Yobu 18:1-21

18  Tsopano Bilidadi wa ku Shuwa anayankha kuti:   “Kodi zikutengerani nthawi yaitali bwanji anthu inu kuti musiye kulankhula?Muyenera kumvetsa kuti kenako tilankhule.   N’chifukwa chiyani mukutiona ngati zinyama,+Ndiponso mukutiona ngati odetsedwa m’maso mwanu?   Iwe amene ukukhadzula moyo wako mumkwiyo wako,Kodi dziko lapansi lingasiyidwe chifukwa cha iwe?Kapena mwala ungasunthe pamalo ake chifukwa cha iwe?   Kuwala kwa oipa kudzazimitsidwa,+Ndipo moto wake sudzawala.   Kuwala kudzazima m’hema wake,+Nyale yake idzazimitsidwa mmenemo.   Adzasiya kuyenda mwamphamvu n’kuyamba kuyenda mopanikizika.Ngakhale malangizo ake adzam’gwetsa.+   Pakuti adzakodwa mu ukonde ndi mapazi ake,Ndipo adzayenda m’zingwe za ukonde.+   Msampha wam’gwira chidendene.+Khwekhwe+ lam’kola. 10  Chingwe choti chim’kole chabisidwa pansi,Ndipo msampha woti um’gwire uli panjira yake. 11  Paliponse, zoopsa zadzidzidzi zimamuchititsa mantha,+Ndipo zimamuthamangitsa zili pafupi naye kwambiri. 12  Mphamvu zake zimachepa,Ndipo tsoka+ limakhala likudikira kuti limuyendetse motsimphina. 13  Mwana woyamba wa imfa azidzanyotsola khungu la munthuyo n’kumadya.Iye adzadya ziwalo zake. 14  Zinthu zimene amazidalira zidzachotsedwa m’hema wake,+Ndipo zidzapita naye kwa mfumu ya zoopsa. 15  M’hema mwake mudzakhala chinthu chimene si chake.Sulufule+ adzawazidwa pamalo ake okhala. 16  Pansi, mizu yake idzauma.+Pamwamba, nthambi yake idzafota. 17  Dzina lake silidzatchulidwanso padziko lapansi,+Ndipo mumsewu simudzakhala dzina lake. 18  Adzamuchotsa powala n’kumukankhira kumdima.Adzamuthamangitsa panthaka ya padziko lapansi. 19  Iye sadzasiya ana kapena mbadwa pakati pa anthu ake,+Ndipo sipadzakhala wopulumuka pamalo amene iye akukhala monga mlendo. 20  Pa tsiku la tsoka lake anthu a Kumadzulo adzayang’ana modabwa,Ndipo anthu a Kum’mawa adzanjenjemera. 21  Izi n’zimene zimachitikira malo okhala munthu woipa,Ndipo awa ndiwo malo a munthu wosadziwa Mulungu.”

Mawu a M'munsi