Yobu 13:1-28

13  “Tamverani! Zonsezi maso anga aziona,Ndipo khutu langa lamva ndi kuziganizira.   Zimene amuna inu mukuzidziwa, inenso ndikuzidziwa bwino.Si ine wotsika kwa inu.+   Komabe ndikanakonda kulankhula ndi Wamphamvuyonse,+Ndikanasangalala ndikanatsutsana ndi Mulungu.   Koma amuna inu ndinu onamizira anzanu.+Nonsenu ndinu madokotala opanda phindu.+   Zikanakhala bwino mukanangokhala chete,Pamenepo mukadakhala anthu anzeru.+   Imvani mfundo zanga zotsutsana nanu,+Ndipo tcherani khutu kuchonderera kwa milomo yanga.   Kodi amuna inu mulankhula zopanda chilungamo m’malo mwa Mulungu?Mulankhula zachinyengo m’malo mwa iye?+   Kodi mum’kondera iyeyo?+Kapena kodi mulimbana ndi Mulungu woona m’khoti?   Kodi zingakhale bwino kuti iye akufufuzeni?+Kapena mungam’pusitse ngati mmene mungapusitsire munthu? 10  Iye adzakudzudzulani ndithu,+Mukadzayesera kuchita zinthu zokondera mwakabisira.+ 11  Kodi kulemekezeka kwake sikudzakuchititsani mantha?Kodi iye sadzakuchititsani kuti muope?+ 12  Mawu anu osaiwalika ndiwo miyambi yopanda pake ngati phulusa.Mayankho anu odziteteza ali ngati zishango zadothi.+ 13  Khalani chete pamaso panga, kuti ineyo ndilankhule.Kenako chilichonse chondifikira chindifikire. 14  N’chifukwa chiyani ndikuika moyo wanga pachiswe,*Ndiponso kuika moyo wanga m’dzanja langa?+ 15  Ngati iye atandipha, kodi sindidzadikirira?+Komabe ndingatsutsane naye pamasom’pamaso za njira zanga. 16  Komanso iye adzakhala chipulumutso changa,+Chifukwa pamaso pake sipadzafika wampatuko.+ 17  Mumvetsere mawu anga mosamala,+Ndipo zolankhula zanga zikhale m’makutu mwanu. 18  Ndimvereni, ndabweretsa mlandu wofunika kuuzenga.+Ineyo ndikudziwa bwino kuti sindinalakwe. 19  Ndani amene angatsutsane nane?+Ngati ndingakhale chete osalankhula, ndikhoza kungofa. 20  Pali zinthu ziwiri zokha zoti musandichitire.Mukatero sindidzabisala pamaso panu.+ 21  Ikani dzanja lanu kutali ndi ine,Ndipo kuopsa kwanu kusandichititse mantha.+ 22  Muitane kuti ine ndivomere.Kapena ndilankhule ndipo inu mundiyankhe. 23  Kodi ine ndinalakwa ndiponso kuchimwa mwa njira yanji?Ndidziwitseni kulakwa kwanga ndiponso tchimo langa. 24  N’chifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu,+N’kunditenga ine ngati mdani wanu?+ 25  Kodi mukuopseza ine tsamba lachabechabe louluzika ndi mphepo?Kapena mukuthamangitsa ine udzu wouma wachabechabe? 26  Pakuti inu mukupitiriza kundilembera zinthu zowawa,+Ndipo mukundipatsa zotsatira za zolakwa zimene ndinachita ndili mnyamata.+ 27  Ndiponso simukuchotsa mapazi anga m’matangadza,+Ndipo mumayang’anitsitsa njira zanga zonse.Mapazi anga mumawalembera malire. 28  Ine* ndili ngati chinthu chowola chimene chimatha.+Ngati chovala chimene njenjete* zimadya.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “kunyamula mnofu wanga ndi mano.”
Kapena kuti “munthu uyu.” M’Chiheberi, “iye” kutanthauza “Yobu.”
Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.