Yobu 16:1-22

16  Tsopano Yobu anayankha kuti:   “Ndamva zinthu zambiri ngati zimenezi.Nonsenu ndinu otonthoza onditopetsa!+   Kodi mawu opanda pakewa saatha?+Kapena chikukupwetekani n’chiyani kuti muziyankha?   Inenso ndikanatha kulankhula ngati mmene mukuchitiramu,Moyo wanu ukanakhala ngati mmene ulili moyo wanga,Kodi ndikanalankhula mawu ogometsa okunenani?+Ndipo kodi ndikanakupukusirani mutu?+   Ndikanakulimbikitsani ndi mawu a m’kamwa mwanga,+Ndipo chitonthozo cha milomo yanga chikanachepetsa . . .   Ndikalankhula, ululu wanga sukuchepa.+Ndikasiya kutero, n’chiyani chikundichokera?   Koma tsopano Mulungu wanditopetsa.+Wawononga onse osonkhana nane.   Komanso inu mwandigwira. Umenewu wakhala umboni,+Mwakuti kuwonda kwanga kwandiukira ndipo kukuchitira umboni pankhope panga.   Mkwiyo wa Mulungu wandikhadzula. Iye ali nane chidani+Ndipo akundikukutira mano.+Mdani wanga akundiyang’ana ndi diso lozonda.+ 10  Iwo ayasamula kukamwa kwawo kuti andimeze.+Andimenya mbama ndi mnyozo.Asonkhana ambirimbiri kuti alimbane nane.+ 11  Mulungu wandipereka kwa anyamata,Ndipo wandiponya mwamphamvu m’manja mwa oipa.+ 12  Ine ndinali pa mtendere koma iye anandikhutchumula.+Anandigwira kumbuyo kwa khosi n’kundimenyetsa pansi,Ndipo walunjikitsa mivi yake pa ine. 13  Anthu ake oponya mivi ndi uta+ andizungulira.Iye wandiboola impso+ koma osamva chisoni,Wakhuthulira ndulu yanga pansi. 14  Iye akungokhalira kundiboola ngati mpanda.Akundithamangira ngati mmene amachitira wamphamvu.+ 15  Khungu langa ndalisokera ziguduli*+ zoti livale,Ndipo ndaika nyanga yanga m’fumbi.+ 16  Nkhope yanga yafiira chifukwa cholira,+Ndipo pazikope zanga pali mdima wandiweyani,+ 17  Chonsecho manja anga sanachite zachiwawa,Ndipo pemphero langa ndi loyera.+ 18  Iwe dziko lapansi, usaphimbe magazi anga.+Pasapezeke malo osungira kulira kwanga. 19  Komanso, wochitira umboni za ine ali kumwamba,Ndipo mboni yanga ili m’mwamba.+ 20  Anzanga asanduka ondilankhulira otsutsana nane.+Diso langa lakhala likuyang’ana kwa Mulungu osagona.+ 21  Chiweruzo chiperekedwe pakati pa mwamuna wamphamvu ndi Mulungu,Mofanana ndi pakati pa mwana wa munthu ndi mnzake.+ 22  Chifukwa pangotsala zaka zochepa,Ndipo ndidzapita ndi njira yomwe sindidzabwerera nayonso.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “masaka.”