Yobu 14:1-22

14  “Munthu wobadwa kwa mkazi,+Amakhala ndi moyo waufupi,+ wodzaza ndi masautso.+   Amaphuka ngati duwa n’kuthotholedwa.+Amathawa ngati mthunzi+ ndipo sakhalaponso.   Ameneyu mwamuyang’ana ndi diso lanu,Ndipo ine mukundizenga mlandu.+   Ndani anabadwa ali woyera kuchokera mwa munthu wodetsedwa?+Palibe ndi mmodzi yemwe.   Masiku a munthu ndi odziwika,+Ndipo chiwerengero cha miyezi yake chili ndi inu.Mwamuikira lamulo kuti asalipitirire.   Siyani kumuyang’anitsitsa kuti apumule,+Mpaka apeze chisangalalo ngati mmene amachitira waganyu pakutha pa tsiku.   Ngakhale mtengo umakhala ndi chiyembekezo.Ukadulidwa umaphukanso,+Ndipo nthambi yake idzakhalapo mpaka kalekale.   Muzu wake ukakalamba m’nthaka,Ndipo chitsa chake chikafa m’fumbi,   Ukadzangomva fungo la madzi udzaphukira,+Ndipo udzamera nthambi ngati mtengo watsopano.+ 10  Koma mwamuna wamphamvu amafa ndipo amagona pansi atagonjetsedwa.Munthu wochokera kufumbi amatha. Kodi ali kuti?+ 11  Madzi amatha m’nyanja,Ndipo madzi a mumtsinje amaphwa n’kuuma.+ 12  Anthu nawonso amagona pansi osadzuka.+Sadzadzuka mpaka kumwamba kutachoka,+Sadzadzutsidwa ku tulo tawo.+ 13  Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda,+Mukanandibisa mpaka mkwiyo wanu utachoka,Mukanati mundiikire nthawi+ n’kudzandikumbukira.+ 14  Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?+Ndidzadikira masiku onse a ntchito yanga yokakamiza,+Mpaka mpumulo wanga utafika.+ 15  Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha.+Mudzalakalaka ntchito ya manja anu. 16  Panopa mukungokhalira kuwerenga mmene mukudutsa mapazi anga,+Mukungoyang’ana machimo anga basi.+ 17  Kulakwa kwanga mwakutsekera m’thumba,+Ndipo mwamata machimo anga ndi zomatira. 18  Ngakhale phiri limagwa n’kugumukagumuka,Ngakhale thanthwe limasunthidwa pamalo ake. 19  Madzi amaperesa ngakhale miyala.Akamathamanga amakokolola dothi la padziko lapansi.Inunso mwawononga chiyembekezo cha munthu. 20  Mumamugonjetsa kwamuyaya, moti amachoka.+Mumapundula nkhope yake n’kumuthamangitsa. 21  Ana ake amalemekezedwa, koma iye sadziwa zimenezo.+Iwo amakhala opanda pake, koma iye sawaganizira. 22  Mnofu wake umawawa adakali nawo,Ndipo moyo wake umapitiriza kulira udakali mwa iye.”

Mawu a M'munsi