasiya,Walanda nyumba imene sanamange,+ 20  Sadzapeza mtendere m’mimba mwake.Zinthu zake zabwinozabwino sizidzam’pulumutsa.+ 21  Palibe chimene chatsala choti ameze,N’chifukwa chake ulemerero wake sudzakhalitsa. 22  Chuma chake chitafika pachimake, adzakhala ndi nkhawa.+Tsoka lidzamugwera ndi mphamvu zonse. 23  Mulungu atumize mkwiyo wake woyaka moto pa iye,N’kuudzaza m’mimba mwake.+Auvumbitsire pa iye kuti ufike mpaka m’matumbo mwake. 24  Iye adzathawa+ zida zankhondo zachitsulo.Uta wa mkuwa udzamulasa. 25  Muvi udzatulukira kumsana kwake,Ndipo chida chonyezimira chidzaboola ndulu yake.+Zida zoopsa zidzam’pweteka.+ 26  Zinthu zake zapamtima zidzakumana ndi mdima wokhawokha.Moto wopanda woukolezera udzamunyeketsa.+Munthu wotsala muhema wake zinthu zidzamuipira. 27  Kumwamba kudzaulula cholakwa chake,+Ndipo dziko lapansi lidzamuukira. 28  Mvula yamphamvu idzakokolola nyumba yake.Zinthu zambiri zidzam’gwera pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu.+ 29  Ili ndilo gawo la munthu woipa kuchokera kwa Mulungu,+Cholowa chake chimene Mulungu wam’patsa.”

Mawu a M'munsi

Ena amati “zimanzuna.”