Yobu 19:1-29

19  Tsopano Yobu anayankha kuti:   “Kodi amuna inu musautsa moyo wanga mpaka liti,+Ndi kundilasa ndi mawu?+   Mwandidzudzula maulendo 10 onsewa.Kodi simukuchita manyazi kuti mukundizunza?+   Ngati ndachita cholakwa,+Cholakwa changacho chikhala ndi ine.   Ngati amuna inu mukudzikweza polimbana nane,+Ndipo mukuonetsa kuti chitonzo changa n’chondiyenerera,+   Dziwani kuti Mulungu mwiniwakeyo ndi amene wandisocheretsa,Ndipo wandizunguliza ndi ukonde wake wosakira nyama.+   Inetu ndakhala ndikukuwa kuti, ‘Chiwawa!’ koma palibe woyankha.+Ndakhala ndikufuula popempha thandizo, koma chilungamo sichikupezeka.+   Iye watchinga njira yanga ndi mpanda wamiyala+ mwakuti sindingathe kudutsa.Ndiponso waika mdima panjira zanga.+   Iye wandichotsera ulemerero wanga,+Wandilanda chisoti chaulemu cha kumutu kwanga. 10  Akundikokera pansi mbali zonse, ine n’kuchoka.Wazula chiyembekezo changa ngati mtengo. 11  Mkwiyo wake nawonso wandiyakira,+Ndipo akungondiona ngati ndine mdani wake. 12  Asilikali ake agwirizana n’kubwera kudzamanga njira yawo kuti alimbane nane,+Ndipo azungulira hema wanga. 13  Iye waika abale anga enieni kutali ndi ine,+Ndipo ngakhale anthu ondidziwa andisiya. 14  Anzanga apamtima anditaya.+Anthu amene ndinali kuwadziwa andiiwala, 15  Iwo amene anali kukhala m’nyumba mwanga monga alendo.+ Akapolo anga aakazi akukhala ngati sakundidziwa.Ndakhala mlendo weniweni m’maso mwawo. 16  Ndaitana wantchito wanga koma sakundiyankha.Ndikukhalira kumuchonderera ndi pakamwa panga kuti andimvere chisoni. 17  Mpweya wanga wasanduka wonyansa kwa mkazi wanga,+Ndipo ndakhala wonunkha kwa ana obadwa kwa mayi anga. 18  Nawonso anyamata ang’onoang’ono andikana.+Ndikaimirira, amayamba kunditsutsa. 19  Amuna onse amene anali anzanga apamtima akudana nane,+Ndipo amene ndinali kuwakonda anditembenukira.+ 20  Ndangotsala mafupa okhaokha,+Ndipo pang’onong’ono n’kanafa.* 21  Ndichitireni chifundo anzanganu, ndichitireni chifundo,+Chifukwa dzanja la Mulungu landikhudza.+ 22  N’chifukwa chiyani amuna inu mukungokhalira kundizunza ngati mmene akuchitira Mulungu?+Kodi simunatope ndi kundinenera zoipa? 23  Tsopano ndikulakalaka mawu anga akanalembedwa!Ndithu akanalembedwa m’buku! 24  Akanalembedwa ndi chitsulo chogobera+ n’kukhuthulirapo mtovu,Akanalembedwa pathanthwe mochita kugoba kuti akhale kwamuyaya. 25  Ineyo ndikudziwa bwino kuti wondiwombola+ ali moyo,Ndipo adzabwera pambuyo panga n’kuimirira+ pafumbi. 26  Pambuyo pa khungu langa limene alisenda, zidzakhala chonchi.Koma ndili wowonda choncho, ndidzaona Mulungu. 27  Inetu ndidzamuona.+Maso angawa, osati a mlendo winawake, adzamuonadi Mulungu.*Impso zanga zasiya kugwira ntchito mkati mwanga. 28  Pakuti amuna inu mukunena kuti, ‘N’chifukwa chiyani tikungokhalira kumuzunza?’+Chonsecho muzu wa nkhaniyo ndine. 29  Opani lupanga,+Chifukwa lupanga limaukira ochita zoipa,Kuti amuna inu mudziwe kuti kuli woweruza.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ndapulumuka ndi khungu la mano anga.”
Mawu ake enieni, “amene maso anga adzamuonadi, koma osati mlendo.”